Chapta 28
1
Chinabwela kuchitika masiku amene ayo kuti A Philisiti anasonkhana masoja wawo pamozi kuti achite nkhondo kumenyana na Israeli. Achishi anati kuli Davide , ''Uchiziwe ichi mopanda chikayiko kuti uzayenda na iwe mugulu ya bankhondo , iwe na masoja wako. ''
2
Davide anati kuli Achishi , '' Ngati niso , muzaziwa chamene kapolo wanu angachite .'' Achishi anti kuli Davide , ''Nishi ine nizakupanga bodigadi wanga masiku yako yonse yaumoyo.''
3
Apa Samueli anali atamwalila , ndipo Israeli yonse inamulila eve nakumuika mumanda yaku Rama , mumuzinda wakwao. Naye Sauli , anali atapitikisa kuwachosa muziko wonse wanthu wamene wanali kukamba nawakufa kapena kukamba na mizimu.
4
Apo a Philisiti anazikolonganika pamozi nakubwela ndipo anankhoma misasa yawo pa Shunemu ; ndipo Sauli anasonkhanisa Israeli yonse pamozi , ndipo anamanga misasa pa Gilubowa
5
Pamene Sauli anaona gulu ya wankhondo yama Philisiti , anachita mantha , ndipo mutima wake unanjenjemela maningi.
6
Sauli anapemphela kwa Yehova kufuna thandizo, koma Mulungu sanamuyankhe - osati kupitila mumaloto kapena mu chimubuluso kapena aneneli.
7
Apo Sauli anati kuli atumiki wake , '' Nipezelenikoni muzimayi wa mizimu , pakuti ningayende kuli eve nakufunsa malangizo wake .'' Atumiki wake anati kuli eve , ''Onani aliko mukazi wa ku Endo wamene na zimvela kuti anakambisana na wakufa.''
8
Nchifukwa chake Sauli anazibisa , pakuvala vovala vachabe chabe nakuyenda , eve na wamuna awili anali naye . Anayenda kuli uja mukazi usiku. Anati , '' Niwombezeleko namuzimu ndipo uniwukisileko kuchokela kuli wakufa wamene nizatomola.''
9
Uja mukazi anati kuli eve , '' Ona , uziwa zamene Sauli anachita , mwamene analesela nakupitikisila kuchokela muziko waja wamene wakamba na wokufa na mizimu . Manje nichani uteya musampha pa moyo wanga , kuti unipayise?''
10
Sauli analapila kuli eve mzina ya Yehova nakunena kuti , ''Malingana Yehova niwamoyo , kulibe chilangiso chizakuchitikila iwe kamba ka ichi chinthu.''
11
Apo muzimayi anati , '' Nikuwushila ndani kuchokela kwa akufa ?'' Sauli anati , ''Niushileko Samueli ine.''
12
Pamene muzimu anaona Samueli , anapunda na mau yokwela nakukamba na Sauli, kuti , '' Waninamizila chani ? Pakuti ndiwe Sauli.''
13
Mfumu anati kuli eve,'' Osayopa . Waona chani? '' Muzimayi anati kuli Sauli , ''Niona mulungu achoka kunja kuchokela mudothi.''
14
Anati kuli eve , '' aoneka bwanji ? '' Eve anayankha kuti, '' Mwamuna wakalamba afukuluka ; niwovalikiwa mukhanjo .'' Sauli anaziwa kuti anali ni Samueli , ndipo anawelama nkhope yake kuchita kufika pansi , nakumuonesa ulemu.
15
Samueli anati kuli Sauli ,'' Wanisokoneza na kuniwushila chani? '' Sauli anayankha , '' Nine wotekeseka maningi , pakuti a Philisiti akonzekela kuchita nkhondo naine , ndipo Mulungu anithawa nakuti aleka kuniyankha vilivonse , kosati kupitila muli aneneli , nangu kupitila mumaloto . Nchifukwa chake nakuyitanani imwe ,kuti munganiziwise ine vamene nizachita.''
16
Samueli anati , ''Nanga ine nishi unipempha chani pakuti Yehova akuthawa nakusanduka ndani wako?
17
Yehova achita kwa iwe chamene anakamba kuti azakachita . Yehova ang'ambaku ufumu kuchosa mukwanja kwako nakupasa weve kuli munthu winangu - kuli Davide.
18
Chifukwa iwe suuna mvelelele mau ya Mulungu nakuti siunachite mkwiyo wake woyofya ma Ameleki , nchifukwa chake achita ichi kuli iwe lelo.
19
Yehova azapeleka Israeli pamozi na iwe mumanja yama Philisiti , ndipo mailo iwe na bana wako wamuna muzayamba kunkhala na ine kuno.Yehova azapeleka nayeve gulu ya masoja ya Israeli mumanja mwa ma Philisiti.''
20
Ndipo Sauli pamene apo anagwa nyutu pansi ndipo anakomoka chifukwa cha mau a Samueli . Anasila mphamvu chifukwa sanadye kanthu ija siku , angankhale uja usiku wonse.
21
Uja muzimayi anabwela kuli Sauli nakuona kuti anali wovutika maningi , anati kuli eve , ''Ona , kapolo wako mukazi akumvela mau yako; naika moyo wanga mukwanja kwanga ndipo namvela mau yako yamene wakamba kuli ine .
22
Manje nichifukwa chake , niku papata iwe , naiwe mvelelela mau yakapolo wako mukazi , ndipo leka nikupase tuchakudya tung'ono pali iwe . Udye pakuti unkhale namphamvu pakuti ukayende njila yakwanu.''
23
Koma Sauli anakana nakunena kuti , '' Sinizadya .'' Koma wanchito wake pamozi na uja muzimayi ,wamamufosing'a , ndipo anamvela kuli mau yao. Apo anauka kuchokela pansi nakunkhala pa bedi.
24
Muzimayi anali na kang'ombe koyina panyumba ; anafulumila nakukapaya ; anatenga unga wa tilingu , nakuwukanya tuma bola , nakupanga buledi ilibe chotumphisila muli tumabola twamene .
25
Analeta vija vakudya pali Sauli na wanchito wake , ndipo wanadya . Ndipo wananyamuka na kuyambapo wamene uja usiku.