Mutu 9

1 Koma Sauli, akali kuyofya zopaya ophunzira ba Ambuye, anayenda kwa akulu asembe 2 nomupempha makala yakuma sinagoge mu Damasiko, kuti ngati wapeza wina aliyense olondola Njira ya Chikristu, amena kapena azimai, ababwelese omangiwa ku Yelusalemu. 3 Pamene enzo yenda, cinacitika kuti pamene anafika pa fupi na Damasiko, mwazizi kunabonekela pali yeve laiti kucoka ku mwamba; 4 ndipo anagwa pansi novela mau kukamba kuti, "Sauli, Sauli, cifukwa nicani unisausa ine?" 5 Sauli anayankha ati, "Ndimwe ndani, Ambuye? Ambuye anamuyankha ati, Ndine Yesu wamene usausa; 6 koma nyamuka ngena mu tauni, uzauziwa vamene ufunika kucita." 7 Bamuna banali nayeve anlibe cokamba, kumvela mau, koma osaona aliyense. 8 Sauli ananyamuka pansi, ndipo pamene anasegula menso, kulibe cili conse camene anaona; so banamugwila pa kwanja nomuleta mu Damasiko. 9 Pamasiku yatatu senzoona, ndipo sadye kapena kumwa kali konse. 10 Manje kunali ophunzira mu Damasiko zina lake Ananiya; ndipo Ambuye anakamba nayeve mu maso mphenya, "Ananiya." Ndipo anakamba ati, " Onani, Nilipano Ambuye." 11 Ambuye anakamba nayeve, "Nyamuka, ndipo yenda munjila yamene iyitaniwa kuti Siteleti, ndipo pa nyumba ya Yudasi akafunse kuti ufuna mwamuna wamene acoka ku Tasasi oyitanidwa Sauli; cifukwa ali kupemphera; 12 ndipo awona maso mphenya ya munthu zina lake ni Ananiya kubwela noyika manja pa iye, kuti ayangane futi." 13 Koma ananiya anayankha, "Ambuye, nemvera kuli ambili pali uyu munthu, kuwononga kwamene awononga ku banthu oyela ali ku Yelusalemu. 14 Ali na mphamvu kucoka kuli mkulu wa nsembe kuti amange aliyense wamene ayitana pa zina lanu." 15 Koma Ambuye anakamba ati kuli yeve, "Enda, cifukwa nicosebenzela canga co sankhika, kunyamula zina langa kuli akunja na mafumu na bana ba Israyeli; 16 cifukwa nizamubonesa mwamene afunika ku vutisiwa cifukwa ca zina langa." 17 So Ananiya anayenda, noloba munyumba. Pakuika manja yake pali yeve, anakamba ati, "Mubale Paul, Ambuye Yesu, wamene anabonekela kuli iwe pa njila pamene wenzobwela, anituma kuti uyangana futi ndipo ulandila Mzimu Oyela." 18 Pamene apo vinthu monga mamba vinacoka kucoka mu menso ya Sauli, ndipo anayangana; ananyamuka ndipo anabatizika; 19 ndipo anadya nonkhala na mphamvu. Anankala na omphunzira ku Damasiko pama siku ambili. 20 Pa nthawi yamene iyo analalikila za Yesu mumasinagoge, kukamba kuti iye nimwana mwamuna wa Mulungu. 21 Bonse bamene anamumvela banadabwa nokamba kuti, " Kansi siuja wamene anabononga baja wamene anaitana pali iyi Zina? Ndipo abwela kuno kuti ababwelese womangidwa kuli mukulu wa nsembe." 22 Koma Sauli anankhala maningi namphamvu, ndipo analeta vuto pali ba Yuda amene enzo nkhala mu Damasiko pakuwasimikizila kuti Jesu ni Kristu. 23 Pamene panapita masiku ambili, Ayuda anapanga zakuti ba mupaye yeve. 24 Koma plani yabo inazibika kuli Sauli. Banayanganila pa geti usiku na muzuba nausiku kuti bamupaye. 25 Koma ophunzira bake banamutenga usiku nomupitisa kucipupa, kumupeleka pansi mu basiketi. 26 Pamene anabwela ku Yelusalemu, Sauli anayesa kujoina ophunzira, koma bonse banamuyopa yeve, sabanakhulupilile kuti enzeli ophunzila. 27 Koma Banabasi anamutenga nomupeleka kuli ma apostozi. Ndipo anabauza mwamene Sauli anabonele Ambuye pa njila nakuti Ambuye anakamba nayeve, namwamene Sauli analalikilila mwamphamvu muzina la Yesu ku Damasiko. 28 Anayenda nayeve pamene benzongena nocoka mu Yelusalemu. Anakamba mwamphamvu muzina la Ambuye Yesu 29 nokambilana na aYuda aCigiliki; koma banapitiliza kufuna kumupaya. 30 Pamene abale banaziba pali ici, banamupeleka ku Sizelia nomutuma ku Tasisi. 31 So manje, mupingo monse mu Judeya, mu Galileya, mu unali namutendele ndipo unalimba; noyenda mukuyopa Ambuye ndiponso mucitonthozo ca Mzimu Oyela, mupingo unakula mu namba. 32 Manje cinabwela cacitika kuti, pamene Petro anapitamo muzinda bonse, anabwela kuli ba okhulupilila benzo nkhala mu tauni ya Lida. 33 Kuja anabwela apeza mwamuna winangu zina lake ni Aneyasi, wamene anali cigonele pabedi yake zaka 8, cifukwa enzeli olemala mendo. 34 Petro anakamba kwa yeve kuti, "Aneyasi, Yesu Kristu akucilisa iwe. Nyamuka noyanzula bedi yako." Ndipo pamene apo ananyamuka. 35 So aliyense wamene enzonkhala mu Lida namu Sharoni anamuona uja mwamuna ndipo anatembenukila kwa Ambuye. 36 Manje kwenzeli ophunzira winangu ku Yopa zinalake ni Tabita, yamene itanthauza "Dokasi." Uyu mzimayi enzeli maningi wazinchito zabwino na zacifundo zamene anacitila osauka. 37 Cinabwela cacitika kuti mumasiku ayo anadwala nomwalila; pamene banamusambika, banamugoneka mucipinda capamwamba. 38 Cifukwa cakuti Lida yenzeli pafupi na Jopa, nakuti ophunzila banamvera kuti Petro enzeli kwamene kuja, banatumako bamuna babili kuli yeve, kumupempha, bwela kuno mosawaya-waya." 39 Petro ananyamuka noyenda nabeve. Pamene anafika, banamupeleka mucipinda capamwamba. Ndipo wonse bazimayi ofedwa anayimilila pafupi nayeve nishi balila. 40 Petro anabacosa panja bonse, anagwada pansi, nopemphela; nobwela upindimukila kuli thupi, anakamba ati, "Tabita, nyamuka." Anasegula menso yake, ndipo pamene anaona Petro ananyamuka nonkhala. 41 Petro anamugwila kwanja nomunyamula; ndipo pamene anaitana okhulupilila na azimai ofedwa, nomupeleka kulibeve wamoyo. 42 Iyi nkhani inazibika mu Yopa monse, ndipo banthu bambili anakhulupila mwa Ambuye. 43 Cinabwela cacitika kuti Petro anakhala masiku ambiri mu Yopa na mwamuna ocedwa Simoni, bopanga vikumba.