Mutu 16

1 Paulo anabwelanso ku Debi na Lisitila; ndipo onani, ophunzira wina zina lake Timoteyo analiko, mwana wa mzimai waci Yuda wamene anali okhulupilila; atate bake enzeli waci Giliki. 2 Banakamba zambino za iye abale bamene anali ku Lisitira na Ikoniyamu. 3 Paulo anamufuna kuti ayende naye; so anamutenga iye nomucita mudulidwe cifukwa ca Ayuda amene anali kumalo ayo, cifukwa bonse banaziba kuti atate bake benzeli ba Giliki. 4 Pamene benzo kupitila mu matauni, banapeleka ku mipingo malamulo kuti iwo amverele, malamulo yamene yanalembedwa nama apostozi na akulu mu Yelusalemu. 5 So mipingo inalimbikisika mucikhulupililo nopakilapo munamba sikuku nasiku. 6 Paulo nabanzake banayenda kupitila mumizinda ya Flagiya na Galatiya, cifukwa Mzimu Oyela anabalesa kulalilikila mau ku mizinda ya Azia. 7 Pamene banafika pafupi na Masiya, anayesa kuyenda ku Bitaniya, koma Mzimu wa Yesu onabalesa. 8 So popitila ku Masiya, anafika kutauni ya Traosi. 9 Masophenya yanamuonekela Paulo usiku: mwamuna waku Masedoniya anali imilile paja, kumuitana nokamba ati, Bwela kuno ku Mesedoniya utithandizile." 10 Pamene Paulo anabona masophenya, pamene apo tinayenda ku Mesedoniya, kuganizila kuti Mulungu anabaitana iwo kuyendo lalikila uthenga kwa beve. 11 Kunyamuka kucoka ku Traosi, tinanyamuka kuyenda ku Samoterace, ndipo siku yokonkhapo tinayenda ku Niyapolisi; 12 kucoka uko tinayenda ku Filipi, yamene ni tauni ya Mesedoniya, tauni yofunikila maningi mu boma na mu Roma, ndipo tinankhala mu tauni iyi masiku yambili. 13 Pa Sabata tinayenda panja pa geti kumbali kwa mumana, kwamene tinaganiza kuti kuli malo yopemphelerako. Tinankhala pansi nokamba na azimai bamene enze anabwela pamozi. 14 Mkazi winangu ocedwa Lidiya, ogulisa va pepo kucoka ku tauni ya Tiyatira, wamene anapembeza Mulungu, anativelela. Ambuye anasegula mtima wake kumverela kuvamene Paulo anakamba. 15 Pamene anabatizika, nanyumba, anatilimbikisa, nakukamba kuti, "ngati mwaniweluza kunkhala okhulupililika kwa Ambuye, bwelani kunyumba kwanga, nonkhala naine." Ndipo atigonjesa. 16 Cinabwela cacitika kuti, pamene tenzoyenda kumalo yopemphelerako, msikana winangu wamene enzeli namuzimu olota anakumana nase. Anapangila abosi bake ndalama zambili muzokamba zake. 17 Uyu msika anakonkha Paulo na ise nopunda, kukamba ati, " Aba banthu nibanchito ba Mulungu Mkulu kulu. Balalikila kwa imwe njila ya cipulumuso. 18 Anacita ici masiku yambili. Koma Paulo, pamene anakalipa maningi naive, anapindimuka nokamba kwa mizimu, Nikulamulila muzina la Yesu Kristu kuti ucoka mwa yeve." Ndipom cinacoka pamene apo. 19 Pamene ba bosi bake anabona kuti popangila ndalama payenda, banamumanga Paulo na Sailai nobapeleka pamaketi pamenso yaolamulila. 20 Pamene anabaleta kuli oweluza, anakamba ati, " aba banthu na Yuda ndipo bapanga mambuto yambili mu tauni mwathu. 21 Baphunzisa zinthu zosaloledwa kuti ise tilandile or kulondola ngati Aroma." 22 Ndipo gulu inanyamukila pamozi ku ukila Paulo na Sailasi; oweluza banang'amba malaya yabo nakubavula nolamulila kuti bamenyedwa nandodo. 23 Pamene banabamenya maningi, banabaponya mundende nolamulila wogading'a kuti abafakeko nzeru maningi. 24 Pamene analandila lamulo iyi, wogading'a anabaponya mukati maningi mwa jele nomanga mendo yawo maningi. 25 Pakati pa usiku Paulo na Sailasi benzo pemphela noyimba nyimbo kwa Mulungu, ndipo bakaidi benangu benzo bamvelerela. 26 Mwazizi kwenzeli kung'ambika pansi kukulu, mpaka maziko yamujele yanagwendezeka; ndipo pamene apo viseko vinaseguka, ndipo macheni ya aliyense yanamasuka. 27 Wogading'a anauka patulo nowona kuti viseko vamujele nivoseguka; anacosa cinayifi cake nonkhala pang'ono kuzipaya, cifukwa anaganiza kuti bakaidi bathaba. 28 Koma Paulo anapunda maningi, kukamba kuti, osazipanga ngozi, cifukwa tonse tilimo muno." 29 Wogading'a anaitanisa laiti nobwelo ngena, nishi anjenjema namantha, nokugwa pansi pali Paulo na Sailasi, 30 nobacosa panja nobwelo akamba ati, Kansi ningacite bwanji kuti nipulumuke?" 31 Banakamba ati, Khulupilila mwa Ambuye Yesu, ndipo uzapulumusiwa, iwe na banja lako lonse. 32 Banakamba mau ya Ambuye kwa yeve, pamozi nabonse benzeli munyumba mwake. 33 Pamene apo gadi anabatenga pa nthawi yamene iyo yausiku, nobasanbika mendo vilonda vabo, ndipo yeve nabanja lake lonse banabatizika pamene apo. 34 Anabwelesa Paulo na Sailasi kunyumba kwake nobapasa vakudya. Anasangala maningi nanyumba yake yonse, cifukwa bonse anakhulupilila Mulungu. 35 Pamanje pamene kwenzeli muzuba, oweluza anatuma mau kuli magadi nokamba ati, Leka abo banthu bayende." 36 Gadi anarepota mau kwa Paulo, kukamba ati, "Oweluza anituma mau kuli ine kuti nibamasule: manje so cokani, muyende bwino. 37 Koma Paulo anakamba ati kuli beve, "Banatimenya pacigulu, banthu balibe mulandu aci Roma, ndipo mwatifaka mujele; manje apa bafuna baticose mwaci sinsi? Yai ndithu, balekeni babwele beka kuti baticose. 38 Magadi anapeleka aya mau kuli oweluza; oweluza anamvera mantha pamene banmvera kuti Paulo na Sailasi benzeli ba Roma. 39 Oweluza anabwela kubapapata; ndipo pamene anabacosa mukele, anauza Paulo na Sailasi kuti acoke mu tauni. 40 So Paulo na Sailasi anacoka mujele noyenda kunyumba kwa Lidiya. Pamene Paulo na Sailasi anabona abale, anabalimbikisa ndipo banacoka mu Tauni.