Mutu 108

1 Mutima wanga wankazikika, Mulungu! Niza imba, inde, niza imba zolemekeza na ulemelelo wanga onse 2 Ukani, lute na harp; Niza ushe mubanda kucha. 3 Niza ku yamikani, Yehova, pakati pa mitundu ya bantu; Nizaku imbilani zolemekeza pakati pa mitundu. 4 Pakuti chikulupililo chanu ni chacikulu pamwamba pa miyamba; ndipo kukulupilika kwanu Kufikila kutambo. 5 Kwezekani, Mulungu, kumwamba pa miyamba, ndipo ulemelelo wanu ukwezeke pa ziko yonse yapansi. 6 Kuti bamene mukonda bapulumusiwe, tipulumuseni na kwanja yanu yamanja naku niyanka ine. 7 Mulungu akamba mukuyelo kwake;" Niza sangalala; Niza gaba Sekemu na ku gaba chigwa cha Sukoti. 8 Giliyadi ni yanga, Manase ni yanga, Efuraimu ni chisota changa, Yuda ni ndodo yanga yacifumu. 9 Moabu ndiye chowashilamo changa; pa Edomu niza ponya nsapato yanga; Niza punda mo sangalala chifukwa ca Afilisiti. 10 Ndani azani ngenesa mu munzi olimba? Ndani azaninpeleka ku Edomu?. 11 Mulungu, kodi simuna tikane ise? Simu pita ku nkondo na gulu yatu ya nkondo. 12 Titandizeni pa mudani watu, pakuti tandizo ya muntu ni yopanda pake. 13 Tiza pambana na chitandizo cha Mulungu; aza pondeleza badani batu.