Mutu 12

1 Pa siku ija muzaka kamba, '' Nizakapasa kuyamika kuli iwe, Yehova. Olo unali okalipa naine, kukalipa kwako kwapindamuka, ndipo wanitontoza ine. 2 Onani, mulungu ndiye chipulumuso changa; nizakulupilila siniza yopa, chifukwa Yehova, inde, Yehova ndiye mpanvu zanga na nyimbo yanga. Ankala chipulumuso changa.'' 3 Ndi chisangalalo mudzatunga madzi ku zitsime za chipulumutso. 4 Tsiku lomwelo mudzati, Yamikani Yehova, ndipo itanani pa dzina lake; lengezani zochita zake mwa mitundu ya anthu, lalikirani kuti dzina lake lakwezedwa. 5 Imbirani Yehova, chifukwa wachita zinthu zazikulu; izi zidziwike padziko lonse lapansi. 6 Fuulani mokweza ndi mokondwera, inu okhala m'Ziyoni, pakuti Woyera wa Israyeli ali pakati panu.