1 Baada ya vinthu vimenevo Yesu wadajilangizancho kwa opuzila pakati pa nyanja ya Tiberia, mchimwecho ndeumo wadajilangiza mwene. 2 Simoni Petro wadali pamonchi ndi Thomaso wadanidwa Didimasi, Nathanieli wa Kana ya Galilaya wana a Zebedayo ndi opuzila wina awili a Yesu. 3 Simoni Petro wadakambila, "ine nipita kuvua nchomba. Nao adamkambila, "ife nafe situpite ndi iwe." Adapita ndi kulowa mpati nampho usiku umeneo wonche siadapate chalichonche. 4 Ndi umawa yapo kudacha, Yesu wadaima mphepete, Nao opuzila siadajiwe kuti wadali Yesu. 5 Ndeyapo Yesu wadaakambila, "anyamata mli ndi chalichonche chakudya?" Nao adajibu, "palibe." 6 Wadaakambila, "nchichani chilopa bendeka la kwene la bwato, namwe simpate kidogo." Kwaiyo adachicha chilepa naoncho siadakhoze kuguzancho ndande ya kuchuluka kwa nchomba. 7 Basi yuncha opuzila ambayo Yesu wamkonda wamkambila Petro, "Ndi Ambuye." Naye Simoni Patro yapo wadavela kuti ndi Ambuye, wadajimanga nchalu yake (pakuti siwadalivale bwino), ndeyapo wadajitaya myancha. 8 Anyiwancha opuzila wina adancha m'bwato (pakuti siadali patari ndi pamtunda, idali mikwamba mia mancha kuchoka mphepete). Nao amagula vincha vilepa vidanchala nchomba. 9 Yapo adafika mphepete, adaona mata wa makala pancha ndi pamwamba pake padali ndi nchamba pamonchi ndi mkate. 10 Yesu wadaakambila, "jina lani baadhi ya nchomba ilo mwavua saino." 11 Ndeyapo Simoni Petro wadakwela ndi kuguguza chicha chilepa chidanchala nchomba zazikulu, kiasi cha nchomba 153, japozidali zambili, chincha chilepa sichidang'ambike. 12 Yesu wadaakambila, "manchani mpate chamasula kukamwa. Palibe ata mmonchi wa apuzila wadaesa kumfuncha, "iwe ndi yani?" Adachiwa kuti wadali mbuye. 13 Yesu wadancha, wadatenga uncha mkate, nde wadaninkha, wadachita mchimwecho ndi kwa zincha nchomba. 14 Imeneyo idali mala ya katatu kwa Yesu kujilangiza kwa opuzila wake baada ya kuhyuka kuchoka kwa akufa. 15 Baada ya kumasula kukamwa, Yesu wadamkambila Simoni Petro, "Simoni mwana wa Yohana powa, unikandaine kuliko anyiyawa?" Petro wadanchibu, "etu Ambuye imwe mnchiwa kuti ndi kondani." Yesu wadamkambila, "uwesa mbelele zanga." 16 Wadamkambila mala ya kawili, "Simoni mwana wa Yona, Bwa, unikonda?" Petro wadamkambila, etu, Ambuye, imwe munchiwa kuti ndikukondani. Yesu wadamkambila, "Wesa mbelele zanga." 17 Wadamkambilancho mala ya katatu, "Simoni, mwana wa Yona, Bwa, unikonda?" Naye Petro wadadandaula kwa muncha wadamkambila mala ya katatu, "Bwa iwe unikonda?" Naye wamkambila, "Ambuye, mnchiwa yonche, ndi mnchiwa kuti ndikukondani." Yesu wadamkambila, dyecha mbelele zanga. 18 Uzene, uzene, ndikukambila, yapo udali mnyamata udazowelela kuvala nchalu wamwene ndi kupita kwalikonche uko udauna; Nampho yapo siukhale mdala siunyoshe mancha yako, ndi mwina siwakuveke nchalu ndi kukupeleka ukosiuuna kupita. 19 Yesu wadakamba yameneyo ili kulangiza ndi mtundu uti wakufa ambao Petro wadakamyamikila Mulungu. Baada ya kukamba yameneyo, wadamkambila Petro, "Ndichate." 20 Petro wadang'anamuka ndi kumwona yuncha opuzila ambayo Yesu wadamkonda wadaachata - Uyu nde uyo wada nchigoneka pa chifua cha Yesu nyengo ya chakudya cha ujulo ndi adamfuncha, "Ambuye, ndi yani siwakuukileni?" 21 Petro wadamwona ndeyapo wadamfuncha Yesu, "Ambuye, uyu munthu siwachite chiyani?" 22 Yesu wadajibu, "ngati nifuna wabaki mpaka yaposindinche, limenelo likuhusu chiyani?" Ndichate. 23 Kwa hiyo mau yameneyo yadaenea mkati mwa anyiwancha abalo, kuti opuzila mmeneyo siwafa. Nampho Yesu siwadamkambile Petro kuti, opuzila mmeneyo siwafa, "ngati ndifuna iye wabaki mpaka yaposininche ya kuhusu chiyani?" 24 Uyunde opuzila wanchocha ushuda wa vinthu hivi, ndi ndaiye walemba vinthu hivi, ndi tujhiwa kuti ushuhuda wake ndi uzene. 25 Kuli vinthu vina vambili ivo Yesu wadachita ngati kila limonchi lidakalembedwa, ndiganizila kuti jhiko lonche sidakatosha kuviika kalakala ambavo vidakalembedwa.