Mutu 2

1 Ndipo tinabwelela na kutenga ulendo wathu mu chipululu mu njila yaku nyanja ya Reedis, monga Yehova anakambila kuli ine; tinayenda mozungulila pili ya Seir mu masiku yambili. 2 Yehova anakamba kuli ine, nakuti, 3 'mwayenda muzunguluka ili pili mwantawi itali; pindamukilani ku mumwela. 4 Lamula bantu, kamba, '' Mufunika kupita mumalile yaba bale banu, mubadwe wa Esau, bamene bankala mu Seiri; bazakuyopani. Mwaicho nkalani bochenjela 5 kuti musamenyane nabo, chifukwa sinizakupasani malo yali yonse yao, iyai, osati ngankale kang'ono pamalo yao kodyakapo; chifukwa napasa pili ya Seiri kuli Esau kunkala chintu chake. 6 Muzagula vakudya kuchoka kuli beve na ndalama, kuti mudye; ndiponso muzagulanso manzi kuchoka kuli beve na ndalama, kuti mumwe. 7 Chifukwa Yehova Mulungu wanu akudalisani imwe mu zonse nchito zanu zamanja; Aziba kuyenda kwanu kupita mu chipululu chachikulu. Muli izi zaka zili fote Yehova Mulungu wanu ankala naimwe, ndipo simunasobe kalikonse.''' 8 Ndipo tinapita kuli ba bale bathu, bana ba Esau bamene bankala ku Seir, kutali kuchoka ku museu wa Arabah, kuchoka ku Elath na kuchoka ku Ezion Geber. Ndipo tinapindimuka na kupita ku njila muchipululu cha Moabu. 9 Yehova anakamba kuli ine, ' osati kuvuta Moabu, nakusamenyana nabo mu nkondo. Chifukwa sinazakupasani malo yake kunkala chintu chanu, chifukwa napasa Ar kuli bamubadwe wa Loti, kunkala chitntu chao.' 10 (Ba Emite banali kunkala kuja kudala, monga bantu bakulu, bambili, ndipo batali monga ba Anakimu; 11 aba nabeve bali monga ba Rapaimu, monga ba Anakimu; koma baku Moabu baitaneni ba Emite. 12 Ma Horite nawo banankala mu Seir kale, koma bana ba Esau bana pambana beve. Banabaononga beve kuchoka pasogolo pawo na kunkala mu malo mwawo, monga Israeli anachita ku malo yawo nakunkala noyo yamene Yehova anapasa kuli beve.) 13 Manje nyamuka na kuyenda mumana wamanzi ku Zeredi.' 14 Ndipo tinayenda pamwamba pa Zeredi pochoka manzi. Manje masiku kuchoka pamene tinabwela kuchoka ku Kadeshi Barnea mpaka kuoloka ku mumana wamanzi wa Zeredi, zinali zaka seti-eiti. Inali pali ija ntawi kuti yonse mibadwo ya bamuna bali woyenela kumenya nkondo banayenda kuchoka ku banthu, monga Yehova analumbila kuli beve. 15 Koma, kwanja kwa Yehova kunali kosusana na uja mubadwe kuti abawononge kuchoka ku banthu mpaka bakanayenda. 16 Ndipo chinachitika, pamene bonse bamuna bali oyenela kumenyana banafa na kuyenda kuchoka pakati pa bathu, 17 kuti Yehova anakamba kuli ine, nakuti, 18 Imwe lelo mufunika kupita ku Ar, ku malile ya Moabu. 19 Mukabwela pafupi molanganana na banthu ba Ammon, musabavute beve kapena kumenyana nawo; chifukwa sinizapa imwe yaliyonse malo ba bathu ba Ammoni kunkala nayo; chifukwa naipasa ku bana ba Loti monga kunkala yawo. 20 (Yaja futi yabelengewa kunkala malo yaba Refaimu. Ba Refaimu banali kunkala kuja kudala-koma ba Amori bama baitana zamuzummimu- 21 bantu monga bakulu, bambili, na batali monga Anakimu. Koma Yehova anaba ononga kukalibe ba Ammori, ndipo bana bapyanika nakunkala mu malo yao. 22 Ichi Yehova anachi chita nakuli bantu ba Esau, banali kunkala ku Seiri, pamene ana ononga ba Horite pamene kukalibe beve, na bamubadwe wa Esau banatenga malo kuli beve nakunkala mumalo ya mpaka lelo. 23 Monga kuli ba Avvite banali kunkala mu minzi mpaka kufika ku Gaza, ba kapitorimu, banachokela ku kapito, bana ba ononga nakunkala mu malo yao.) 24 '''' Manje nyamukani, yambamponi na ulendo wanu, nakupita ku chikwa cha baku Anoni; onani, napasa mumanja yanu Sihoni waku Amori, mfumu yaba Heshiboni, na malo yake. Yambani kuyatenga, nakumenyana naye mu nkondo. 25 Lelo nizayamba kuika manta na kuyopa imwe pa bantu bali pansi pa myamba; bazanvela nkani pali imwe na njenjema nakunkala na manta kamba ka imwe.' 26 Ninatuma bopeleka mau kuchokela mu chipululu cha Kademoti mapaka ku Sihoni, mfumu ya Heshiboni, na mau yamutendele, kukamba, 27 ' lekani nipiteko mu malo yanu; nizapita naku nkala chabe pa panjila; sinizapindamukila ku kwanja ya manja olo yamanzele. 28 Muzanigulisako vakudya pa ndalama, kuti ningadye; munipaseko manzi pa ndalama, kuti ningamwe; nilekeni chabe nipiteko na mendo; 29 monga bamubadwe wa Esau banali kunkala ku Seiri, na baku Moabu banali kunkala ku Ar, banachitila kuli ine; mpaka ninapita ku Yodano mpaka mumalo yamene Yehova mulungu watu atipasa ife.' 30 Koma Sihoni, mfumu ya Heshboni, sanafune kuleka ife kupitila kuli eve; chifukwa Yehova Mulungu wanu anayumisa maganizo yake na kulimbisa mutima wake, kuti iye angamugonjese mwa mpavu zanu, monga mwamene akuchita lelo. 31 Yehova anakamba kuli ine, 'Ona, Ine nayamba kupulumusa Sihoni na malo yake basogolo panu; yambani kutenga, kuti imwe mutenge malo yake.' 32 Mwaicho Sihoni anachoka mokangana naife, eve na bonse bantu bake, kumenyana pa Jahazi. 33 Yehova mulungu watu anamupasa kuli ife ndipo tinamugonjesa na bana bake bamuna na bantu bake bonse. 34 Tina tenga yonse mizinda yake pa ntau ija naku onongelatu mizinda yonse- bamuna na bakazi na bana bang'ono; sitinasiyeko opulumuka aliyense. 35 Koma chabe vibeto tinatenga vapindu kuli ife, pamozi na va pindu vamu mizinda zamene tinatenga. 36 Kuchoka ku Aroer, yamene ili mumbali mwa chigwa cha Arnon, na kuchoka ku munzi wamene uli muchigwa, kufikila ku Gileadi, kuja kunalibe munzi utali kwa ife. Yehova Mulungu wathu anatipasa mumanja mwathu. 37 Kunali chabe ku malo ya wobadwa kwa Ammoni kwamene simunayende, monga kuli yonse mbali ya mumana wa Jabbok, na minzi ya ziko yapapili-Kulikonse Yehova Mulungu wathu analesa kuti tiyendemo.