Mutu 16
1
Pamene siku ya Sabata inatha, Maliya Magadalene ndi Maliya amake a Yakobo, ndi Salome anagula mafuta yonukira kuti akazoze thupi ya Yesu.
2
M'mamawa pa siku yoyamba ya wiki, anayenda ku manda pamene zuwa linatuluka.
3
Analikulankhula kuwina ndimzace, "Ndani azaticoselapo cimwala pa khomo ya manda?"
4
Pamene anayangana kumwamba, anaona kuti cimwala palibe pa khomo ya manda, cifukwa cinali cikulu kwambiri.
5
Anangena mkati mwa manda ndipo anaona mnyamata wovala zoyela, analinkhale kuzanja lamanja, ndipo anadabwa.
6
Iye anati kwa iwo, "Musacite mantha. Mulikufuna Yesu, waku nazareti, wamene anapacikidwa. Anauka! mulibe muno. Onanipamene anamuika iye.
7
Manje pitani, mukauze wophunzira ake ndi Petulo kuti alikuyenda patsogolo panu ku Galileya. Kunja mzamuona iye, Nganimwane anakuuzilani."
8
Anayenda ndikuthamanga kucokela ku manda; Anacitha mantha ndi kuthuthuma. Sanakhambe ciliconse kuli aliyense cifukwa anali ndi mantha.
9
Pasiku yoyamba ya wiki, athaukha, anaonekela coyamba kwa kwa Maliya Magadelena, uja wamene anacosamo viwanda seveni.
10
Anayenda ndikukhauza iwo amene anali naye, pamene anali kulira ndi kucita maliro.
11
Anamva kuti ali moyo, ndipo waonekela kwa iye, koma sanakhuluphirire.
12
Ndipo patapita izi, anaonekela mosiyana kuli awiri a iwo, pamene anali kuyenda kudziko ina.
13
Anayenda ndi kukauza wophunzira aja ena, koma sanakhuluphirire iwo.
14
Yesu pambuyo pake anaonekela kwa aja Eleveni pamene anali kuyandikira ku gome, ndipo anawazuzula iwo cifukwa cosakuluphirira ndi kuuma mitima yawo, cifukwa sanakhuluphirire aja amene anamuona ataukha.
15
Anati kwa iwo, "Yendani kudziko lonse la pansi, ndikulalikira uthenga ku zolengedwa zonse.
16
Iye amene azakhuluphirira ndi kubatizidwa azaphulumusidwa ndi iye amene sazakhuluphirira azakanidwa.
17
Ndipo zizindikiro izi zizawasatha iwo amene akhuluphirira: Mzina langaazacosa ziwanda. Azalankhula m'malirime yatsopano.
18
Azathola njoka ndi manja awo ndipo sizawaluma, ndipo pamene azamwa zinthu zowapaya nazo, sazafa. Azasanjika manja awo pa wodwala ndipo wodwala azapola."
19
Pambuyo polankhula izi Ambuye kuli iwo, anathengedwa kupita kumwamba ndikukakhala kuzanja lamanja ya Mulungu.
20
Wophunzila anacoka ndikuyamba kulalikira kuli konse, ndipo Ambuye anawasewenzesa kuvomelezela mau ake ndi zizindikiro zinali nawo.