Chapta
1
Apa Davide anathawa kuchoka ku Nayothi mu Roma nakubwela nakukamba kuli Jonathan,''Nachita chani ?'' Kusalungama kwanga nikuti? Chimo yanga kuli wa tate wako Riyabwanji, pakuti afuna-funa kutenga moyo wanga?''
2
Jonathan anati kuli Davide,''Nchapatali siuzafa.Atate banga siwachita chinthu kapena chikulu kapena ching'ono kulibe kuniuzako ine. Nichifukwa chani watate wanga lwangabise ichi chinthu kuli ine ? Simuwamene chili.''
3
Kama Davide analapa futi nakukamba ati,Watate wako waziwa bwino kuti ine ninapeza chikondi kuli iwe. Anakamba ati,'Osamuwuza Jonathan za ichi, angakwinyilile!Koma malingama Yehova niwamoyo, ndipo na iwe ulimoyo, pakaliko koma mupata pakati pa ine na imfa,''
4
Apo Jonathan anati kuli Davide, ''chilichonse chamene uzakamba,nizakuchitila iwe.''
5
Davide anati kwa Jonathan, Mailo ni mwezi wanyowani,ndipo nifunika kunkhala pansi nakudya na Mfumu. Koma leka niyende kuti nikazibise musanga mpaka siku yachitatu mumazulo.
6
Ngati atate wako azanifuna m'jila iliyonse,ndipo iwe ukakambekuti,''Davide anapempela liwi molimbikila maningi kuli iwe pakuti angathamangile ku Bethelehemu muzinda wa kwawo; chifukwa nithawi ya nsembe yapa chaka kuja pamukoka wonse.
7
Ngati auzakamba kuti chili chabe bwino ninshi kapolo wanu nizankhala namutendele.Koma ngati azakalipa maningi,apo muzaziwa kuti waganizila kuchita choipa.
8
Nachifuka chake muchite mwachi fundo na kapolo wanu.Pakuti munangenesa kapolo wanu muchipangano cha Yehova naimwe.Koma ngati muli chimo mwa ine,munipaye imwe mwawene;ndaba nchifukwa bwanji ndipo chamene muzaniletela kuli wa tate wanu?''
9
Jonathan anati,chinkhale kutali na iwe!Ngati nizaziwa kuti atate wanga wanganiza choyipa kuti chibwele pali iwe,kushe ine siningakuwuze iwe?''
10
Apo Davide anati kuli Jonathan,''Ndani azaniuza ngati pali mpata wakuti atate wako azayankha mwa ukali maningi?''
11
Joathan anati kuli Davide,''Bwela,tiye tiyende kunja Musanga,''ndipo wonse abili wanayenda Musanga
12
Jonathan anati kuli Davide,''Yehova Mulungu wa Isaeli ankhale niumboni.Nikayenda kufunsa atate wanga pafupi fupi ino nthawi mayilo,kapena pa siku yachitatu,ona,ngati kuli manganiza abwino pali Davide, ninshi ine simungatume kuli iwe na kuchiulula kuli iwe?
13
Ngati chizakondwelesa atate wanga kuti akuchite choipa,Yehova achite kuli Jonathan namaningi futi ngati siniza chiulula kuli iwe nakukutumiza kutali,pakuti ungayende mumuntendele.Yehova ankhalena iwe,monga mwamene analili na watate.
14
Ngati nikali namoyo,kuche siuzanionesa ine kukhulupilika kwa chipangano cha Mulungu kuti nisafe?
15
Osajuwa ichipangano chanu kukhulupilika kwako kuchokela kju nyumba kwanga kwamuyaya-olo pamene Yehova azajuwa kuchosako wonse wa ndani wa Davide kuchoka paziko yapansi.''
16
Ndipo Jonathan anapanga chipangano na nyumba ya Davide kukamba kuti,''Mulungu afuna kulondolola kuchoka mukwanja kwa adani wa Davide.''
17
Jonathan analengesa Davide alapile futi chifukwa cha chikondi chamene anali nacho pali eve,chifukwa anamukonda mwamene anakondela moyo wake.
18
Apo Jonathan anati kuli eve,''mayilo ni mwezi wanyowani ,uzayeweka chifukwa mpando wako uzankhala palibe muntu.
19
Ukayenda kunkhala masiku yatatu,ukatelemuke Musanga nakubwela ku malo yamene wenze unabisamako weka pamene ichi chinthu chofuma kukupaya chenze mumanja,ndipo ukankhale pafupi na mwala Ezel.
20
Nizakaponya tolasila mu uta tutatu kuside kwake,monga nilasa kanthu.
21
Ndipo nizatuma munyamata wanga na kunena kuli eve kuti,'yenda utupeze tumivi,' Ngati nizakamba kuli munyamata wamung'ono, 'ona,miviili kumbali iyi yako;yatenga,''ninshi ukabwele;pakuti kuzankhala chitetezo kuli iwe osati choyipa, malingama Mulungu ni wamoyo
22
''Koma ngati nizanena kuli munyamata, 'ona, mivi yali kupitilila pali iwe,ninshi iwe akayende kwanu, pakuti Yehova akutumiza kutali.
23
Pali chipangano chamene iwe na ine takambilana, ona, Yehova ali pakati pa iwe na ine kwamuyaya.'''
24
Apo Davide anazibisa yeka Musanga.Pamene mwezi wanyowani unankhala,Mfumu inakhala pansi kuti adye chakudya.
25
Mfumu inankhala pamupando wake, monga mwa nthawi zonse, pamupando wamene unali kufupi kachiwumba.Jonathan anayimilila, ndipo Abinala anankhala pafupi kumbali kwa Sauli. Koma mala ya Davide panalibe munthu.
26
Chodabwisa Sauli sanakambepo chinthu chilichonse ija siku,chifukwa ananganiza ''chinthu chinangu chamuchitikila.Siwoyela; zoona siwoyera,''
27
Koma siku yachiwili, siku yokonkhapo mwezi wanyowani, malo ya Davide panalibe munthu. Sauli anati kuli mwana wake Jonathan ,''nichani mwana wa Jessi sanabwele kuchakudya kapena mailo loko lelo?''
28
Jonathan anamuyankha Sauli kuti, ''Davide anapempha molimbika kuli ine kuti ayende ku Bethelemu.
29
Anati ,''chonde lekani niyende. Pakuti Banja yathu iyendo chita nsembe mumuzinda, ndipo mbale wanga wani lamulila kuti nipezekeko. Lomba ngati napeza chifundo kuli imwe, napapata lekani niyende nikaone azibale anga.' nchifukwa chake eve sanabwele ku tebulu yamfumu.
30
Apo ukali wa Sauli unanyeka pali Jonathan, ndipo anati kuli eve, ''iwe mwana wa muzimayi wapotozeka, na wowukila! Nanga ine siniziwa kuti iwe unasankha mwana wa Jessi kunsoni zako wemwine, na kumanyazi ya chithanku cha a mai wako?
31
Pakuti malingana mwana wa Jessi ali wamoyo paziko yapansi, kulibe iwe loko ufumu wako. Kuti ukankhazikike.Manje kansi, tuma ndipo umulete kuli ine, ndawa afunika kufa vazoona.''
32
Jonathan anayankha atate wake kuti, ''Nipali chifukwa bwanji kuti afunika kupayiwa? Achita chani?
33
Apo Sauli anamuponyela mkondo wake kuti amupaye. Kamba ka ichi Jonathan anaziwa kuti atate wake analikufunisisa kuti amupaye Davide.
34
Jonathan ananyamuka kuchoka pa tebulo na ukali woyofya ndipo sanadye chakudya pa siku yachibili ya mwezi,Ndawa anankhala na chisoni pali Davide chifukwa atate wake wenze wanamusula eve.
35
Mumawa Jonathani anayenda kusanga monga mwachipangano kumalo anene anapangana na Davide, ndipo munyamata mung'ono anali nayeve.
36
Anati kuli munyamata wake ''thamanga upeze mivi yamene naponya'' pamene munyamata anali kuthamanga, analosa muvi kumupitilila.
37
Pamene munyamata anafika pamalo pamene muvi wamene anaponya Jonathani unagwela, Jonathani anamuyitana munyamata nakuti kushe muvi siuli kusongola kupitilila pali iwe?''
38
Ndipo Jonathani anayitana munyamata, yendesa, fulumila, osankhalila!'' Apo munyamata wa Jonathani ana wonkhesa ija mivi nakubwela kuli Mbuye wake.
39
Koma munyamata sanaziwe vilivonse.Chabe Jonathani na Davide ndiye anaziwa za ichu chisinsi.
40
Jonathani anapasa zida zake zankhondo kuli munyamata wake nakukamba kuli eve kuti, ''yenda,vipeleke mutawuni,''
41
Nthawi ying'ono ing'ono maningi atayenda miyamota, Davide anayimilila kuchokela kumbuye kwa chulu,anangowa kuyang'ana nkhope yake pansi, nakuwelama yeka katatu. Wanapasana makissi nakulila mokuwa pamozi,analila maningi kuchilapo ni Davide.
42
Jonathani anati kuli Davide, yenda muntendele,chifukwa ise tonse tinalapila m'zina ya Yehova, leka Yehova ankhale pakati pa iwe na ine,na pakati pa mbadwa zanga na mbadwa zako,kwamuyaya.''' Apo Davide anayimilila nakuchoka, ndipo Jonathani anabwela mumuzinda.