Mutu 1

1 2 3 4 Ambiri ayeselela kufaka mundandanda, ndikufotokoza pazinthu zamene zinafikilizi kwaise, pamene anazipasila kwaise, iwo amene kuchokela pachiyambi anali akamboni amanso mpenya ndi atumiki autenga.kodi kwainenso chinaoneka chabwino_ pamene anafunisisa mundandanda paza iyi ntano yazinthu zonse kuchokela kuchiyambi- kuti alembe mundandanda paza iwe, oposa kuchenjelesa Theofilas.Ichi chinali mwatelo pakuti muzibe chonadi pazinthu zamene iwo anauziwa. 5 6 7 Munthawi yamasiku ya Helodi, mfumu ya bayudah ,kunali wina opeleka wansembe ndi zina la Zachariya, kuchekela kuchigao cha Abiya.mukazi wake analikochokela pa bana bakazi ba Aaroni,ndizina lake linali Elizabeta.Onse anali olungama pamanso ya Mulungu, ndi kumvelela yonse malamulo ndi mwambo za Mulungu. koma analibe mwana , chifukwa Elizabeta anali osabala, ndiponso onse abili anali okula mumuzinku paliija nthawi. 8 9 10 Koma chinabwelo pezeka kuti Zachaliya anali pamanso pa Mulungu,kuchita zinchito zake zaopeleka wansembe kulinganiza na ndandanda ya chigao chake.kulinganiza ndi njila yao posankha kuti niuti opeleka wansembe wamene angatumikile, anasankhiwa ndi njuga pongena mutempele ya Mulungu kukashoka nsembe.Yonse maunjiunji ya banthu yanali kupempela panja paliija nthawi yamene anali kushoka nsembe. 11 12 13 Koma mungelo wa Mulungu anaonekela kwa iye ndikuimilila kuzanja la manja laguwa yansembe.Pamene Zakaliya anamuona anayofyewa ndi kugwela kwa iye. Koma mungelo wa Mulunga ananena kwa iye, ''Usayofyewe, Zakaliya, chifukwa mapempelo yako yamveka. mukazi wako Elizabeta azakubalila mwana mwamuna. Uzamuitana zina yake Yohane. 14 15 Uzankhala na chimwemwe ndi chisangalalo, ndipo ambiri azamwetukila ku badwa kwake.Azankhala wamukulu pamanso ya Mulungu.Asakamwepo vinyu loko zozazamwa maningi, ndipo azazozedwa ndi muzimu oyela kuchokela mu mimba mwaba maibake. 16 17 Ndi banthu bambiri baku Isilaeli azapindimukila kwa Mulungu.Iye azaenda pasogolo pamanso ya Mulungu mumuzimu ndi mphamvu za Eliyah.Azachita izi kuti apindimule mitima ya azitate ku bana bao, pakuti bajabamene sibamvelela baende mu nzelu zaolungama- nolengesa banthu baMulungu kunkhala okonzekela iye.'' 18 19 20 Zakaliya ananena kwamungelo, '' kuti ningazibe bwanji izi? popeza ndine mwamuna okakalamba ndi mukazi wanga niokotata maningi.'' mungelo anayankha ndi kunena kuli iye, ''Ndine Gabuliyela, wamene aimilila mumanso pa Mulungu. nenze ninatumiwa kukamba naimwe, kuleta uyu utenga wabwino.Ndiponso, uzankhala chete, ndikukangiwa kukamba, kufikila na siku lamene izi zinthu zi zafikilizika.Ichi nichifukwa chakuti siunakululupile mau yanga, yamene yazafikilizika pa nthawi yokwana.'' 21 22 23 Koma banthu banali kuembekeza Zakaliya. Anali odabwa popeza kuti analikutaya nthawi yambiri mutempele.Ndiponso pamene anachoka, sianakambe ndi bemve. Anazindikila kuti anaona mansompenya pamene anali mutempele.Anapitiliza kualangiza ziziwiso, ndi kunkhala mwakachete.Inabwela yafika nthawi yake yamasiku yosebenza yanasila, Anaenda kunyumba kwake. 24 25 Pambuyo yamasiku aya,mukazi wake Elizabeta anamita.Anazipatulako eka pa myezi zisanu. ananena, ''Kuti izi ndiye zamene Mulungu anichitila ine pamene ananiyanganila ndi chisomo pakuti, achosepo manyazi paliine kubanthu.'' 26 27 28 29 Mu mwezi wachisanu na kamozi, Mungelo Gabriela enze anatumiwa kuchokela kwa Mulungu kumuzinda wa Galileyo wamene aitanidwa Nazareti, kukobekela namwali kumwamuna otanidwa zina Yosefe.Anali wambali lamunyumba ya Davidi, Ndi zina lanamwali uyu linali Mariya.Anabwela kwa iye ndi kunena, ''Mulibwanji, inu odala! Ambuye alinanu.'' Koma anali osokonezeka kamba ka mau yake ndiku dabwisiwa nakunena ati kodi, kangankhale kaposhedwe ka bwanji. 30 31 32 33 Mungelo ananena kuli iye, ''Usayope, Mariya, wapeza chisomo na Mulungu.Ona, iwe uzamita mumimba mwako ndikubeleka mwana mwamuna.Uzamuitana zina 'Yesu.' Azankhala wamukulu, ndiponso azaitaniwa mwana waolemekezeka.Ambuye Mulungu azamupasa ufumu wamumubado wa Davidi.Utumiki wake uzankhala pa nyumba ya Jacob muyayaya, ndiponso ufumu wake siuzasila.'' 34 35 Mariya ananena ku mungelo, ''Kodi izi zichitika bwanji, popeza kuti sininagonepo na mwamuna?'' Mungelo anayankha ndikunena kwa iye, ''Muzimu oyela azabwela pali iwe, ndi mphamvu zawakumwamba zizabwela pali iwe. koma oyela wamene azabadwa azaitaniwa mwana wa Mulungu. 36 37 38 Ndiponso ona, mubale wako Elizabeta amita mwana mwamuna muunkonte wake. Uyu nimwenzi wachisanu na kamozi, iye wamene anali kuitanidwa osabala.Kulibe chovuta kwa Mulungu.'' Mariya ananena, ona'' ine ndine mutumiki mukazi wa Mulungu.Lekani chinkhale vameneivo kulinganisa na utenga wanu.'' Ndiponso mungelo anamusiya. 39 40 41 Koma mariya pamasiku yaja anaima mwamusanga ndiponso anenda muziko lamaphiri, mumuzinda wa judeya. Anaenda munyumba ya Zachariya ndi kuposhana na Elizabeta.Koma chinachitika nichakuti pamene Elizabeta anamvela moni wa Mariya, mwana mumimba yake anajumpa, ndiponso Elizabeta anazozedwa ndi mphamvu za Muzimu Oyela. 42 43 44 45 Ananyamula ndi liu lake na kukambila pamwamba, Odala ndinu pabakazi, ndiponso zibeleko za mumimba mwanu nizodala.Ndiponso nichifukwa chachani kuti chachitika kwaine kuti amai ba Mulungu wanga kuti angabwele kwaine? Koma onani, pamene liu lakuposha kwanu labwela kumatu yanga, mwana mumimba yanga ajumpa na chimwemwe.Ndiponso niodala wamene akulupilila chifukwa kuzankhala kufilizika kwamau yamene Mulungu anena kwa iye.'' 46 47 Mariya ananena kuti, '' Umoyo wanga ulemekezeka ambuye, Ndimuzimu wanga usangalila Mulungu wa mupulumusi wanga. 48 49 Koma ayanganila pankhalidwe langa lapanshi ine kapolo wake mukazi. koma onani, kuchela manje mibado zonse zizani itana odala.chifukwa iye wamene aliwa mphamvu achita zazikulu kuli ine, ndi zina lake niloyela. 50 51 Chifundo chake chichokela kumibado na mibado kuli aba bamene ayopa iye. Alangiza mphamvu zake ndi zanja lake; ndi kusalanganya iwo amene aliozikweza mumaganizilo ya mitima zao 52 53 Anataya mafumukazi kuchoka pa maufumu wao.Ndiponso anakweza iwo apamalo yapansi.Anazoza anjala ndi zinthu za bwino,koma iwo olemela anabatuma manjamanja. 54 55 Apasila tandizo kwa Izilaeli mutumiki wake, monga mukukumbuka chifundo chake (monga mwamene anakambila kuli azitate atu) kuli Abraham ndi mibado zake muyayaya. 56 57 58 Mariya anankhala na Elizabeta monga mwezi itatu ndi kubwelela kunyumba kwake.Koma nthawi yobeleka mwana inafika ndiponso anabala mwana mwamuna, Bamene analikunkhala nao ndi achibululu anamvela kuti Mulungu analangiza chifundo kwa iye, ndiponso anasangalala ndi iye. 59 60 61 Koma chinachitika pasiku lachisanu natutatu pamene anabwela kuzembulula mwana. Asembe bamuitana ''Zakaliya,'' zina yaba tate bake,Koma amaibake banayankha ndikunena, ''Iyayi azaitaniwa Yoani.'' Ananena kwaiye, ''Ati kulibe paachibululu anu amene ataniwa Yoani.'' 62 63 Anapanga ziziwisilo kwa atate bake kuti azibe vamene enzofuna kumuitana.Atate bake anafunsa tebulo yolembelapo, ndi kulemba, '' kuti zina lake ni Yoani.'' Onse anankhala odabwisiwa pali ichi. 64 65 66 Pameneapo chabe kamwakake kana seguliwa ndi lilime inamasuliwa. Anakamba ndiku tamanda Mulungu.Kuofewa kunabwela palionse amene analikungala omuzingulila. Izi zonse zinthu zinawanda monsemonse mumaphiri ya mumuzinda wa judeya. Ndi onse anamvela anazisunga mumitima zao nakunena, '' Kodi azankhala mwana wabwanji uyu?'' chifukwa zanja la Mulungu ilipali iye. 67 68 Batate bake a Zakaliya anazozedwa ndimuzimu oyela ndikupasa uneneli, kuti, Matamando yankhale kuliambuye , Mulungu wa Izilaeli, chifukwa abwela kutandiza ndiponso kufikiliza chiombolo chabanthu bake. 69 70 71 Akweza lisengo lakalachipulumuso kuli ise ba munyumba ya mutumiki wake Davidi, monga mwamene ananenela ndi kamwa kaaneneli oyela amene analiko nthawi yakudala.Azaleta chipulumuso kwaadani bathu ndiponso ndi kuzanja yabonse bamene batizonda. 72 73 74 75 Azachita izi kuonesa chifundo kuli azitatate bathu ndiponso kuakumbusa chipangano choyela, chilapo chamene ananena kuli Atate watu Abraham.Analapa kutipasa ise, popeza kuti anatiombola kuchoka kuzanja la badani bathu, kuti tikamutumikile kopanda mantha, muchiyelo na muchilungamo kwaiye masiku yatu yonse. 76 77 Inde, ndi iwe, mwana, uzaitaniwa muneneli wauyo wapa mwamba, chikufukwa uzaenda pasogolo pamanso yambuye kukonza njila zake, nakukonzeka banthu pakubwela kwake, na kupasa nzelu zachipulumuso kubanthu bake naku kululukila machimo. 78 79 Izi zizachitika kamba kachifundo cha Mulungu watu , chifukwa chakuti zuba iwala kuchaka kumwamba azabwela kutitandiza, kuwala kuliabo bamene bankhala mumudima ndiponso muchinfwile cha infa.Azachita izi kusogolela mendo yatu munjila ya mtendere.'' 80 Koma uyu mwana anakula ndiponso anabwela alimba mumuzimu, ndiponso anali muchipululu kufika namasiku yoonekela potuba kuli a Izilaeli.