1 Salimo ya Davide. mvelani pempelo yanga, Yehova; mvelani kupapata kwanga. Chifukwa cho kukulupilika kwanu na chilungamo chanu, niyankeni! 2 Musangene muchiweluzo na kapolo wanu, pakuti pamenso panu palibe wolungama. 3 Mudani akonka moyo wanga; anishanyaulila pansi; Aninkazika mumudima monga bantu bamene banafa kudaladala. 4 Muzimu wanga wakomoka mukati mwanga; mutima wanga wavutika mukati. 5 Nikumbukila masiku yakudala; Niganizila ntchito zanu zonse; Nimaganizila pavamene mwakwanilisa. 6 Natambasula manja yanga kuli imwe; umoyo wanga umvela njota ya imwe mziko yo yuma. Selah 7 Niyankeni msanga, Yehova, pakuti mzimu wanga wakomoka. Musabise nkope yanu, kuti nisankale monga bantu bogwela mu chimugodi. 8 Nimvele pangano yanu yokulupilika kuseni. pakuti nikulupilila muli imwe. Nnilangizeni njila yakuti niyendelmo, pakuti ndikwezeka umoyo wanga kuli imwe. 9 Nipulumuseni kubadani banga,Yehova; Nitabila kuli imwe kubisama. 10 Nipunzseni kuchita chifunilo chanu, pakuti imwe ndimwe Mulungu wanga. Mzimu wanu wabwino unisogolele mziko yachilungamo. 11 Yehova, chifukwa cha zina yanu, munisunge na moyo; mu chilungamo chanu muchose umoyo wanga mumavuto. 12 Muchipangano chanu chosani badani banga ndipo muwononge badani bonse ba umoyo wanga, pakuti ine ndine mtumiki wanu.