1
Ndipo Yehova ana muuza Abrahamu, " Choka muziko yako, nakuli babululu bako, nakuli nyumba yaba tate bako, kumalo yamene ine niza ku langiza iwe.
2
Niza mpanga kuchoka kuli iwe, ziko ikulu, nakukudalisa, naku panga zina lako ikulu, uza nkhala daliso.
3
Niza dalisa abo bamene bakudalisa, koma amene akuetmbela naine niza batembelela. Kupitila muli iwe mabanja yonse yapa chalo baza dalisika."
4
gNdipo Abrahamu anayenda, monga mwamene Yehova ana muuzila, na Loti, anayenda na eve. Abramu analina zaka sevente fiive pamene ana choka mu Haran
5
Abramu anatenga Sarai, mukazi wake, Loti, mwana wa mubale wake, vintu vawo vonse vamene bana peza, pamodzi na bantu bamene banatenga ku Haran. Bana choka nakuyenda ku malo ya Kanani nakufika mu malo ya Kanani.
6
Abramu anapitamo mu malo paka kufika ku Shechem, ku mtengo wa Thundu mu Moreh. Pa nthawi ija Akanani anali nkhunkhala mu malo.
7
Yehova anaonekela kuli Abramu, naku kamba, " Ku bana bobadwa kuli iwe niza pasa malo aya." Ndipo pamene paja Abramu ana manga guwa kuli Yehova wamene anaonekele kuli eve.
8
Kuchokela kuja ana vendela ku phiri yaku ziko yaku mawa mu Betele, kwamene anayika hema yake, na Betele kumazulo na Ai ku mawa. Kuja ana manga guwa ya Yehova nakuyitana pa zina la Yehova.
9
Ndipo Abramu anapitiliza ulendo, kuyenda moyagana ku Negev.
10
Kunali njaa mu dziko, ndipo Abramu anayenda ku Egypito ku nkhala, cifukwa njala ina liyi nkhulu kwambili mu dziko.
11
Pamene anali kugena mu Egypito, ana kamba naye Sarai mukazi wake, " Ona kuno, ni ziba kuti ndiwe muzimai wokongola.
12
Pamene Ai Egypito bakakuona iwe, baza kamba kuti, ' Uyu ndiye mukazi wake,' na kunipaya ine, koma bazakusunga wa moyo.
13
Ukambe kuti ndiwe mulongosi wanga, pakuti vinkhale va bwino pali ine cifukwa ca iwe, na umoyo wanga uzapulumusiwa cifukwa ca iwe."
14
Cina citika kuti pamene Abramu anagena mu Eygpito, AiEygpito anaona kuti Sarai anali wokongola maningi.
15
Pamene bana bamuna ba Farao bana muona, naku mutamanda kuli Farao, naku mupeleka muzimai mu nyumba ya Farao.
16
Cifukwa ca eve, Falao anamucitila va bwino Abramu, ndipo Abramu analandila mbelele na ngombe, abulu amuna, anchito amuna, anchito akazi, abulu akazi na ngamila.
17
Ndipo Yehova ana muvutisa Fsrao na nyumba yake na matenda yakulu cifukwa ca Sarai, mukazi wa Abramu.
18
Farao ana muyitana Abramu, nakukamba, " Nichani camene wacita kuli ine? Cifukwa ni cani sunani uze ine kuti anali mukazi wako?
19
Nicani camene unakambila, 'Nimulongesi wanga,' kuti ni mutenge nkhukhala mukazi wanga? Manje apa, uyu mukazi wako, mutenge, ndipo muyende."
20
Ndipo Farao analamulila kuli banyamata bake za eve, nakumupisha, pamodzi na mukazi wake na vonse vamene enze navo.