Mutu 97

1 Yehova alamulila; lekani ziko yapansi ikondwele; visumbu vambili vikondwele. 2 Makumbi na mudima vimuzunguluka. Kululungama na chiweluzo chabwino ndiye maziko ya mupando wake wachifumu. 3 Mulilo upita pasogolo pake na kunyekesa badani bake pambali ponse. 4 mphezi zake ziunikila ziko yapansi; ziko yapansi iona nakunjenjema. 5 Mapili yasungunuka monga sela pamenso pa Yehova, Ambuye wa ziko yonse yapansi. 6 Mulengalenga ukambilila chilungamo chake, ndipo mitundu yonse yaona ulemelelo wake. 7 Bonse balambila mafano yosema bazachita manyazi, bamene bazitamandila ma mafano yalibe kantu- bamugwadila eve, milungu yonse! 8 Ziyoni ananvela nakukondwela, ndipo minzi ya Yuda inakondwela chifukwa cha malemba yanu yolungama, Yehova. 9 Pakuti imwe, Yehova, ndimwe wamumwambamwamba pa ziko yonse yapansi. Mwakwezekewa kupita milungu yonse. 10 Imwe bamene mukonda Yehova, nakuzonda voipa! Amateteza moyo ya bokulupilika, ndipo amabachosa mumanja ya boipa. 11 Kuunika kumafesedwa kuli bolungama na chisangalalo kuli bamene ba mitima yazona. 12 Kondwelani muli Yehova, bolungama imwe; ndipo tokozani pamene mukumbukila chiyelo chake.