1 Paulo, mutumwi- osati mutumwi ochokela ku munthu kapena kwa munthu nthambi, koma kuli Yesu Kristu ndi Mulungu Ambuye, amene anamuukitsa iye kuchokela kwakufa- 2 ndiponso onse abale ndi ine, ku mipingo wa Galatiya: 3 Chikondi kwa inu ndiponso mutendere ochokela kwa Mulungu ndi Ambuye Yesu Kristu, 4 amene anazipatsa mwinewake chifukwa cha machimo yathu kuti iye anga timasule kuchokela ku chaka choophya, mogwilizana na chikonzekero cha Mulungu ndi Ambuye, 5 kuli iye khala ulemu nthawi ndi nthawi zonse. Ameni. 6 Ine ndi odabwa kuti inu muli ku tembenukira kutali na iye wamene anamitanani pa chikondi cha Kristu. Ine ndi odabwa kuti inu muli kutembenukira ku mau amubaibulo osiyana. 7 Izi sikukamba kuti kuli wina mau amubaibulo, koma kuli ena anthu amene apangitsa inu mavuto ndiponso ali kufuna ku sintha mau amubaibulo ya Kristu. 8 Koma chingakhale ati ife kapena mungelo ochokela kumwamba ayenera ku chula kwa inu mau amubaibolo ena kuposa yamene tinachula kwa inu, lola iye ankhale wotembereredwa. 9 Ngati ife mwamene tinakamba pamaso, panopa ine nakamba kachiwili, " Ngati kuli amene alikuchula kwa inu mau ena kuposa amene inu munalandilila, lola iye ankhale wotembeleledwa." 10 Pakuti kodi ndikopa anthu tsopano, kapena Mulungu? Kodi ndifuna kukoperetsa anthu?Ngati nilikukondweletsa anthu, sinizakakhala wanchito. 11 Pakuti ndikudziwitsani inu, abale, kuti utenga wabwino wolalikila ndi ine suli monga mwa anthu. 12 Ine sininaulandilekuchokela ku munthu, kapena sininaupunzile. Koma una bwela mwa bvumbulutso ya Yesu Kristu kuli ine. 13 Inu munamvela makhalidwe anga kale mwa chiyuda, mwamene ndinali kulondalonda mipingo wa Mulungu kupililila kuyesa ndiponso ine ninali kufuna kuyiononga. 14 Ndipo ndinawaposa ndi kutsogola mwa ciyuda ambiri a msinkhu wanga mwa mtundu wanga, ndipo neze wachangu kwambili ine ku miyambo zama nkolo anga. 15 Koma pamene Mulungu, amene anadipatula kuchokela mu mimba ya amai anga, ndiponso nakuniyitana mu cisomo cake, 16 kuti avumbulutse Mwana wake mwa ine, kuti ndimulalikile iye mwa amitundu, pomwepo sininafufumile kufunnsa thupi ndi magazi. 17 Kapena kuyenda ku Yerusalemu kuli iwo amene anakhla atumwi pamene nikalimbe nkukhala ine. Koma ninayenda ku Arabiya ndipo ndinabwelanso ku Damasiko. 18 Pamenepo panapita zaka zitatu ndinapita ku Yerusalemu kuti nika muzibe Kefa ndiponso ine ninankhala kwa iye masiku khumi ndi asanu. 19 Koma wina wa atumwi sininamuone koma Yakobo, mbale wa Ambuye. 20 Ndipo izi ndimilembelani inu, ine ndimilimbikitsani pamaso pa Mulungu, kuti sininama ine. 21 Pamenepo ndinabwela ku mbali za Suriya ndi Kilikiya. 22 Koma sinaliwozibika ku mipingo ya Yudeya amene alimu Kristu. 23 Koma amalinkumvela chabe kuti, " iye wakutilondalonda ife kale alikulalikila chikulupililo chamene anali chipasula kale." 24 Ndipo analemekeza Mulungu chifukwa chaine.