Mutu 39

1 Pantawi ija Marduk-baladani mwana wamwana wa balatani mfumu ya Babiloni, anatuma nkalata na mpaso kuli Hezekia; pamene ananvela kuti Hezekia anali wodwala ndipo apola. 2 Hezekia anakondwela pali ivi vintu; analangiza botumikila bake munyumba yosungilamo vamutengo wodula- siliva, golide, tonunkula tumafuti tumafuta, nyumba yosungilamo zida za nkondo, na zonse zezikupezaka nyumba yake. Munalibe munyumba yake, kapena mu unfumu wake, chamene hwezekiah sanabalangize. 3 Pamene apo esaya anabwela kwa mfumu Hezekia namufunsa, ''bushe aba bamuna bakamba chani kuli iwe? nanga bachokela kuti?'' Hezekia anakamba kuti, ''bachokela patali kuziko la babiloni.'' 4 Esaya anafunsa, '' kodi baona chani munyumba yako?'' Hezekia anayanka, ''baonazonse munyumba yanga. Kulibe chamene sininabalangize chili munyumba yanga.'' 5 Esaya anakamba kuli Hezekia, ''nvela mau a Yehova wamakamu: 6 'Ona, masiku azabwela pamene vintu vonse vili munyumba ya mfumu, zintu zamene makolo anafaka kufikila siku yalelo, vizapelekewa ku babiloni. Kulibe chamene chizasala, akamba Yehova. 7 Bazatenga benangu bamumi bado yako, bamene azasunga, ndipo bazankala bolemekezeka munyumba ya mfumu wa Babiloni.''' 8 Ndipo Hezekia anakamba kuli Esaya, ''mau ya Yehova yamene wakamba niyabwino.'' Chifukwa anaganiza monga, ''kuzankala mutendele naku nkazikika mumasiku yanga.''