Mutu 23

1 Paulo anayangana pali ma membala ba nkhanso nokamba ati, "Abale, nankhala pamaso pa Mulungu mumaganizo abwino kufikila lelo." 2 Mukulu wa nsembe Ananiyasi analamulila baja bamene naimilila pafupi nayeve kuti amumenye pakamwa. 3 Ndipo Paulo anakamba ati kwa yeve, Mulungu azakumenya iwe, iwe cipilala ca waiti. Kansi wankhala kuniweluza ine mwa lamulo, koma ulamulila kuti banimenye, mosushana na lamulo?" 4 Baja bamene banaimilila pafupi banakamba ati, "Umu ndiye mwamene unyozela mukulu wansembe wa Mulungu?" 5 Paulo anati, Sininanyozele , abale, kuti enzeli mukulu wa nsembe. Cifukwa kunalembewa, Suzakamba zoipa pali wolamulila wa banthu bako." 6 Pamene Paulo anabona kuti mbali imozi yaba khanso anali a saduki ndipo mbali imozi apharise, anakamba mopunda mu khanso, "Abale, ndine Mupharise, mwana mwamuna wa Mupharise. Nicifukwa cakuti nilinaco cisimikizo kuyembekezela bakufa kuuka ndiye camene niweluziliwa." 7 Pamene anakamba izi, kusushana pakati pa Apharise na Saduki kunayamba, ndipo gulu inagabikana. 8 Cifukwa Asaduki akamba kuti kulibe kuuka, kulibe angelo, namizimu, koma Apharise bagwilizana nazo zonse. 9 So mukangano ukulu unacitika, ndipo olemba binangu benzeli kumbali ya Pharisi anaimilila nosusha, kukamba kuti, "Sitipeza mulandu nauyu munthu. Nanga ngati muzimu kapena mungelo akamba naiye?" 10 Ndipo apo kunauka kukangana maningi, kapitawo mukulu anayopa kuti Paulo azamupweteka, so analamulila asilikali kuti bamutenge mwacikakamizo pakati pama membara ba khanso, nakumubwelesa pamalo yothabila. 11 Usiku okokhapo Ambuye anaimilila pafupi nayeve nomuuza kuti, "Osayopa, monga mwamene wapelekela umboni pali ine mu Yelusalemu, so ufunika kupeleka umboni mu Roma." 12 Pamene kunakhala kuseni, bena ba Yuda banagwilizana noitana tembelelo pali beve: banakamba ati sibazadya kapena kumwa ciliconse paka maupaye Paulo. 13 Benzeli wokwanila ngati bamuna bali 40 bamene banapanga iyi pangano. 14 Banayenda kuli mukulu wa nsembe na azikulu nokamba ati, tazifaka pa tembelelo ikulu, sitizadya kanthu paka tipaye Paulo. 15 Manje so, lekani khanso iwuze kapitawo mukulu alete Paulo kuli iwe, cifukwa ungaweluze mulandu wake bwino. Kuli ise, ndise wokonzekela kumupaya iye akalibe kufika kuno." 16 Koma mwana wa sisita wa Paulo anamvela kuti benzo muyembekezela, so anayenda noloba mumalo yothabilapo numuuza Paulo. 17 Paulo anaitana umozi wa asilikali nokamba ati, "Mupeleke uyu nyamata kuli mukulu wa asilikali, cifukwa ali navamene afuna kumuuza." 18 So musilikali anatenga munyamata nomuleta kuli kapitawo mukulu nokamba ati, Paulo kaidi ananiitanila yeve, noniuza kuti nilete uyu munyamata kwa iwe. Alinacokamba kwa iwe." 19 Kapitawo mukulu anamutenga pakwanja pamalo yobisika nomufunsa, "Ufuna kuniuza cani?" 20 Mnyamata anakamba ati, Ayuda bagwilizana kuti bakupemphe kuti ulete Paulo mailo ku khanso, monga ngati bafuna kumufunsa bwino bwino pali uyu mulandu. 21 Koma usabvomele, cifukwa kuli bamuna wopitilila bali 40 bamene bamuyembekezela. Bazifaka tembelelo, kuti sibazadya kapena kumwa mpaka bamupaye Paulo. Namanje so, niwokonzekela, kuyembekezela kuti ubvomele." 22 So kapitawo mukulu anamusiya mnyamata kuti ayende, nishi amuuza kuti, "Usauze aliyense kuti waniuza izi zinthu." 23 Pamene apo anamuitanila asilikali babili nokamba ati, Konzekelani basilikali bali 200 kuti bayende ku Sezariya, nabali 70 bamahosi, nabamikondo bali 200. Muzayenda na 9:00 koloko." 24 Anabalamulila kuti bamupase nyama yamene Paulo aza yenzanomupeleka kuli govana Felike. 25 Ndipo analemba kalata kuti: 26 Klaudiyasi Lisiyasi kuli olemekezeka Govana Felike, nikupasa moni. 27 Uyu munthu anamagidwa na Ayuda ndipo enzofuna upaiwa nabeve, pamene apo tinabwela nabasilikali nomumasula, cifukwa ninamvela kuti enzeli sitizeni waku Roma. 28 Ninafuna kuziba camene banamupasila mulando, so ninamupeleka ku khanso yabo. 29 Ninabvela kuti banamupasa mulandu pamafunso ya malamulo tabo, koma kwenzelibe mulandu pali yeve wenzofunika kui bamupaye kapena kumufaka mujele. 30 So ninazibisiwa kuti penzeli pangano pali uyu munthu, so mwamusanga musanga ninamutuma kuli imwe, ndipo ninauza womupasa mulandu kuti balete milandu zake kuli imwe. Bayi." 31 So asilikali anabvelela kulamulila kwawo: banatena Paulo usiku nomuleta kuli Antipatirisi. 32 Siku yokokhapo, basilikali bambili anasiya baja benzeli pamahosi kuti bayende nayebve ndipo beve babwelele kumalo yothabilapo. 33 Pamene baja benzeli pamahosi banafika Sezariya nopeleka kalata kuli govana, ndiponso banapeleka Paulo kuli yeve. 34 Pamene govana anabelenga kalata, anafunsa kumuzinda kwamene Paulo anacokela; pamene anamvela kuti anacokela ku Silisiya, 35 anakamba ati, nizakubvela mofikapo pamene bamene bakupasa mulandu bafika." So analamulila kuti bamusungile mu hedikota yaboma ya Herode.