Mutu 3

3 1 Chilichonse chili na nthawi yake, na nyengo yavintu vonse paziko lapansi. 2 Kuli ntawi yakubadwa na ntawi yakufa, ntawi yobyala na ntawi yakunyula mbeu, v 3 ntawi yaku paya na ntawi yakupolesa, ntawi yakuwononga na ntawi yakumanga. 4 Pali ntawi yolira ndi nthawi yoseka, nthawi yolira ndi nthawi yovina, 5 nthawi yoponya miyala ndi nthawi yosonkhanitsa miyala, nthawi yolandira anthu ena, ndi nthawi yosiya kukumbatira. 6 Kuli ntawi yakufuna vinthu na ntawi yakuleka kufuna vinthu, ntawi yakusunga vinthu na mphindi yakutaya zinthu, 7 mphindi yakung'amba zovala ndi mphindi yakukonza zovala, mphindi yakutonthola ndi nthawi yolankhula . 8 Pali nyengo yakutemwa na nyengo yakudana, nyengo ya nkhondo na nyengo ya mtende. 9 Kodi wogwira ntchito amapindulapo chiyani pantchito yake? 10 Ndawona ntchito yomwe Mulungu wapatsa anthu kuti aimalize. 11 Mulungu adapanga chilichonse kukhala choyenera nthawi yake. Komanso waika zamuyaya m'mitima mwawo. Koma anthu sangathe kumvetsetsa zomwe Mulungu wachita, kuyambira pachiyambi mpaka kumapeto. 12 Ndikudziwa kuti palibenso china chabwino kwa munthu kuti azisangalala ndi kuchita zabwino masiku onse a moyo wake. 13 ndikuti aliyense adye ndi kumwa, ndipo azindikire momwe angasangalalire ndi zabwino zochokera pantchito yake yonse. Iyi ndi mphatso ya Mulungu kwa anthu. 14 Ndikudziwa kuti chilichonse chimene Mulungu amachita chimakhala mpaka muyaya. Palibe chomwe chingawonjezedwe kapena kuchotsedwa, chifukwa ndi Mulungu amene wachita izi kuti anthu amupemphere ndi ulemu. 15 Chilichonse chomwe chinalipo chinalipo kale; chilichonse chomwe chidzakhalepo chinalipo kale. Mulungu amapangitsa anthu kufunafuna zobisika. 16 Ndaona zoipa zimene zili pansi pano, pamene pakuyenera kuweruzidwa, ndipo m'malo mwa chilungamo, zoipa zinali pomwepo. 17 Ndinati mumtima mwanga, "Mulungu adzaweruza olungama ndi oipa pa nthawi yoyenera pa nkhani iliyonse ndi zochita zonse." 18 Ndinati mumtima mwanga, "Mulungu amayesa anthu kuti awawonetse kuti ali ngati nyama." 19 Tsoka la ana a anthu ndi tsogolo la nyama ndi chimodzimodzi. Imfa ya m'modzi ili ngati imfa ya mnzake. Mpweyawo ndi wofanana ndi onsewo. Palibe mwayi kwa anthu kuposa zinyama. 20 Zonse ndi zopanda pake. Chilichonse chikupita kumalo omwewo. Chilichonse chimachokera kufumbi, ndipo chilichonse chimabwerera kufumbi. 21 Ndani akudziwa ngati mzimu wa anthu upita kumwamba ndipo mzimu wa nyama umatsikira pansi? 22 Chifukwa chake ndidazindikiranso kuti palibe chabwino kwa munthu koposa kusangalala ndi ntchito yake, chifukwa ndi gawo lake. Ndani angamubweretse kudzawona zomwe zidzachitike pambuyo pake?