MUTU 4

1 2 Koma Yesu, kunkhala ozozedwa ndi muzimu oyela, Anabwelela ku musinje wa Yodan, Ndiponso nasogoledwa ndi muzimu oyela kuyenda muchipululu mwamene anaenda masiku makumi ndi anai kuyesedwa ndi satana.Sianadye chilichonse masiku yaja, Ndiponso pokusila kwanthawi ija anamvela njala. 3 4 Satana ananena kwaiye, '' Ngati ndiwe mwana wa Mulungu, Sandula mwala izi kunkhala Mukate.''Yesu anamuyankha, '' Nicholembedwa, '' Kuti munthu siazankhalila mukate weka.'' 5 6 7 Koma satana anamusogolela Yesu kumupeleka pamalo yapamwamba ndiponso anamulangiza maufumu yapaziko pakanthawi kang'ono.Ndi satana ananena kwaiye, ''Kuti nizakupasa mphamvu zonse ndi ulemelelo, chifukwa wapasiwa kuli ine, Nndiponso ningapase aliyense. chifukwa chaichi, ngati unganigwadile pansi ndiponso unipempeze ine, chisankhala chako. 9 10 11 Komanso satana anasogolela Yesu ku Yelusalemu nakumupeleka pamalo yotalimpisa yapa tempele, Ndiponso ananena kwaiye, ''Ngati ndiwe mwana wa Mulungu zitaye weka pansi kuchokela pano. Chifukwa chinalembedwa, 'Azatuma angelo abo ameneazakusamalila, ndi kukuchingiliza iwe,' 'Ndiponso, ' Bazakunyamula mumanja yao nakukunyamula pamwamba, kuti usazigwesele pamwala.'' 12 13 Napakumuyankha, Yesu ananena, '' Chinanenewa, '' Kuti usafake Mulungu wako mumayeso.'' Pamene satana anasiliza kumuyesa Yesu, Anamusiya iye ndikuyenda paka panthawi ina. 14 15 Koma Yesu anabwelela ku Galili mumphamvu zamuzimu. ndiponso utenga pali Iye unamwazikana malo yonse yenzo zingulila chija chigao. Ndiponso anayamba kupunzisa mutempele ndiponso bonse anamutamanda. 16 17 Iye anabwela ku Nazareti, muzinda mwamene anakulila, ndiponso kulinganiza na mwambo wake, Enze kungena mutempele pasiku la sabata, kulingana ndi mwambo, Ndiponso enze kuimilila ndi kubelenga naliwu lapamawmba.Buku ya muneneli Aizaya Inapasidwa kuli Iye. Analikusegula buku ija, Ndiponso anapeaza pamalo pamene chinalembedwa, 18 19 '' Muzimu wa Mulungu alipali ine, chifukwa anizoza ine kulalika utenga wa bwino kuosauka. Anituma ine kulalikila pa kumasusila omangidwa, ndiponso kubwezedwa kwa manso osapenya, ndi kumasula ogwedezeka, ndi kunenela pachaka za chisomo cha Mulungu.'' 20 21 22 Komanso anaivala buku ija, ndikubwezela bamene analikusunga ndi kunkhala pansi.Manso yabonse muja mutempele yanalipaliche pali enve. Anayamba kukamba kuli iwo, '' Kuti lelo ayamalemba yafikilizika mukumvela kwanu.'' Bonse muja mumalo anapelekela umboni pazamena ananena ndiponso bonse banadabwisiwa pamau yachisomo yamene yanalikuchoka mukamwa kake. Banali kunena kuti, '' Uyu ni mwana wa Yosefe, kodi sichocho?'' 23 24 Ananena kwa iwo, '' Chachendi muzanena proverb iyi kuli ine, ''Adotolo, zichiliseni mweka.Vilivonse vamene tinamvela mulikuchita mu kapenamu, chitani chimozi mozi muno mumuzinda wanu.'' Koma ananena, '' Chonadi ninena kwainu, kulibe muneneli wamene analandilidwa mumuzinda wake. 25 26 27 Koma muchoonadi nikuuzani kuti kunali mazenela yambiri mu Izilaeli munthawi ya Elijah, pamene mulengalenga unavaliwa zaka zitatu ndi makakumi asanunu ndi kamozi, ndiponso njala yaikulu inagwela pantaka ija.Koma Elijah sianatumiwe kulialionse, koma chabe ku zerepata wa mu sidoni, kuli ofedwa wamene analikunkhala kuja.Ndiponso kunali akungu ambiri mu Izilaeli ija nthawi ya muneneli Elisha, Koma kulibe anachilisiwapo kucheselako Namani waku sirian.'' 28 29 30 Banthu bonse musinagogi anazozedwa ndi ukali pamene anamvela izi zinthu. Onse anachamuka, ndikumupatikiza kuchoka mumuzinda, ndiponso anamusogolela pamwamba pa phiri kwamene muzinda unamangiwa, kuti bamutaye kuchokela pamwamba paphiri.Koma anapitila pakati kao ndikuenda kumaloena. 31 32 Ndipo anaenda kukapenamu, muzinda wa mu Galilileyo, ndiponso anayamba kubapunzisa paza sabata.Anadabwisiwa pakupunziza kwake, chifukwa anali kunena ndi ulamulilo. 33 34 Koma mumasinagogi kunali mwamuna wamene anali namuzimu onyansa, ndiponso analila ndi liu lapamwamba, '' Ah! nanga nichani chamene tingachite na iwe, Yesu waku Nazareti? Kodi wabwela kutiononga? Niziba kuti ndiwe _ oyela wa Mulungu.'' 35 36 37 Yesu anazuzula muzimu onyansa, ndikunena, '' Osakambe kuti chokamo mwaiye!'' Pamene muzimu onyansa anagwesa mwamuna pansi pakati paiwo, anachoka mwa iye, ndiponso sianamuononge munjila iliyonse.Banthu bonse banadabwa, ndiponso anapitiliza kukambapo pali izi kuliwina ndi muzake. Bananena kuti, '' Kondi ni mau yabwanji aya? Alamulila ndi mizimu zonyansa ndi ulamulilo ndipo ndi mphamvu ndiponso zichoka.'' Ndiponso utenga pali iye unayamba kuyenda pasogolo pamalo yaliyonse yanazungulila yaja malo. 38 39 Ndiponso Yesu anaenda choka musinagogi ndiponso anangena munyumba ya Simoni. Koma bapongozi ba Simoni bakazi analikuvutika ndimatenda, ndiponso anabapapatilako. Koma anaimilila pali iye ndiponso anazuzula matenda, ndiponso yanatuluka mwaiye.Pameneapo ananyamuka ndiponso anayamba ndi kuatumikila. 40 41 Pamene zuba anali kungena, banthu onse analeta odwala kuli Yesu anali ndimatenda osiyanasiyana. Anafaka zanja palialionse ndiku achilisa.Mizimu zonyansa nazo zinachoka mulibambiri, na kulila ndikunena kuti, '' Ndiwe mwana wa Mulungu.''Yesu anazuzula mizimu zonyansa ndiponso sianazisilile kukamba, chifukwa anaziba kuti ndiwe Kristhu. 42 43 44 Pamene nthawi yamuzuba inafika, Anayenda mumalo yobisika. Banthu bambiri banali kumusakila ndiponso anabwela kumamalo kwamene enzelili. banayeselela kumulesa kuti asayende nakubasiya. Ndiponso ananena kwaiwo, '' Nifunikilanso kulalikila utenga wabwino pazaufumu wa Mulungu kumizinda zinangu, nichifukwa chaichi ninatumiwa.'' Ndipo anapitiliza kulalilila mumasinagogi mumalo yonse ya mu judeya.