Mpambo 2

1 Ngati kulikutilidwa mtima mkati mwa Kristo. Ngati kulichikondi mkati mwake. Ngati kuli chigwilizano cha Mzimu Oyela. Ngati kulikwelekelela ndi lisungu. 2 Chikwanicheni chisangalalo changa pa ganizo limoji mkakala ndi chikondi chimoji, mkala amoji mkati mwa mzimu ndi kukala ndi ganizo limoji. 3 Msachita mweka ndi dama. Ikapanda kwa kujichicha ndi kwaona wina abwino kupunda kuposa anyaimwe. 4 Kila mnaoji wanu wasajipenye iyepe ndi mafuno yake yokha, nampho waone mafuno ya wina kuti ndi ya bwino. 5 Mkale ndi ganizo ngati walinayo Kikristo Yesu. 6 Ingakale iye ngati Mulungu. Nampho siwada jisamale kukhala ngati Mulungu ndi chinthu chakugwilana nacho. 7 Pambuyo pake wadajichicha mwene. Wadatenga chifani cha mtumiki. Ndi kuoneka ngati wanthu,wadaoneka munthu. 8 Iye wadajichicha ndi kukala ovecha mbaka na kufa, nyita yapamtanda. 9 Ndipo Mulungu adamkweza kwa mbili. Adampacha jina la likulu kupitilila yonche. 10 Wadachitha chimwechi mjina la Yesu kuti bombono lalilonchele likwatame. Mabombono ya alikumwamba ndi alipamwamba pa dothi ndi ali panchi pa dothi. 11 Ndi wadachita chimwechi kuthi lilime lalilo nchelo livomele kuthi Yesu Kristo kutti nde Bwana , pa chilemelelo cha Mulungu atate. 12 Kwaicho, okondedwa wanga ngathi umomdalemekeza siku zonche, osathi ndande ya kukalapo ine nampho nyengo ino wapitilila ingakale ine ndi sakalapo, fumani uombole wanu mwa achinawene kwa mantha ndi kutenthemela. 13 Pakuti Mulungu wachitha nchitho mkati mwanu ili wakoze kuganiza ndi kuchitha vinthu vijha vakumkadwilicha iye. 14 Chitani vinthu vonche popanda kudanda ulidwa ndi mtafu. 15 Mchite chimwecho kuthi msadadandaulidwa ndi kukala ndi wana a Mulungu okulupa lila ndi opande kudandaulidwa. 16 Gwilani kupunda mau la umoyo ndande ndikale ndi ndande yoelekela siku la Kristo. Ndipo kuthi sindijiwa kuti sindida thamange chajhe sindidavutika chaje. 17 Ata ngathi ndi pungulidwa ngathi nchembe pamwamba pa golde ndi nchitho yachikulupi chanu, ndikondwa, ndi anyaimwe onche. 18 Nampho namwe mkondwe, ndi mkondwe pamoji ndi ine. 19 Nampho ndikulupilila mkati mwa ambuye Yesu kumuthuma Timotheo kwanu pafupi yapa, kuti ndikoze kuthilidwa mtima yaposindizijwe nkhani zanu. 20 Pakuthi ndilije mwina wakapenyedwe ngati kake, waganizo la uzene kwa ndande zanu. 21 Wina onche ndidakakoza kwa apeleka kwanu ali ndi vochita vao achinawene pe, ndi osati vinthu va Yesu Kristo. 22 Nampho mujiwa mate yake, ndande ngati mwana umowatumikila atatawake, nde umo wadatumika pamoji ndiine pakupeleka mau la Mulungu. 23 Kwaicho ndi mtuma msanga nyengo yapo sindijiwe chiyani sichindionekele ine. 24 Nampho ndikulupilila mkati mwa ambuye kuti ine namwene kuja pafupi yapa. 25 Nampho ndiganiza kubweza kwanu Epafrodito. Iye ndi mmbale wanga ndi w nchito mnjanga, mtenga ndi mtumiki wanu kwa ndande yanga. 26 Pakuti wadali ndi manta ndi wamakumbila kukala nda anyaimwe mwaonche, pakuti mudavel kuti wadali odwala. 27 Nde kuti wadaliodwala kupunda pafupi kumwalila, nampho Mulungu wadamlengela lisungu ndi ubwino umeneo siudali pamwamba paifepe, nampho udali pamwamba panga, kuti ndisakala ndi chisoni pamwamba pa chisoni. 28 Kwa icho ndimbweza msanga kwanu. Kuti yaposimdamuonenche, mkale osangalala pamoji ndi ine sindikale ndachoche dwela mantha. 29 Mtanileni Epafrodito mkati mwa mabuye kwa chisangalalo chonche. Alemekezani wanthu ngati iye. 30 Kwa ndande ya nchito ya ambuye kuti wadali pafupi kumwalila. wadaluswi cha umoyo wake ndande yakuniombola pa kunithangalila ine pakuti muli pathali ndi ine.