Chapta 4
1
Mau a Samweli anabwela kuli Israeli yonse . Apa Israeli anayenda kuuja kunkhondo kukamenyana ma Philistini. Anamana misasa Elbeneza , koma ma Philistini anamanga wisasa pa Apheki.
2
A Philistini anatanthama mumunzele kumenyana na Israeli anamenyedwa na ma Philistini , wamene wanapaya amuna kuwelengela pa fupi kukwana folo sauzande pamalo pamene wanamenyalama.
3
Pamene wanthu wanabelela pamusasa, wakulu wa Israeli wanati , ''Nchifukwa chani Yehova atigonjesa lelo pamenso pama Philistini ? '' Lekeni tilete chombo chachipangano cha Yehova kuno kuchokela ku Shilo , pakuti chizankhala kuno na ife , kuti chingatisunge m'chitelezo kuti chosa mumanja yawadari wathu.''
4
Apo wanthu ana tumako wamuna ku Shilo kuchokela uko wananyamula bokosi yachipangano ya ambuye Yehova wamene amankhala pamwamba pa ma cherubimu. Anyamata wabili wa Eli , Hophini na Phineyas , wanali kwamene na bokosi yachipangano ya Mulungu.
5
Pamene bokosi yachipangano cha Yehova inafika pamusasa , wonse wanthu waku Israeli anakuwa maningi , nanthaka inavomekeza kukuwa kwao.
6
Pamene ma Philistini anamvela chongo kamba kakukuwa , wanakamba kuti , '' Uku kukuwa mokweza mumisasa ya a Heberi kutanthauzanji ? '' Pamene apo anaziwa kuti bokosi yachipangano ya Yehova inali ya fika mu misasa.
7
A philistini anachita mautha; nakukamba kuti , '' Mwangena kamulungu mumusasa . '' Wanakamba kuti , '' Soka kwa ise ! kukalibe kuchitikapo va so kumbuyo konse uku !
8
Soka kwa ise ! Ndani azatichingilila kuli iyi milunguyamphamvu? Aya nimilungu yamene yanayamba kumenya aku Egypito na vilango vambili vosiyanasiyana musanga .
9
Limbikani, ndipo munkhale wamuna weniweni , ndipo mumenyane.''
10
Ma Philistini wanamenya ,nkhondo , ndipo Israeli anagonjesewa. Munthu aliyose anathawila kunyumba kwake , ndipo wopayiwa wanali wambili maningi ; ndaba sate sauzande masoja woyenda pansi wakugulu ya Israeli wanafa.
11
Bokosi yachipangano ya Yehova inapokewa , na bana bawili wamuna wa Eli , Hofini na Phiniyasi wanafa.
12
Mwamuna wakutundu wa Benjamini anathawa kuchokela pamuzele wankhondo nakubwela ku Shilo yamene iyi siku , anafika navovala vake vong'ambika na lukungu mumutu mwake.
13
Pamene anafika , Eli anali nkhala pa mpando wake mbali mwa musewu kuyanganila chifukwa mutima wake unanjenjemela nankhawa pa bokosi yachipangano cha Mulungu. Pamene uyu mwamuna ana lowa mu tawuni naku peleka uthenga , tawuni yonse inalila mokuwa.
14
Pamene Eli anamvela chongo cha kulila kwamphamvu anati , '' Tanthauzo yake ya uku kupunda kwa pamwamba maningi nichani?'' Munthu uja anabwela mofulumila nakumuwuza Eli.
15
Apo Eli anali na Zaka nayinte - eyiti musinkhu wake ; Menso yake siyanali kuyang'ana moukhazikika ndipo sienzekuwona.
16
Munthu uja anati kwa Eli , ''Ndine mwamuna wamene wabwela kuchokela kumuzele wankhondo . Nathawa kuchoka kunkhondo lelo. ''Eli anati , zayenda bwanji, mwana wanga?''
17
Mwamuna analeta nkhani yachilendo anayankha na kunena kuti , '' Israeli anathawa ma Philistini , Ndipo pankhala kumenyewa kukulu maningi pawanthu wathu. Nafuti , wana banu babili wamuna Hofini na Phineyasi , wafa , ndipo chombo chachipangano cha Mulungu chapokewa.''
18
Pamene anatomola chombo cha Mulungu Eli anagwa chagada kuchoka pampando wake pambali pa geti . Mkosi wake unatyoka , ndipo anafa , chifukwa anali wokalamba na kulema . Anaweluza Israeli kwa zaka fote.
19
Ano mpongozi wake , mkazi wa Phineyasi , anali na mimba na kusala pang'ono kubala . Pamene anamvela nkhani yachilendo kuti bokosi yachipangano ya Mulungu inagwiriwa nakuti apongozi wake ndiponso wamuna wake wanafa , anagwada nakubala , koma ululu wapo bala unamukulila.
20
Atasala pang'ono kufa azimayi wamene wanali kumuthandiza wanakamba kuti kuli yeve , ''Osayopa ndaba wabala mwana mwamuna .'' Koma sanayankhe kapena kuikako mutima kuli vamene wanakamba.
21
Anamuteya mwana zina yake Ikabodi, kukamba kuti , ''Ulemelelo wachokamo mu Israeli '' pakuti chombo cha Mulungu chinatengewa mwachikakamizo, ndiponso chifukwa cha bapongozi wake na mwamuna wake.
22
Iye anati , '' Ulemelelo wa Mulungu wachokamo mu Israeli , chifukwa bokosi yachipangano ya Mulungu yapokewa mwa chikakamizo.''