Mutu 12
1
Ndipo Yesu anayamba kuphunzitsa mumafanizo. Iye anati, "Mdala wina anabyala munda wake wa mpesa, ndipo anaika linga kuzengulusa munda wonse, ndikukumba kuwelengela mpesa. Anamanga nsanja ya olonda ndikuukongoletsa munda kuli aja wolima mpesa. Ndipo anayenda pa ulendo.
2
Panthawi yake, anatuma wanchito kuwolima munda kuti akampaseko zipatso zina zamunda.
3
Koma anamtenga iye , ndikumumenya ndi kumbweza kulibe ciliconse.
4
Anatumanso wanchito wina, ndipo anamucita vilonda kumutu ndikumvesa nsoni.
5
Anatumatso wina, ndipo uyu anamupaya. ndipo ambiri anawacita cimodzi- modzi, kuwamenya ena ndi kupaya ena.
6
Panasala cabe umodzi munthu wotuma, amene anali mwana wake wokondedwa. Anali wosiliza wamene anamtuma kwa iwo. Iye anati, "Iye azampasa ulemu."
7
Koma aja olima m'munda anati kwa wina ndi mzace, "Uyu ndiye ndiye wopyana wake. Tiyeni, timpaye, ndipo ife tizakhala wopyana."
8
Anamugwira ndi kumpaya ndipo anamponyela kuseli kwa munda.
9
Manje, ula mwine wa munda, azawacita? Azabwela ndi kuzawaononga aja wolima munda ndi kupasa munda kuli ena.
10
Kodi musanawerenge m'malembo? 'Uja mwala wamene womanga anaukhana, wakhala wapangondya.
11
Ici cinacokela kwa Ambuye, ndipo ndicodabwisa ku menso kwathu.
12
Anafuna kumgwira Yesu, koma anacita mantha ndi kuculuka kwa anthu, cifukwa anaziwa kuti analanhkula fanizo iyi kuwasusa iwo. Telo anamusiya ndi kucokapo.
13
Ndipo anatumako Afalisi ndi Ahelodiya kuli iye kuti ampeze na mlandu m'makambidwe.
14
Pamene anabwela, anati kwa iye, "Mphunzisi, tiziwa kuti inu m'makamba kosayopa munthu, ndipo sim'makamba kuti mvese bwino munthu. M'maphunzisa coonzdi conse ca Mulungu. Kodi nicovomelekezeka kano yai mwalamulo kulipira msonkho?"
15
Koma Yesu anaziwa malingililo yawo ya cinyengo ndipo anati kwa iwo, "Cifukwa niciyani m'funa kundiyesa? Letani kwa ine ndalama niyiwone."
16
Anabwelesa imozi kwa Yesu. Anati kwa iye, "Kodi pali mutu ndi malemba andani?" Iwo nati, "Kaisayi"
17
Yesu anati, Pelekani kwa Kaisayi zinthu za Kaisayi ndi kwa Mulungu zinthu za Mulungu." Anadabwa ndi iye.
18
Ndipo Asaduki, amene anti kulibe kuukha kwa kufa, anabwela kwa iye. Anamufunsa iye, nati,
19
"Mphunzisi, Mose analemba kwa ise, 'Ngati mkazi wa mbale wako afa ndikusiya mkazi wake kumbuyo, koma sanasyemo ana, mwamuna afunika akwatire mkazi wa mbale, ndikunkhala naye ana a mbale ake.'
20
Kunali abale ake seveni; woyamba anakwatira ndikufa, sanasiyemo ana.
21
Waciwili anamkwatira iye ndipo anafa kosasiyamo ana. Ndiwacitatu cimodzi-modzi.
22
Ndiwa seveni sanasiyemo ana. Posiliza pake, uja mwamkazi anamwaliratso.
23
Paciukitso, pamene azakaukatso, uja mwanakazi azankhala wandani? Cifukwa wonse aja seveni anamkwatirapo."
24
Yesu anati, "Ici sindiye cifukwa cake mulakwisa, Cifukwa simuziwa malembo kapena mpamvu ya Mulungu?
25
Pamene azauka kwa kufa, Sikuzakhala kukwatira kapena kukwatiliwa, koma azankhala ngati Angelo a kumwamba.
26
Koma nkhani ya akufa kuti azaukha, kodi simunawelenge mbuku ya Mose, pankhani ya cisamba, mwamene Mulungu analankhulila kwa iye ndipo anati, 'Ndine Mulungu wa Abrahamu ndi Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo'?
27
Si Mulungu wa akufa, koma wa amoyo. Mulikusokoneza."
28
Umodzi wa alembi anaza ndi kumva zokambilana zawo; anamva kuti Yesu ali kwayankha bwino. Anamfunsa iye, "Kodi lamulo yofunika kwambiri pa wonse ni iti?"
29
Yesu anayankha, "Lamulo yofunika kwambiri ni iyi, 'Mvera Isilayeli, Ambuye Mulungu wathu, Ambuye ndi umodzi.
30
Ufunika kumkonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako, ndi malingaliro yako yonse, ndi mpamvu zako zonse.'
31
Ndipo lamulo yaciwiri ndiyo iyi, ' Uzikonda mnansi mwamene uzikondela weka.' Palibe lamulo loposa aya."
32
Ndipo alembi anati, "Mphunzisi, wabwino! mwakamba zoona kuti Mulungu ndi umodzi, ndipo kulibe wina koposa iye.
33
Kumkonda iye ndi mtima wonse, ndikumvesa konse, ndi mpamvu zonse, ndi kukonda mnansi wako mwamene uzikondela iwe weka, ici ciposa nsembe yoshoka kano sembe yopeleka."
34
Pamene Yesu anaona kuti wayankha mwa nzelu, iye anati, "Iwe sulikuthali na ufumu wa Mulungu." Patapita izi,
palibe wina anamfunsa Yesu mafunso ena.
35
Ndipo Yesu anayankha, pamene anali kuphunzisa mutempele; iye anati, "nanga bwanji alembi anena kuti Kristu ndi mwana wa Davide?
36
Davide mwine yeka posogozedwa ndi Mzimu Woyela, anati, 'Ambuye anati kwa Ambuye anga, nkhala ku zanja langa ya manja, kufikira pamene ndizapanga adani ako kunkhala pansi pa mendo ako.'
37
Davide iye anamuitana iye, 'Ambuye" nanga ziteka bwanji kuti Kristu kukhala mwana wa Davide?" Anthu ambiri anamvela iye mwacikondwelelo.
38
Paciphunzitso cake Yesu anati, "Cenjelani ndi alembi, amene amakonda kuyenda mnjira pamene avala minjira itali ndipo amakonda kupasa moni pamsika
39
ndipo amakonda kunkhala m'malo wolemekezeka mu masunagoge m'mapwando amakonda kunkhala malo ya cifumu.
40
Ndipo amavutisha manyumba ya azimai wofedwa, ndipo amapemphela pemphelo itali kuti anthu awaone. Awa anthu azalandila cilango cikulu."
41
Ndipo Yesu anakhala pansi pafupi ndi thumba yopelekelamo zambale; analikuona anthu ali kupeleka ndalama mthumba. Anthu ambiri wolemela analikupeleka ndalama zambiri.
42
Koma wosauka wamasiye anabwela ndi tungwinjiri tuwili, tolingana na peni.
43
Ndipo anaitana wophunzira ake nati kwa iwo, "Zoonadi ndikuuzani, uyu mzimai wamasiye wapeleka zambiri kupambana awa wonse apeleka mthumba iyi.
44
Cifukwa wonse apeleka kulingana ndikuculuka kwa cuma cawo. Koma uyu wamasiye , kucokela mkusauka kwake, apeleka zonse zamene anali nazo."