Mutu 14
1
Kunasala cabe masiku yawiri ikalibe kukumana madyelelo ya Pasika ya Buledi ilibe cotupisa. Mkulu wa ansembe ndi alembi anali kuonapo mwamene angamugwirile Yesu ndikumpaya iye.
2
Cifukwa anati, "Kosati panthawi ya bwando, kuti pasankhale Ciwawa pakati ka anthu."
3
Pamene Yesu anali ku Betaniya mnyumba ya Simoni wa makathe, pamene anayandikila ku gome, mzimai wina anabwela ndi botolo ya mafuta yonukila, yodula kwambiri, ya nadi yosayanjana ndi mafuta yena. anapwanya botolo ndi kuthenga mafuta ndikumuzola kumutu.
4
Koma ena anakalipa. Anayamba kulankhula kuli wina ndi mzace nati, "Kodi maganizo aya yo ononga bwanji?
5
Aya mafuta yonunkhila kwenze bwino kuti agulise pandalama zopitilila fili hundiredi dinali, ndi kupasa wosauka." Ndipo anayamba kumukalipila iye.
6
Koma Yesu anati, "Musiyeni mzimai uyu. Cifukwa nicani mufuna kumuvuta uyu? Acita cinthu cabwino kwambimbiri kwa ine.
7
Nthawi zonse muzankhala nawo wosauka, ndipo nthawi iliyonse yamene mufuna kuwacitila cabwino muzawacitila, koma simuzakhala naine nthawi zonse.
8
Mzimai uyu wacita camene wakwanisha kucita: Wazoza thupi yanga kukonzeka kuikiwa m'manda.
9
Zoonadi ndilankhula ndi inu, kulikonse kwamene uthenga wabwino ulalikilidwa kudziko lonse lapansi , camene wacita mzimai uyu, cizalankhulidwa, mokumbukila iye."
10
Ndipo Yudasi Isikaliyoti, umodzi aja twelufu, anacokapo ndikuyenda kwa mkulu wa ansembe kuti ampeleke iye kwa iwo.
11
Pamene mkulu wa ansembe anamva izi, anakondwela kwambiri ndikulonjeza kumpasa ndalama. Anayamba kusakila njila yompelekela kwa iwo.
12
Siku yoyamba ya buledi yopanda cotupisa, pamene anapeleka nkhosa nsembe ya pasaka, wophunzila ake anti kwa iye, "Mufuna kuti tiyende kuti tikhakonze, kuti tidye cakudya ca pasaka?"
13
Anatuma awiri wa wophunzira ake ndikunena nawo kuti, "Pitani kumzinda, mzakumana ndi munthu wonyamula mgomo wa manzi. M'mukonkhe iye.
14
Pamene azangena mnyumba, nainunso mngene ndipo muti kwa mwine nyumba kuti, 'Mphunzisi anti, "kodi cipinda canga ca alendo niciti kuti tidyelemo pasaka ndi wophunzira anga?"
15
Iye azakuonesani cipinda cikulu, capamwamba cokonzelatu bwino. Mutikonzekele ife tonse kwamene uko."
16
Wophunzila aja ananyamuka ndikyenda kumzinda. Anapeza zonse nga nimwamene analakambira kwa iwo, ndipo anakonza cakudya ca pasaka.
17
Pamene kunafika m'mazulo, anabwela pamonzi ndi aja twelufu.
18
pamene anali kuyandikira pa gome yodyelapo, Yesu anati, "Zoonadi ndikuuzani inu, umodzi wa inu azandipeleka kwa dani."
19
Wonse anacita cisoni, ndipo anati kwa wina ndi mzace anati kwa iye, "mwacoonadi sindine?"
20
Yesu anayankha ndipo anti kwa iwo, "ndi umodzi wa twelufu, wamene ndizatowela naye buledi pamodzi ndi ine mbale.
21
Cifukwa Mwana wa Munthu azayenda ngani mwamene malembo anenela za iye. Koma soka kwa uyo munthu wamene azapeleka Mwana wa Munthu! kunali kwabino kwa iye ngati sanabadwe."
22
Pamene anali kudya, Yesu anatenga buledi, anaidalisa, ndikusuna. Anawapasa iwo nati, "Thengani iyi. Iyi ndiye thupi yanga,"
23
Anathengaso kapu, ndikuyamika, ndikwapasa iwo, ndipo wonse anamwamo.
24
Anati kwa iwo, "Aya ndi magazi yanga yacipangano, magazi yamene yazacoka ya anthu ambiri.
25
Zoonadi ndinena ndi inu, Sindizamwanso kucokela kucipatso ici ca mpesa kufikila ija siku pamene ndizamwa catsopano mufumu wa Mulungu."
26
Pamene anayimba nyimbo, anayenda kuluphiri ya Olive.
27
Yesu anati kwa iwo, "wonse inu mzagwa, cifukwa kunalembedwa, 'ndizamenya mbusa ndipo nkhosa zizamwazika.'
28
Koma pamene ndizaukisidwa kwa kufa, Ndizakayenda patsogolo panu ku Galileya."
29
Petulo anati kwa iye, "Ngakale kuti wonse azagwa , Ine sindizacita izo."
30
Yesu anati kwa iye, "Zoonadi ndinena ndi iwe, usiku wa lero, akalibe kulira kombwe kawiri, uzanikana katatu.
31
"Koma Petulo anati, "Ngati nikufa ndizafa ndi inu, Sindizakukanani inu." Wonse analonjeza cimodzi-modzi.
32
Ndipo anabwela kumalo wocedwa Gesemani, ndipo Yesu anati kwa wophunzila ake, " Nkhalani pano pamene ndiyenda kukapemphela."
33
Anathenga Petulo, Yakobo ndi Yohane ndi iye ndikuyamba kuvutika n'mtima ndimavuto.
34
Iye anati kwa iwo, "Moyo wanga ndiwovutika kwambiri, kufikira pamuyeso wa imfa. Nkhalani pano ndikuona."
35
Yesu anayendako patsogolo pan'gono, ndikugwa pansi, ndikuyamba kupemphela kuti cinali coteka, iyi nthawi ipitirire pali iye.
36
Iye anati, " Abba, Atate, zinthu zonse ndizotheka ndi inu. Cosani kapu iye pali ine. Koma osati mwacifuniro canga koma canu."
37
Anabwelela ndipo anapeza iwo kuti aligone, ndipo anati kwa Petulo, "Simoni, kodi ulikugona? Kodi sungayembekezeko cabe kwa ola imodzi?
38
Wona ndikupemphela kuti usangene mumayeselo. Mzimu ulikufuna koma thupi ya lema."
39
Anayendatso patsogolo kukapemphela, ndipo anabwezelapo mau amodzi- amodzi.
40
Anabwelatso ndipo anawapeza alimtulo, cifukwa menso yawo analema kwambiri kuti analimbe zoomuuza iye.
41
Anabwelatso kacitatu ndipo anati kwa iwo, "Kodi mukaligone ndikupumula? Kwakwana! Nthawi yafika. Wonani! Mwana wa Munthu alikupelekedwa mumanja ya wocimwa.
42
Ukani; tiyeni. Wonani, amene alikunimpeleka ali pafupi."
43
Akali kukamba, Yudasi umodzi wa aja twelufu, anafika, ndipo anthu ambiri anali ndi iye ndi malupanga ndi mikondo, ndi mkulu wa ansembe, ndi alembi, ndi akulu.
44
Manje uja wompeleka anawauza cizindikiro, Kuti, " wamene ndizakising'a, niwamene. M'mukate ndikumsogozela kukamvalila."
45
Pamene Yudasi anafika, panthawi yamene iyo anabwela kwa Yesu ndipo anati, "Rabbi! ndikumkising'a.
46
Ndipo anamgwira iye ndikuyenda naye.
47
Koma umodzi wa iwo amene anaimirira anathenga cipanga ndi kujuwa kwatu kwa kapolo wa mkulu wa ansembe.
48
Yesu anati kwa iwo, "kodi mwabwela na vipanga ndi mikondo kwati mwabwela ku gwira kawalala?
49
Pamene ndinali namwe masiku wonse ndipo ndinali kuphunzisa mtempele simunanigwile ine. Koma izi kuti malembo akwanilisike."
50
Ndipo aja wonse amene anali ndi Yesu anamsiya ndi kuthawa.
51
Mnyamata, wovala zovala za kaniki nayenso anamsatira Yesu. Pamene azibambo anamgwira Yesu,
52
anasiya covala zake ndikutawa malisece.
53
Anamsogolela Yesu kwa mkulu wansembe. Kwamene kuja anasonkhana naye akulu ansembe, akulu ndi alembi.
54
Manje Petulo analikumsata iye patali, patali ngati nyumba ya mkulu wansembe. Anankhala pakati pa asilikali, amene anali kuota moto.
55
Manje mkulu wa ansembe ndi bungwe yonse ya Ayuda anali kufuna-funa umboni womususa Yesu kuti ampaye. Koma sanaupeze .
56
Cifukwa ambiri anabwela ndi umboni waboza kumunamizila iye, koma cukanga umboni wawo sunagwirizane.
57
Ena anabwelesa umboni waboza kumunenela; iwo anati,
58
"Tinamvela uyu munthu akunena kuti, 'Ndingagwese tempele iyi ndimanja yanga, ndipo m'masiku yatatu ndingamange ina yosamangika ndi manja."
59
Cukanga uyu umboni sunagwilizane.
60
Akulu ansembe anaimirira ndikumfunsa Yesu, "Kodi suuyankha? Kodi nizabwanji izi zamene akuneneza iwe?"
61
Koma anali cete sanayankhe ciliconse. Akulu ansembe anafunsatso nati, "Kodi ndiwe Kristu, mwana wodalisika?"
62
Yesu anati, "Ndine. ndipo mzakaona Mwana wa Munthu pamene azankhala kuzanja lamanja la mpamvu ndipo alikubwela m'makumbi kucokela kumwamba."
63
Mkulu wansembe anang'amba covala cake ndikunena, " Tikali kufuna umboni wina?
64
Mwazimvelela noka manyozo. kodi mugamula bwanji?" Wonse anamususa nati ayenela kufa.
65
Ena anayamba kumtira mata ndikumvala pamenso ndikumenya iye nati kwa iye, "Nenela!" Asilikali anamtenga ndi kumumenya kwambiri.
66
Pamene Petulo anali pansi kunyumba ya wansembe, umodzi wanchito mkazi wa Mkulu wansembe anaza kwa iye,
67
Anamuona Petulo pamene anaimirira ku moto alikuota, ndipo anamuyangana kwambiri iye. Ndipo anati, "Iwenso unali ndi mnazarene, Yesu."
68
Koma iye anakana, nati, " Sindimuziwa kapena kumvela zamene ulikulankhula iwe." Ndipo anacoka mnyumba ija ya wansembe.
69
Koma uja mwannchitho mkazi anamuona iye ndipo anayamba kulankhulanso ndiaja amene anaimirira paja, " Uyu Munthu ndi umodzi wa iwo!"
70
Koma iye anakananso. Patapita kanthawi pang'ono aja amene anaimirira naye analikulankhula kwa Petulo nati, " Zoonadi iwe ndiwe umodzi wa iwo, cifukwa naiwenso ndiwe mgalileya."
71
Koma iye anayamba kuzitembelela ndi kulapa, " Ine uyu munthu sindimuziwa amene muli kulankhulapo."
72
Kombwe analira panthawi yamene iyo kwaciwiri. Ndipo Petulo anakumbuka mau amene Yesu anakambakwa iye, " Kombwe akalibe kulira kawili, iwe uzanikana katatu." Ndipo mtima wake unasweka ndipo analira.