1 Paulo, kapolo wa Kristo Yesupachikondi cha Mulungu, ndi Timotheo m'bale wathu. 2 Kwa opemphela ndi abale okulupalila mkati mwa Kristo ali Kukolosai. Neema ikale kwanu ndi mitendele kwa Mulungu atate wathu. 3 Tuyamikila Mulungu, tate wa ambuye Yesu Kristo, ndikupemphelani nyengo zonche. 4 Tavela chikulupi chanu mkati mwa Yesu Kristo, ndi chikondi muli nacho anyiwaja onche asankhidwa kwa ndande ya Mulungu. 5 Muli ndichikondi ichi kisa ndande ya chiembekezo cha uzene icho chidaikidwa kumwamba kwa ndande zanu, Muda vela pakati pa chiembekezo icho cha uzene pakati pa mau la uzene la Mulungu. 6 Iyo yaja kwanu, mau la Mulungu ili, libala vipacho ndi kuenela pa jhiko lonche. Yakala yochita chimwechi mkati mwanu chivambile paja mudavela ndi kujiyaluza pakati pa neema ya Mulungu mkati mwa uzene. 7 Ili nde mau la Mulungu ilo mwajiyaluza kuchokela kwa Epafra, okondendwa wanthu kapolo mnyathu, iyeyo nde kapolo wa chikulupi wa Kristo pambuyo pathu. 8 Epafra wachita chikondi chanu chijiwike kwaife. 9 Kwa ndande ya chikondi ichi, chiyambile sikutudavelaizi, tudasiye kukupemphelani. Takala opemphela kuti mkale ndi malango ya chikondi chake cha ulemu woncha wa mumtima. 10 Takala opemphela kuti mkoze kwendandi pamvu za ambuye mnjila zokadwa takala opemphela kuti simbale vipacho kwa pochita chabwino nde kuti simkale mkati mwa malango ya Mulungu. 11 Tupempha kuti mkoze kutilidwa pamvu pa kujikoza kulingana ndi pamvu za ufumu wake pakati pakuvumilia. 12 Tukupemphani kuti, kwa chisangalalo simuyamike kwa atate yao akuchetani anyaimwe mkoze kukala osidilwa okulupalila. 13 Watilamicha kuchokela kulamulo la kumdima ndi kutifikiza pa ufumu wa mwana wake okondedwa. 14 Mkati mwa mwanayo twaomboledwa, ndi kukululikilidwa chimo. 15 Mwana ngati uyo siwaoneka. Ndimbadwa oyamba kwa okonjedwa 16 onche.Pakuti kwa iye vinthu vonche vidakonjedwa, ivo vili kumwamba ndi ivo vili pajhiko, vinthu ivo vioneka ndi vosa oneke. Ikakala ndi va nyengo kapena lamulo kapena la mulo kapena alindi pamvu, vinthu vonche vapangidwa ndi iyeyo ndi kwa ndande yake. 17 Iyeyo wadalipo pambuyo pa vinthu vonche vagwilina pamoji. 18 Iyeyo nde munthu wa tupi kuti iyendi nyumba ya mapemphelo, iye ndiyoyamba ndi mbadwa oyambila kuchoka kwa akuta, kwa icho walindimalo yoyamba mkati mwa vinthu vonche. 19 Pakuti Mulungu wadakondwa kuti kukwanila kwake kukale mkati mwake, 20 ndi kuvanichana vinthu vonche kwa iye kwa njila ya mwana wakeyo. Mulungu wadachita mtendele kwa njila ya mwazi pa mtanda wake. Mulungu wadavanichana vinthu vonche kwa iye mwene, ingakale vinthu va pajhiko kapena vinthu va kumwamba. 21 Namwecho panyengo imoji mudali alendo kwa Mulungu ndi mdali osavane wake pa njelu ndi vocheta voipa. 22 Nampho chipano akugwilizaneni anyaimwe kwa tupi lake kupitila nyifa. Wadachita chimwechi kukubwezani kuti mkale oyela, osadandaulidwe ndi popande kuipa pachogolo pake. 23 Ngati simwendekele chikulupi choima ndi kukalacha uzene, Popande kuchochedwa kutali kuchoka pachipenyelelo choima ndi pamphelo ilo mwalivela ili nde mau ilo lida lengezedwa, kwa kila munthu uyo wadapanyidwa kwa kila munthu uyo wadapangidwa pa jhiko. Ili nde mau paine Paulo, ndakala otumika kapolo. 24 Chipano ndi kontwla mavuto yanga chifuko chanu. Nane nikwaniliza patupi langa chopelewela pa mavuto ya Kikristo, chifuko cha tupi lake, kuti nde nyumba ya Mulungu. 25 Ine ndi kapolo wa nyumba mo ya Mulungu, sawasawa ndi nchito ndidapachidwa kuchokela kwa Mulungu chifuko chanu kuika kwa mbili mau la Mulungu. 26 Uwu nde uzene obisika uwo udali wa bisika pa viaka vambili kwa vibadwa. Nampho nyengo imo wamasukila kwa onche okulupalila Mulungu. 27 Ndi anyiwaja Mulungu wadafuna kuvunukula umo kuli ndi ulemelelo chisili cha uzene mkati mwa jhiko. Ndekuti Kristo wali mkati mwanu nde ulemelelo uwo ukuja. 28 Utu nde uyo tumlengeza. Tukumuyaluza munthu kwa njelu zonche, ili tumpleke munthu oyela mkati mwa Kristo. 29 Pa ndande iyi ine ndilimbikila kuchoka na ndi pamvu yakeyo igwila nchito mkati mwanga.