Mutu 13
1
Manje pamene Yesu anali kucoka kufuma m'tempele, umodzi wa wophunzila ake anati kwa iye, "Mphunzisi, wonani mwala uyu wabwino na mamangidwe abwino!"
2
Iye anati ka iye, " Mulikuona mamangidwe akulu aya? Palibe mwala uliwonse wamene uzasala pamwamba pa uyake wamene uti ukakane kucosewapo."
3
Pamene anankhala paluphiri lwa Oliva kumpali kwina kwa tempele, Petulo, Yakobo, Yohane ndi Anduleya anamfunsa cakuseli,
4
"Tiuzyeni kodi izi zizacitika liti? Kodi cizindikiro nicani kuti izi zilikufupi kuti zicitike?"
5
Yesu anamba anawauza iwo, "Nkhalani celu kuti wina asakusoceleseni.
6
Ambiri azabwela mzina langa ndikuti, 'Ndine wamene, 'ndipo azasocelesa ambiri.
7
Pamene mzamvela za nkhondo ndi nkhani za nkhondo, msakavutike mtima, izi zifunika kuti zicitike, koma kusila kwa dziko kukalimbe kucitika.
8
Cifukwa dziko lizaukirana ndi dziko. ndiufumu uzaukirana ndi ufumu. Kuzankhala civomezi ca dziko madela ambiri, ndi njala. Ici nicayambi cabe ca cipota.
9
Nkalani na celu. Azakupelekani inu kwa akulu ansaka, ndipo muzakamenyedwa mumasunagogi. Mzakaimilila kwa akulu a boma ndi mafumu cifukwa ca ine, ngati umboni kwawo.
10
Koma uthenga wabwino ufunika kuti ulalikiridwe ku madziko wonse.
11
Pamene azakakugwirani ndikukupelekhani, msakhacite nkhawa kuti tizakakamba ciani. Cifukwa panthawi ija, zamene mzakakamba zizakapasidwa kwa inu; simzakakhala inu wolankhula , koma Mzimu Woyela.
12
Mbale azakapeleka mbale mzake kuti apedwe, ndi atate azakapeleka mwana wawo. Ndi ana azaukira makolo awo ndkufuna kuti apedwe.
13
Azakuzondani anthu ambiri cifukwa ca zina langa. koma amene azalimbikira kufikira kucimalizilo, uja munthu azaphulumusidwa.
14
Pamene mzakaona zamalodza zosaloledwa zilikuimilila pamene sizifunika kuimilirira (inu amene mziwa kuwelenga mvesesani), inu muli ku Yudeya tamangani ku maluphiri,
15
uyo ali pamwamba pamtenge wa nyumba asaseluke kungena mkati mwanyumba kapena kuti akatenge cili conse kucosa mnyumba,
16
uyo ali m'munda asabwelele kuti athenge covala cake.
17
Koma soka kuli aja amene ali ndi ana ndi iwo amene oyamwisha ana m'masiku aja!
18
Pemphelani kuti osati vikacitike mtnawi ya mphepo.
19
Cifikwa kuzakhala zowawisa zikulu, kuti zikalibe kucitikapo kuyambila koyamba, pamene Mulungu analenga dziko lapansi, kufikira manje, yayi, sikuzankhalanso.
20
Kapena Ambuye akacepeseko masiku, kulibe aliyense amene azaphulumusidwa. Koma cifukwa ca awo wolungama, amene iwo anasankha, azacosako masiku.
21
Ndipo ngati wina azati kwa inu, 'Onani uyu niye Kristu!' kapena Onani, kuja kwamene alili! Msakhulupirire.
22
Cifukwa a Kristu aboza ndi aneneli aboza, azaonekela ndikuonesa zizindikiro ndi zodabwisa, kui asocelese, ngati nkoteka cukanga wolungama.
23
Nkhalani celu! Ndakuuzani zonse izi nthawi ikhaliko.
24
Koma yakasila masautso pamasiku yaja, zuwa lizasandulika mdima, mwezi suzapelekanso kuwala,
25
nyenyezi zizagwa kucokela kumwamba, ndi mpamvu zamene zili kumwamba zizasung'uzika.
26
Ndipo mzaona Mwana wa Munthu alikubwela m'makumbi ndi mpamvu zikulu ndi ulemelelo.
27
Ndipo azatuma angelo ake azasonkhanisa wonse wolungama kucokela kumpali zonse zinai, kucokela kusilililo kwa dziko ndikusilililo kwa thambo.
28
Mphunzilani ciphunzitso ca mtengo wa mukuyu. pamene muona misambo iyamba kupukira ndikuyoyosha matepo, mziwa kuti nthawi ya kupya kuli pafupi.
29
Cimodzi-modzi pamene muona izi zilikucitika, ziwani kuti ali pafupi, pafupi ndi pageti.
30
Zoonadi ndikuuzani, uyu mbadwo suzapita pamene izi zizacitika.
31
Kumwamba ndi dziko lapansi zizapita, koma mau anga sazapita.
32
Koma kulingana za siku kapena nthawi, palibe amene azaiwa, cukanga angelo kumwamba, kapena Mwana koma Atate.
33
Nkhalani acelu! Yanganani ndi kupemphela cifukwa simuziwa nthawi yamene iyo.
34
Cilingana ndi munthu amane anayenda paulendo- anasiya nyumba yake ndikuikamo anchito kuti akale woyiyanganila, aliyense ndi nchito yake ndipo analemba na woyangana kuti ankhale m'maso.
35
Cifukwa cake nkhalani ndi celu, cifukwa simuziwa pamene mwine nyumba azabwela; kungankale m'mazulo, kapena pakati kausiku, kapena pamene kombwe alikulila m'mamawa.
36
Ngati azabwela movundumukiza, asakakupezani muli mtulo.
37
Camene nili kunena ine kwa inu ndilikunena kwali aliyense: Nkhalani maso!"