Mutu 2

1 Pamenepo pambuyo zaka ndi zina ndinabwelanso ku Yerusalemu pamodzi ndi Baranaba, ndinatengaso Tito kunipelekeza ine. 2 Ine ndinayenda chifukwa chachi bvumbulutso ndiponso nina bauza uthenga wabwino wamene nilikulalikila kwa amitundu. Ine ndinalankhula mwamseri kuli ena amene anali olemekezeka, kuti kapena siningatamange- kapena sinatamange- chopanda phindu. 3 Koma angakhale Tito, amene anali ndi ine, ndiye Giriki, anamukakamiza kuti adulidwe. 4 Abale achiyengo anabwela mwa chisinsi kusuzumira pali ufulu wamene tilinawo mwa Kristu Yesu. Iwo anafunisisa kuti akatichitise ukapolo, 5 koma ife sitinakolola mwa kuzipeleka kuli iwo mu nthawi, kuti choonadi cha uthenga wabwino chingasale na inu. 6 Koma iwo amene anali kuonekela olemekezeka ( chimene iwo anali kale, kulibe kanthu kwa ine, Mulungu samalangiza tsankho)- iwo, ine nakamba, amene analikuoneka olemekezeka sanawonjezele kanthu kalikonse kwa ine. 7 Poyamba mosiyana, iwo anawona kuti ine ndinapatsidwa na uthenga wa bwino kuli iwo amene osadulidwa, monga kwa Petro anapatsidwa uthenga wabwino wa mdulidwe. 8 Pakuti Mulungu anasebenza mwa Petro kumutuma kwa odulidwa, anachitanso mwa ine kundituma kwa amitundu. 9 Pamene Yokobo, Kefa, ndi Yohane, amene anazidikila kumanga mupingo, anamvetsa cisomo chamene ndinapatsidwa ine, iwo anapatsa ine ndi Barnaba dzinja lamanja la ciyanjano. Iwo anachita izi kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa mdulidwe. 10 Iwo anapempa kuti ife tikumbukile wosauka, ichichinthu chamene ine ndinali wofunisisa kuchichita. 11 Koma pamene Kefa anabwela ku Antiokeya, ndinatsutsana naye pamanso pake chifukwa iye anatsutsika wolakwa. 12 Pamanso wina wake anthu anabwela kuchokela kwa Yakobo, Kefa anali kudya ndi amitundu. Koma pamene aba anthu anabwela, iye anasiya ndipo anazipatula kwa amitundu. Iye anakuyopa iwo a ku mdulidwe. 13 Ndipo ayuda otsala anagwilizana mulizi za chinyengo. Ngankhale Barnaba anatengewa na chinyengocha iwo. 14 Koma pamene ine nina wona kuti machitidwe ya iwo sanali kuyenda mu choonadi cha uthenga wabwino, ndi nakamba kwa Kefa pamanso pa onse, " Ngati uli muyuda, koma munkhala monga amitundu ndipo si muyuda, mukangamiza bwanji amitundu kunkhala monga Ayuda?" 15 Ife tekha ndife Ayuda mwa chibadwile ndipo osati amitundu wochimwa; 16 koma ife tiziba kuti munthu sayesedwa wolungama pa nchito ya lamulo koma mwa chikulupililo cha Kristu Yesu. Ife tinabwela mu chikulupililo mwa Kristu Yesu kuti tikayesedwe olungama pa chikulupililo mwa Kristu ndipo osati panchito ya lamulo. Pa nchito ya lamulo kulibe thupi izayesedwa wolungama. 17 Koma ngati, pofuna kuyesedwa olungama mwa Kristu, tipezekanso tili ocimwa, kodi Kristu ama lengeza chimo? Simwamene nditu! 18 Ngati ine namanganso izi zintu zamene ninawononga,ine nazisimikizila ndekha ndine olakwa. 19 Pakuti mwa lamulo, kuti ine ndikhale ndi moyo kwa Mulungu. 20 Ine ndinapacikidwa ndi Kristu. Sindine wamene alina umoyo ai, koma Kristu amene ali ndi moyo mwa ine. Koma moyo umene ndili nao mu thupi ndilinao mu chikulupililo cha Mwana wa Mulungu, amene ana ndikonda ndiponso nakuzipeleka chifukwa cha ine. 21 Ine sinimafaka pambali cisomo ca Mulungu, pakati ngati cilungamo cili mwa lamulo, nditu Kristu anafa pa chabe!