MUTU 2

1 2 3 Koma muli yaja masiku,chinabwela chachitika kuti Siza Ogastasi anatuma mbiri yakuti kupenda kwa banthu bonse kuchitike muli ziko lija. Ukukunali kupenda koyamba pamene Kilinas anali mukulu waboma mu silia.Koma aliyense anapita kumizinda yao ndi kukalembesa mazina yao. 4 5 Ndi Yosefe anapita kuchokela kugalileyo,mumuzinda wa nazareti, nakuyenda ku judeya, mumuzinda wamene uitanidwa Davidi wamu betilehemu, chifukwa analikuchokela mubanja ya mubado wa Davidi.Anapita kuja kukalembesa pamozi ndi Mariya, wamene enze okolobekelewa kuli iye ndiponso anali namimba. 6 7 Manje chinabwela chachitika kuti pamene bakalikwamenekuja, nthawi inafika yobala. Anabala mwana mwamuna, mwana wake oyamba, ndiponso anamu vininkila na nyula yopitamo milaini, ndiponso nakumufaka mukola, chifukwa kunalibe malo muja mwamene anafikila. 8 9 Kunali boyembela ngo'mbe muja muchigao bamene banalikunkhala muminda, kuyembela ngo'mbe zao usiku.Mungelo wa Mulungu anaonekela kwa iwo, ndi ulrmelelo wa Mulungu unalangisiwa kuli bemve, ndiponso anayofedwa. 10 11 12 Koma mungelo ananena kwa iwo, '' musayofedwe, chifukwa naleta utenga wa bwino wamene uzabwelesa chimwemwe chachikulu kubanthu bonse.Lelo mulumusi abadwa mumuzinda wa Davidi! iye ndiye kilisitu ambuye! ichi chizankhala chizibiso chamene chiza pasiwa kuli iwe, uzapeza mwana opombewa munyula yamilaini wamene alimukola.'' 13 14 Mosachedwa angelo analikwamene kuja nagulu likulu la asikali ochekala kumwamba atamanda Mulungu, ndi kunena, Ulemelelo kwa Mulungu mumwambamo, ndiponso lekani pankhale mtendere pa ziko kulibaja banthu baja bamene iyo bamvesedwa bwino.'' 15 16 Chinabwela chachitika kuti pamene angelo anachoka pamalo yao ndi kuyenda kumwamba, oyembela ngo'mbe anazi uza iwo oka, '' Tiyeni manje ku batilehemu, tikaone ichi chamene chachitika, chamene amuye alengesa kuti ise tizibe.'' Anaendisa kuyenda ndiponso anapeza Mariya ndi Yosefe, nakupeza mwana agona mukola. 17 18 19 20 Pochekala kumuona,analengesa kuziba chamene chinauziwa kuli bemve pamwana uyu.Bonse bamene bana mvela banali odabwisiwa ndichamene anauziwa nabaja oyembela.Koma Mariya anangopitiliza kuganizila pazinthu zonse zamene anamvela, ndi kuzisungilila mumutima wake. Oyembela anabwelamo, ndiponso analikulemekeza ndi kutamanda Mulungu palizonse zamene banamvela ndi kuona, monga mwamene chinakambidwa kuli benve. 21 Pamene masiku asanu ndi yatatu anafika, ndiyepamene anajubiwa, anaitaniwa zina Yesu, Zina yamene anapasiwa na angelo pamene akalibe kumitiwa mumimba. 22 23 24 Pamene masiku ofunikila kuzembululiwa yanakwana, kulinganiza ndi malamulo ya Mosesi, Yosefe ndi Mariya anamuleta mutempele mujelusalemu kumupasila kuli Mulungu. Monga mwamene chinalembewa mumalamulo ya Mulungu, Mwamuna aliyense wamene amasegula , azankhala opatulidwa na Mulungu.'' Koma anapeleka nsembe kulinganisa namwamene chinakambiwa mumalamulo ya Mulungu, '' Tunkhunda tubili loko tubana tun'gono tubili twamapijoni.'' 25 26 Kunaliko mwamuna mujelusalemu otanidwa simoni ndiponso anali olungama ndi ozipelaka.Anali kuyanganila pakubwezewa kwa Izilaeli,Ndiponso muzimu oyela anali paliiye.Chenze chinavumbulusiwa kwaiye na muzimu oyela kuti siazaona infa pamene akalibe kuona ambuye wa kristhu. 27 28 29 Kusogolelewa mwa muzimu, simoni anabwela mutempele.pamene makolo analeta mwana mun'gono Yesu, kubwela kuchita kulinganiza na mwambo wa malamulo, anamutenga mumanja yake ndi kutamanda Mulungu na kunena, '' kuti lekani mutumiki wanu ayende mwa mtendere, Ambuye, kulinganiza na mau yanu. 30 31 32 Menso yanga yaona chipulumuso chanu, chamene mwakonzeka pamanso yabanthu bonse: Nyali yachivumbuluso kuli majentao ndiponso ulemelelo kubanthu banu Izilaeli.'' 33 34 35 Batate ba mwana na bamai bake anali odabwisiwa panzithu zamene zina kambika pali iye. Simoni anaba dalitsa ndi kune kwa kuli Maliya mai wake, '' Onani, uyu mwana anasankidwa kwaio bamene ogwesewa ndi kunyamuliwa kwa banthu bambili mu Izilaeli ndiponso kwachiziwiso chamene chinakaniwa__ ndiponso monga lupanga ong'amba umoyo wanu_ pakuti maganizilo yamitima zambili ya vumbulusiwe.'' 36 37 38 Muneneli otanidwa zina Anna analiko. analimwana mukazi wa faniwelo kuchoka mumutundu wa Asha.Anali mukulu maningi.Anankhala na mwamuna wake zaka makumi ndi awiri kuchokela kuunamwali wake, ndiponso anali ofelewa zaka 80.Sianachokepo mutempele chifukwa analikutumikila mumapempelo ndi kusala kudya, usiku ndi muzuba. pali ijanthawi, anabwela kulibemve ndiponso anayamba kupeleka matamando kwa Mulungu ndi kukamba pa mwana kwa alionse analiku kuembekezela chipulumuso cha Yelusalemu. 39 40 Pamene anasiliza zonse izi banali kufunikila kuchita kulingani ndi malamulo ya Mulungu, Banabwelela kugalileyo, mumuzinda wao wa Nazareti. Mwana anakula ndiponso anali ndi mphamvu, kuchulukila munzelu ndiponso chisomo cha Mulungu chinali pali iye. 41 42 43 44 Makolo bake banalikuyenda chaka chilichonse ku Yelusalemu kumadyelelo ya paskha.Pamene anali ndi zaka makumi yabili ndi tubili, banaendanso panthawi ya mwambo wa madyelelo.Kuchekela pamene banankhalako masiku yokwana yamadyelelo, anayamba kubwelelamo ku nyumba kwao.Koma munyamata Yesu anasalila mu Yelusalema ndiponso makolo yake sibanazibe.Banalikuganizila kuti kapena alinagulu yamene anali nao pamodzi, koma anaenda ulendo uyu siku limozi.Ndiponso anayamba kumusakila kuliba banja lao ndi pa abwenzi ao. 45 46 47 Pamene sibana mupeze, anabwelela ku Yelusalemu ndi kuyamba kumu sakila kuja.China bwela chachitika kuti pochokakela masiku yatatu, Bana mupeza mutempele, Enze nkhezi pakati ka apunzisi, kumvelela kwaiwo ndi kufunsa mafunso.Bonse banamumvela anadabwa pa kumvesesa kwake ndi mayankho yake. 48 49 50 Pamene bana muona, bana dabwa. bamai bake bananena kuli iye, '' Iwe mwana, nichifukwa chachani watichitila ivi iyi njila? Mvela ine nabatate bako tenzekukusakila.'' Ananena kwaiwo, Nichani chamene munisakilila? kodi simunazibe kuti nifunikila kupezeka munyumba ya batate banga?'' koma sibanamvesese chamene analikutanthauza pa mau aya. 51 52 Ndipo anabwelela kunyumba ndi benve ku Nazaleti ndiponso anali omvelela kwa iwo. Bamai bake anasungilila zonse izi mumutima wao.Koma Yesu anapitiliza kukula munzelu za kuya ndi kutupi, ndiponso anachulukila muchisomo na Mulungu ndipo ku banthu.