Mpambo 1

1 Paulo ndi Timotheo, atumiki a Kristo Yesu kwa waja adapatulidwa mwa Kristo akala Kufilipi, pamoji ndi apenyelela ndi madikani. 2 Lisungu ndi mtendele kuchoka kwa Mulungu atate watu ndi ambuye watu Yesu Kristo. 3 Nimuyamika Mulungu wanga ujapo nikuku mbukilani mwaonche. 4 Nyengo zonche pemphelalanga chifukwa chanu mwaonche nikondwela yapo nikupemphelani. 5 Nili ndi mayamiko yambili chifukwa cha mgwilizano wanu mwa mau ya Mulungu Chiyambile siku loyamba mpaka lelo. 6 Nikulupilila kuti iye wadanyambika nchito ya bwino ya bwino mkati mwanu siwaendekele kuisiliza mbaka siku ya ambuye Yesu Kristo. 7 Ni bwino kwa ine kujivela chimwechi kwanu mwaonche ndande nakuikani mumtima mwanga ndande anyiiimwe mwakala ogwili zana ndiine Mulisungu pa kamangidwa kwanga ndi utetezi wanga wa mau la Mulungu. 8 Mulungu ndi mboni wanga umo ndili ndi kumbilo kwanu mwa mkati wa chikondi cha ambuye Kristo Yesu. 9 Ndi nimpempha kuti chikondi chanu chikuluke kupunda mwa malango ndi njelu zonche. 10 Nipempha kwa ichi mukale ndi ukozelelo woyesela ndi kusankha vinthu vili vabwino kupunda nikupemphelani mukale woyela popanda mlandu ulionche pa siku ya Kristo. 11 Nampho mjalichidwe ndi chipacho cha matechi pezeka mwa Yesu Kristo kwa kuyela ndi uelekelo wa Mulungu. 12 Chipano abale wanga ndifuna mjiwe kuti vinthu vichokela kwanga vichita mau la Mulungu liendekele kupunda. 13 Nde ndande kumangidwa kwanga mwa Kristo mwajiwika mwa openyelela boma onche ndi kwa kila munthu. 14 Ndi abale ambili mwa ambuye chifuko cha kumangidwa kwenga apeza kumbilo ndi kufuna kulalika mau popande mantha. 15 Wina zene aakamba ambuye Kristo kwa nchanje ndi ndeo ndi wina kwa mtima wabwino. 16 Yao amkamba Kristo mwa mtima wa bwino ajiwa kuti naikidwa pano ndande yoteteza mau la Mulungu. 17 Wina amkamba Kristo mojipatula ndi mtima oipa aganiza kuti andipelekela mavuto mwa maluzi yangu. 18 Kwa icho siniopa, ikale njila yoipa kapena ya zene Kristo walalikidwa mwa ichi nikodwa yetu sinikondwe. 19 Ndande nijiwa kuti ichi sichipeleke kumasulidwa kwanga ichi sichipezeke ndande ya mapemphelo yanu ndi mtandizo wa Mzimu wa Yesu Kristo. 20 Mwa chikulupi changa cha zene ndikuti sinidaona nchoni pamalo pake mwa mphavu zonche ngati siku zonche ndi chapano mkulupilila kuti Kristo siwakwezedwe mwatupi langa ingakalemwa umoyo kapena mwa nyifa. 21 Mate kwa ine kukala ndi Kristo ndi kufa ndi pindu. 22 Nampho ngati kukala kwa tupi m'bale chipacho mwa nchito yanga mwa icho sinijiwa ndi chili chosanka. 23 Mate nditutuzidwa kupunda ndi maganizo yawili yaya, nili ndi kumbilo la kulisia tupi ndi kukala pamoji ndi Kristo, chinthu cha mtengo wa ukulu. 24 Ingakale kukala ndi tupili ni chinthu cha mate kupunda kwanu. 25 Ndande nijiwa sinikalile ndi kuendekela pamoji ndi anyiimwe mwaonche mwachitu kuko ndi kondwelo la chikulupi chanu. 26 Ndi ichi sichibwelese chikondwelo chanu ncha chikulu mwa Kristo Yesu, ndande yanga siichulundande yokalapo kwangancho pamoji na mwe. 27 Mfunika kukala ukalo wanu mwa maendedwe yofunika mu mau amlungu, chitani chimwecho kuti nikaja nikukuonani pina ngati sini kuonani nivele mwaina chiimile mwa Mzimu umoji ni mpikisanila chikulupi cha mau a Mulungu kwa pamoji. 28 Msaofyedwa ndi chilichonche chichitidwa na adani wanu, kai nijiwa ndi chilangizi cho wanangika nampho kwanu ni chilangizi cha upulumusi kuchoka kwa Mulungu. 29 Anyiimwe mwapachidwa kwa ndande ya Kristo osati ndande yo mkulupalila koma ndi kuvutichidwa mwa iye. 30 Pakuti muli ndi mguzano umweuja ngati mdauona kwanga ndi mvela kuti nikali nao mbaka chipano.