Chapta 19
1
Sauli anati kuli mwana wake Jonathani na kuli wanchito wake wonse kuti wafunika kumupaya Davide . Koma Jonathani , mwana wa Sauli , anali kukondwela maningi na Davide. Nchifukwa chake Jonathani anauza Davide , '' Sauli tate wanga afuna kukupaya iwe .
2
Nchifukwa chake uchenjele kuseni ndipo uzibise mumalo osaziwika .
3
Ine nizayenda kunja nakuimilila pafupi na batate wanga munsanga mwamene uzankhala , nakukamba na watate wanga za iwe . Nikayenda kuziwapo vilivonse ine nizakuwuza.''
4
Jonathani anakamba bwino kuli tate wake za Davide nakunena kuti eve kuti , osati mfumu ichimwile kapolo wake Davide . Pakuti sianakulakwilani imwe, ndiponso zichitidwe zake zakuletelani ubwino.
5
Pakuti anatenga moyo wake mumanja mwake popaya mu Philisiti . Yehova analeta kuchimfya kukulu kuli Israeli yonse . Munachiona ici nakukondwela maningi.Nchifukwa chani mufuna kuchimwila mwazi wosalakwa po paya Davide kulibe chifukwa?''
6
Sauli anali kumuelelela Jonathani . Sauli analapila kuti, ''' Malingana Yehova niwamoyo , sazapayiwa.''
7
Apo Jonathani anayitana Davide , ndipo Jonathani anamuwuza izi zinthu zonse , Jonathani anabwelesa Davide kuli Sauli , ndipo anali mumenso mwake monga kudala.
8
Kunali nkhondo futi , ndipo Davide anayenda kunja kukamenyana nama Philisiti nakuwa gonjesa nakuwapaya maningi . Wanamuthawa.
9
Muzimu woyipa wotumiziwa na Yehova unabwela pali Sauli pamene anali kunkhala munyumba mwake na mkondo wake mumanja ndipo pamene Davide anali kuliza chisulo chake .
10
Sauli anayeselela kumuphinila kuchiwumba namukondo Davide , koma anamyomyoloka kuthawa panali Sauli , mwakuti Sauli analasa muchiwumba na ija mkondo . Davide anajumpha nakuthawa uja usiku.
11
Sauli anatuma nthumwi zake kunyumba kwao Davide kumulonda pakuti akamupaye kuseni . Michala , mkazi wa Davide , anamuwuza , ''Ngati siupulumusa moyo wako usiku walelo mailo uzapayiwa.''
12
Apo Michala anaselusa Davide kupitila pa windo . Eve anayenda nakuthawa, nakusowa.
13
Michala anatenga chikadoli chamunyumba wakuchigoneka pa bedi . Ndipo anayika pillo wa masaka yambuzi kumitu , nakuchiphimbana vovala.
14
Pamene Sauli anatenga nthumwi kuti zitenge Davide , mkazi wake anati , '' Mwodwala.''
15
Apo Sauli anatuma nthumwi zoyenda kumuona Davide ; anati , ''Muleteni kuno kuli ine mubedi , pakuti nimupaye.''
16
Pamene anthumwi wanangena mukati , onani ; chikadoli chamunyumba chinaligone pabedi pamozi napillo ya masaka ya mbuzi kumitu kwake .
17
Sauli anati kuli Michala . ''Waninamila chani nakulekelela mudani wanga ayenda , pakuti athawa nakusowa ?'' Michala anayankha Sauli , ''Anati kuli ine , ' Nileke niyende ufuna nikupayile chani iwe?''
18
Apo Davide anatthamanga nakuthawa , ndipo anayenda kuli Samueli ku Roma na kumuuza zonse zamene Sauli anachita kuli eve. Apo eve na Samueli anayenda na kunkhala ku Nayothi.
19
Chimauziwa kuli Sauli , kuti , ''Onani , Davide aliku Nayothi mu Roma.''
20
Apo Sauli anatuma nthumwi kuti akamugwilile Davide . Pamene anaona gulu ya aneneli ili kusesema , ndipo Samueli amilila monga musogoleli wawo , muzimu wa Mulungu unabwela pali waja nthumwi wa Sauli , ndipo naweve wananenera.
21
Pamene Sauli anuziwa za ichi, anatuma nthumwi zinangu , ndipo naweve anachita uneneli . Ndipo Sauli anatuma ma nthumwi wenangu gulu yachitatu, naweve futi wanasesema .
22
Ndipo na yeve anayenda ku Roma anakufika chisime chitali chaku Seku . Anafunsa , '' Alikuti Smueli na Davide?'' Winangu anakamba kuti , ''Onani, wali pa Nayothi mu Roma . ''
23
Sauli anayenda ku Nayothi mu Roma.Muzimu wa mulungu unabwela pali eve,ndipo pamene anali kuyenda ananenela mpaka anafika pa Nayothi mu Roma.
24
Anavula mochita kung'amba vovala vake kunenela nayeve mumenso mwa Samueli . Anagona chinthako muzuba monse na usiku wonse . Ichi nichifukwa chake wana funsa '' Kushe Sauli anayeve ali m'mozi wa aneneli?''