Mutu 1

1 Ici ndiye ciyambi ca nkani yabwino ya Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu. 2 Monga vinalembewa na Mneneri Yesaya," Onani nituma Kapaso wanga pamenso panu, wamene azakonza njila yanu. 3 Mau ya uyo opunda msanga, 'Konzani njira ya Ambuye; mupangileni njila ilibe makona." 4 Yohane anabwera, nakubatiza msanga nolalikila za ubatizo olapa paku khululukidwa kwa macimo. 5 Ziko yonse ya Yudeya na anthu onse aku Yerusalemu anayenda kuli yeve. Anabatiziwa na eve mumana wa Yolodani, nakuvomela macimo yawo. 6 Yohane anzovala zovala zausako wa ngamila na beluti ya cikumba mumsana mwake, ndipo anali kudya nthete na uchi wamusanga. 7 Analalikila, "Winangu alikubwela pambuyo panga wamene ali wamphavu kupambana ine, ndipo sindiyenela kubelama kumangusula ntambo yansapato zake. 8 Ine nikubatizani na manzi, koma iye azakubatizani imwe na Mzimu Woyela." 9 Vinacitika ivi mumasiku aja pamene Yesu acacokera ku Nazalete mu Galileya, ndipo anabatiziwa na Yohane m'mumana wa Yolodani. 10 Pamene Yesu anacoka mumanzi, anaona kumwamba kwa seguka na Mzimu ulikuseluka mowoneka ngati kunda. 11 Na mau anacokela kumwamba nati, "Ndiwe mwana wanga wenikonda. Ndi kondwela nawe." 12 Ndipo Mzimu unampeleka yeve kuyenda kusanga. 13 Enze msanga kwa masiku 40, kuyesewa na satana. Anali na nyama za msanga, na Angelo kumtumikila eve. 14 Manje pamene Yohane anamangiwa, Yesu anabwele ku Galileya alikulalikila uthenga wa Mulungu, 15 elo enzokamba ati, "Nthawi yakwana, ndipo ufumu wa Mulungu uli pafupi. Lapani ndipo mkhulupilile mu uthenga." 16 Pamene enzokuyenda mumbali mwa kamana ka Galileya, anaona Simoni na Anduleya mbale wa Simoni alikukuponya kombe muchimana, cifukwa anali ogwira nsomba. 17 Yesu anabauza ati, " Bwelani, nikonkheni, ndipo ndizakupangani ogwira anthu." 18 Ndipo pamene apo anasiya makombe nomukonkha. 19 Pamene Yesu anayendako cabe pang'ono, anaona Yakobo mwana wa Zebediya na Yohane mbale wake; anali muboti alikutunga makombe. 20 Anabaitana ndipo anasiya Atate awo Azebediya na a nchito muboti, nakumukonka. 21 Ndipo anafika ku kapenamu, ndipo pa sabata, Yesu anangena musunagoge nophunzisa. 22 Anadabwa navenzeli kuphunzisa, analikuphunzisila ngati munthu anali na ulamuliro osati nga na alembi. 23 Pamene apo munali munthu musunagoge enze na mizimu yoipa yamene inalila 24 nati, "Nanga tinambali bwanji naiwe, Yesu waku Nazareti? Wabwela kutiononga? Nikuziba iwe. Niwe woyela wa Mulungu!" 25 Yesu anakalipila dimoni nati, " Siya kukamba ndipo coka mwaiye!" 26 mzimu woipa unamgwesa pansi nakucoka mwa iye ulikulila mokuwa. 27 Ndipo anthu wonse anadabwa, ndipo anafunsana wina ndi muzake, " Nanga ici nicani? Ciphunziso casopano cina ulamulilo? Alamulila na mizimu yoipa ndipo imumvelela!" 28 Mbili yake inamveka pali ponse mumzinda wonse wa ku Galileya. 29 Pamene anacoka musunagoge, anangena munyumba ya Simoni na Andeleya pamodzi na Yakobo na Yohane. 30 Manje apongozi a Simoni enze gone odwala mphepo, anamuuza Yesu za iye. 31 Ndipo Yesu anabwela, anamugwila pa kwanja , nakumunyamula; mphepo inacoka, ndipo anayamba kubapasa vakudya. 32 Mazulo mwake, pamene zuba inangene , anabwelesa kwake wonse odwala nabamene enze naviwanda. 33 Muzinda wonse unasonkhana panja pa ciseko. 34 Anacilisa ambiri enze odwala matenda wosiyana-siyana nocosa madimoni ambiri, koma sanavomeleze madimoni kuti yakambe cifukwa yanamuziwa iye. 35 Anauka kuseni-seni, kukali kofipa; anacoka nakuyenda kumalo kwayeka ndipo anapemphela kwamene kuja. 36 Simoni na aja enze naye anamusakira. 37 Anamupeza nakumuuza kuti, "Anthu wonse asakila iwe." 38 Iye anati, "Tiyeni tiyende kwina, kumizinda inangu, kuti nikalalikileko nakweve. Nicifukwa cake nina bwela kuno." 39 Anayenda malo yonse ya Galileya, kulalikila mumasunagoge yawo nakucosa madimoni. 40 Munthu wolwala makate anabwela kwa yeve. Anali kupempha iye; anagwada pansi nakuti, "Ngati mufuna, munganitubise" 41 Yesu anamvela cifundo, nakumugwila nakwanja kwake nati, "Ndifuna, kuyelesewe." 42 Pamene apo makate anacoka iye, ndipo anapola. 43 Yesu anamucenjeza maningi nakumuuza ati ayende 44 Anati kwa yeve, "usayese kuuza munthu aliyense, koma yenda ukazilangize kwa wansembe, ndipo ukapeleke nsembe yakukuyelesela ija yamene analamulila Mose, ngati umboni kwa beve." 45 Koma anayenda nayamba kuuuza aliyense nopeleka nkhani nopangisa kuti Yesu asakwanise kungena momasuka m'muzinda uliwonse. Ndipo anankhala ku malo kunalibe anthu enzonkhalako ndipo anthu anabwela kuli eve kucokela kosiyana-siyana.