Mutu 104

1 Nizalemekeza Yehova na moyo wanga wonse, Yehova Mulungu wanga, ndimwe bakulu; mwavaliwa ulemerero na ukulu. 2 Mumaziphimba na kuwala monga chovala; munayala kumwamba monga nsalu yochinga. 3 Mumayalila zipinda zanu mu makumbi; mupanga makumbi galeta yako; mumayenda pa mapiko a mphepo. 4 Apanga mphepo mutumiki wake, malawi yamoto ya kapolo wake. 5 Anakazikisa maziko ya ziko yapansi, ndipo silizagwedezeka ku ntawi zonse. 6 Munaphimba ziko yapansi na manzi monga chovala; manzi anaphimba mapili. 7 Kuzuzula kwanu kunaphwanyisa manzi; pa kunveka kwa ya mabingu anu banataba. 8 Mapili anakwela ndipo zigwa zinasikila kumalo kwamene munawaikila. 9 Munawaikila malile kuti basaoloke; sibazaphimba ziko yapansi. 10 Anachitisa kasupe kuyenda muzigwa; misinje kuyenda pakati pa mapili. 11 Amatila manzi nyama zonse za munsanga; ma kavalo bamunsanga yasiliza chilaka chao. 12 Mumpepete mwa misinje tunyoni tumanga zisa zawo; zimayimba pakati pa ntambi. 13 Amwesa mapili kuchokela muzipinda zake zamazi zakumwamba. ziko yapansi yazaza na zipaso za nchito yake. 14 Amamelesa musipu wa ng’ombe, na zomela zoti bantu bazimele, kuti muntu babeleke chakudya muntaka. 15 Amapanga vinyo kuti bakondwelese muntu, mafuta opangisa nkope yake kuwala, na chakudya chochilikiza moyo wake. 16 Mitengo ya Yehova ipeza mvula yambili; mikunguza ya ku Lebanoni yamene anashanga. 17 Tunyoni tumanga zisa zawo. Dokowe apanga mutengo wa mukuyu nyumba yake; 18 Mbuzi zamunsanga zimankala pamapili yatali; pamwamba pa mapili ndiye potabilako mbila. 19 Anaika mwezi kuzindikisa nyengo; zuba limaziba ntawi yake yakulowa. 20 Mumachitisa mudima wausiku pamene zilombo zonse za munsanga zimatuluka. 21 Mikango ikubangula nyama, nakufunafuna cakudya cao kuli Mulungu. 22 Pamene zuba inyamuka, zimabwelela mumbuyo nakugona mumapanga yawo. 23 Pakali pano, bantu bamapita ku nchito zawo na kugwila nchito mpaka mazulo. 24 Yehova, nchito zanu nizochuluka! Munazipanga zonse na nzelu; ziko yapansi izasefukila na nchito zanu. 25 Kumeneko kuli nyanja yakuya ndi yotakata, yozala na zolengewa zosabelengeka, zing'ono nazikulu . 26 Zombo zimayenda kwamene, ndipo Leviathan aliko, wamene munapanga kuti azisewela munyanja. 27 Zonse izi ziyangana kuli imwe kuti muzipase chakudya chawo pa ntawi yake. 28 Mukabapasa, bamasonkanisa; posegula kwanja yanu, zikuta. 29 Mukabisa nkope yanu, zizunzika; mukachosa mpweya yao, bamafa nakubwelela kufumbi. 30 Pamene mutumiza muzimu wanu, zilengewa, ndipo mukonzanso kuminzi. 31 Lekani ulemelelo wa Yehova ankale kwamuyayaya; Yehova akodwela na volenga vaka. 32 Amayangana pa ziko ya pansi, ndipo injenjema; amagwila mapili, ndipo bankala na chusi 33 Nizayimbila Yehova moyo wanga wonse; nizayimbila zolemekeza Mulungu wanga masiku yonse ya moyo wanga. 34 Malingalilo yanga ankale okoma kuli eve; Nizakondwela muli Yehova. 35 Bochimwa awonongeke paziko yapansi, ndipo boipa asankalepo. Nimatamanda Yehova na moyo wanga wonse. Tamandani Yehova.