1 Kwa chimwecho okondedwa wanga, anyiyao nikulumbilani, anyiyao ndi chisangalalo nd kolona langa, imenichimiile pakati pa mulungu anyaimwe mabwenji okondedwa. 2 Nikupempha iwe Eudia, ndi nikupempha iwe Sintika, mubwezele kugwilizana kwanu kwa mtendele pakati panu, kwa chifuko anyaimwe mwaonche mwawili mudalunjana ndi Mulungu. 3 Kwa chazene, nikupemphaninchoni anyaimwe anchito anjanga, atangatileni anyiyawa wachikazi pakuti adatumika pamoji ndi ine pakati popeleka mau la Mulungu. 4 Pakati pa ambuye masiku yonche. Tena sinikambe, sangalalani. 5 Upole wanu ndi ujuwikane kwa wanthu onche, ambuye ali pafupi. 6 Msachaucha kwa chinthu chalichonche, pambuyo pake, chitani vinthu vanu vonche kwa njila yopemphela, kupempa ndi kuyamikila ndi chifuno chanu chijiwikane kwa Mulungu. 7 Basi mtendele wa ambuye uli waukulu kupitilila kujiwa konche, siupenyelele umoyo ndi maganizo yanu kwa mtandizo wa Kristo Yesu. 8 Potelapake, achaabale wanga, viganizileni kupunda vinthu vonche vili vauzene, ulemu, haki, ubwino, yali ndi ulemu, pamoji ndi yaja yafunika kuyekeledwa. 9 Vichiteni vinthu vonche ivomwajiyaluza, ivomwajilandila ivomwavivela ndi vija mwaviona kwanga ndi io atate watu amtendele sakale namwe. 10 Nilinacho chisangalalo chachikulu kupunda pakati panu kupitila ambuye pakuti anyaimwe mulangizancho ganizo kwanu pakati pa kujilovya kwanu pakati pa chifuna changa. Kwa chazene, panepo poyamba mudakumbila kunitangatila kwa chifuno changa atangati simudapate malo yonitangatila. 11 Sinikamba chimwecho kuti nijipatile chinthu kwa chifuno changa. Pakuti najiyaluza kugwamika katika hali zonche. 12 Nijiwa kukala katika hali yachepekela ndi hali yokala ndi vambili. Katika madela yonche ya ine najiyaluza chisisi cha mtundu obwela nyengo yokuta ndi nyengo ya njala yani vambili ndi kukala ofuna. 13 Nikoza kuvichita ivi kwa kutangatilishwa ndi iye wanitila mphavu. 14 Ata chimwecho, mudachita bwino kugwilizana na nane pakati pa masauko yanga. 15 Anyaimwe Afilipi mujiwa kuti chiyambo cha mau la Mulungu yapo nidachoka Kumakedonia, palibe kanisa ilo lidanikozecha katika vinthu ivovifunika kuchocha ndi kulandila ingakale anyaimwe mweka. 16 Ata yaponidali Kuthesalonike, anyaimwe mudanitumila mtandizo kwa mbili kwa chifuko cho vojifuni vanga. 17 Msaganiza kuti nifuna mtandizo, nampho nikamba kuti mpate vipacho vipeleka pindu kwanu. 18 Nalandika vinthu vonche, ndi chipano najazidwa ndi vinthu vambili. Nalandila vinthu vanu kuchokela kwa Pafrodito. Ndi vabwino vene vonunkila ngati manukato vene kuvomeleka, vonche ndi nchembe iyo imkwadilicha Mulungu. 19 Kwa ndande imeneyo, Mulungu wanga siwakuongezeleni chifuno chanu kwa ulemelelo wa ufulu wake katika Kristo Yesu. 20 Chipano kwa Mulungu ndi atate wanga ukale ufulu wa muyaya ndi muyaya. Amina. 21 Moni zimfikile kila muumini katika Kristo Yesu. Okondedwa nilinamwepane akulonjelani. 22 Ndi waumini onche pano nikulonjelani hasa anyiwaja wana Akaisari. 23 Chipano nema ya ambuye watu Yesu Kristo ikale ndi mizimu yanu.