Chapta 26
1
Maziphiti anabwela kuli Sauli pa Gibeya na kunena kuti, '' Kushe Davide sali wobisama mulupili lwa Hakila , yamene ili tikalibe kufika ku Jeshimoni?''
2
Apo Sauli ananyamuka nakuyenda kupolikilala kusanga yaku Ziphi , ali na thri sauzande wanthu wesankhindwa wamu Israeli pamozi naye , kufuna Davide mu sanga ya Ziphi.
3
Sauli anamanga misasa pa lupili lwa Hakila , yamene ili mukalibe kufika ku Jeshimoni , pambali pa musewu . Koma Davide anali kunkhala mu sanga , ndipo ana ona kuti Sauli anali kubwela kukonkha eve musanga.
4
Apo Davide anatuma akamuchoke nakuziwa kuti Sauli wabwela zoona .
5
Davide ananyamuka nakuyenda kumalo kwamene Sauli anali atakhoma misasa; anaona pamalo pamene Sauli anagona ,na Abinala mwana wa Neli, Genero wa Gulu yake yankhondo ; Sauli anagona mu musasa , ndipo wanthu wana khoma misasa mumuzungulaka , wonse wogona.
6
Apo Davide anati kuli Ahimelechi mu Hihiti , na kuli Abishai mwana wa Zeruia , mbale wa Joab , '' Ndani aza seluka na ine kuyenda kuli Sauli mumusasa ?'' Abishai anati , ''Ine ! Ine nizaseluka na imwe.
7
Apo Davide na Abishai anayenda kuli masoja usiku , Sauli analiko atagona mu m'kati mwamisasa namkondo wake wolasa pansi pa fupi na mutu wake . Abinala na masoja wanangu momuzunguluka .
8
Apo Abishai anati kuli Davide , '' Lelo Mulungu ayika mudani wake mumanja yako . Apa chonde lekani nimuphinile pansi na mukondo nankhonya imozi chabe . Sinizamuchaya kachiwili.''
9
Davide anati kuli Abishai , '' Osamuononga pakuti nindani angatambasule kwanja yake kuchitila chipongwe ozozedwa wa Yehova nakunkhala alibe mulandu? ''
10
Davide anati , ''Malingana Yehova niwamoyo , Mulungu azamupaya yeka ,kapena siku yake izafika yokufa , kapena azayenda ku nkhondo nakufa kwamene uko.
11
Mulungu asachilole kuti ine nitambasule kwanja kwanga mosusana na wozozedwa wake ; koma apa , nikupempha iwe , tenga mukondo wamene uli kumutu kwake na chikapu chamanzi , ndipo tiyeni tiyende.
12
Apo Davide anatenga mkondo na chikapu cha manzi kuchosa kumutu kwa Sauli , ndipo wanachokapo . Kunalibe futi aliyense wamene anauka , pakuti wonse wanali mtulo, chifukwa tulo kwakuya tochokela kuli Mulungu twenze tunawagwela weve.
13
Choncho Davide anayenda kumbali inangu yalupili na kuyimilila pa mwamba patali ; panali chimutunda chikulu pakati pawo.
14
Davide anapunda kuli banthu na kuli Abinala mwana wa Neri ; anati , '' Siuyankha , Abinala ?'' Apo Abinala anayankha kunena kuti, '' Ndiwe ndani nindani wamene akuwa kuli mfumu?''
15
Davide anati kuli Abinala ,'' Sindiwe munthu alibe mantha ? Ndani wamene ali monga iwe mu Israeli ? Ndani ndipo kuti siunamuyang'anile mbuye wako mfumu? pakuti winangu enze abwela kuti apaye mfumu a mbuye wako.
16
Ichi chinthu chamene wachita sichabwino . Malingana Yehova niwamoyo iwe ufunika kufa chifukwa sinakwanilise kulonda a mbuye wako , wozozedwa wa Yehova . Manje ona kwamene kuli mkondo wa ambuye wako na chikapu cha manzi vamene venze kufupi namutu wako!''
17
Sauli anaiziwa liwu ya Davide nakunena kuti, '' Aya nimau yako , mwana wanga Davide ?'' Davide anati , '' Nilizu yanga , ambuye wanga , mfumu .''
18
Anati , '' Nchifukwa chani ambuye wanga mupilikisa kapolo wanu ? Nachita chani ? Muli chimo yanji mumanja mwanga ?
19
Nchifukwa chake apa manje nipempha kuli imwe , lekani ambuye wanga a mfumu amvelelele kuli mau ya kapolo wanu , ngati ni Yehova wamene akuvundwani imwe pali ine kuti munichite chipongwe ine , lekani avomele chopeleka ; koma ngati nimunthu atembeleledwe mumensomwa Yehova, pakuti lelo wanipitikisa kunja , kuti ine nisagwililile ku chokolo chakwa Yehova ; wakamba kuti kuli ine , 'Yenda ukapembeze milungu inangu.'
20
Kansi manje nchifukwa chake , osaleka mwazi wanga ugwele pansi kutali na chinso cha Yehova ; pakuti mfumu yaku Israeli yabwela kunja kusakila nsanya imozi monga mwamene wina azangelela nkwale yamumalupili.''
21
Apo Sauli anati , '' Nachiwa , bwelela , Davide mwana wanga ,pakuti sinizakuchita futi choyipa , chifukwa moyo wanga waoneka wamtengo wapatali m'menso mwako lelo . Ona , na sobela uchipuba na kupanga misiteki yoyipa maningi.''
22
Davide anayankha nakukamba kuti , '' Onani mkondo wanu ulikuno , mfumu ! Lekani m'mozi mwa anyamata abwele kuno na kuwutenga akuleteleni kwamene mulili.
23
Mulungu amupase munthu aliyonse pali chilungamo chake nakukhulupilik kwake ; chifukwa Yehova enze akuyika mumanja mwanga lelo , koma sininapaye wozozedwa wake.
24
Onani , mwamene umoyo wanu wenze wa mutengo wapatalimumenso mwanga lelo , ndiye mwamene umoyo wanga uneke wa phindu maningi m 'menso mwa Yehova ,ndipo anipulumuseko ine kunichosa mu mavuto yonse .''
25
Apo Sauli anati kuli Davide , ''Udalisike , Davide mwana wanga ! Uzachita zoona vikulu ndipo uzakwanilisa mkunichita .'' Apo Davide anayenda njila yake , ndipo Sauli anabwelela kwao.