1 Bamuna benangu banacoka ku Yudeya nomphunzisa abale, kunenakuti, pokhapo mukadulidwa monga pa mwambo wa Mose, simungapulumusidwe." 2 Pamene Paulo na Banabasi anakangana nocita nawo ndale, abale anaganiza kuti Paulo, Banabasi nabena afunika kuyenda ku Yelusalemu kuli ma apostozi na akulu pali iye nkhani. 3 Ndipo apo, pakutumidwa nampingo, anapitila ku Fonisiya na Samaria nocita anaounsi kutembenuka kwa Akunja. Anabwelesa cisangalalo cacikulu kuli abale onse. 4 Pamene anafika ku Yelusalemu, analandliwa na mpingo nama apostozi na akulu, ndipo analipota zonse zinthu zamene Mulungu anacita pamozi naiwo. 5 Koma amuna bena bamene anakhulupilila, enzeli ku gulupu ya Afalisi, anaimila nokamba ati, "nicofunikila kubacita mdulidwe nakubalamulila kuti asunge malamo ya Mose. 6 So ma apostozi na akulu anakuma pamozi kuti ayanganepo iyi nkhani. 7 Pamene banakambilana kwa nthawi itali, Petulo ananyamuka nokamba kwa iwo, "Abale, muziba kuti panthawi yambwino yamene yapita Mulungu anasankha pakati pawo, kuti kupitila mukamwa mwanga Akunja amvele mau awuthenga, nokhulupilila. 8 Mulungu, aziba mtima, abapasa umboni, kubapasa Mzimu Oyela, monga mwamene anacitila ise; 9 ndipo sanapange kupatula pakati pa ise nabeve, kupanga mitima kuyela mwacikhulupililo. 10 Mwanje nicifukw ninji muyesa Mulungu, kuti muyike joko pamikosi yaophunzila yamene ngakhale azitate bathu kapena banakwanisa kucilandila? 11 Koma tikhulupilila kuti tizapulumusiwa kupitila mcisomo ca Ambuye Yesu, monga cinalili kwabeve." 12 Gulu yonse inankhala zii pamene benzomvela Banabasi na Paulo penzo repota pa visanzo na vodabwisa Mulungu anacita pakati pa Akunja kupyolela mwabeve. 13 Pamene banaleka kukamba, Jemusi anayankha, nokamba ati, Abale, mvelani kwa ine. 14 Simoni wakamba mwamene Mulungu poyamba mwacisomo anathandizila Akunja kuti mwabeve atenge banthu kwa zina lake. 15 Mau y aneneri yanagwilizana nazeve, monga kunalembewa, 16 'Zikasila izi zinthu nizabwelela, Ndipo nizamanganso tenti ya Davide, yamene inagwa; Nizainyamula noibwezelapo, 17 kuti baja bamuna banasala akafune Ambuye, kuyikilako akunja oyitanidwa na zina langa.' 18 Ici ndiye camene Ambuye akamba, nindani wacita izi zinthu zamene zinazibika kucoka kudala. (Ma Baibulo inangu yabelenga guti, Ici ndiye camene Ambuye akamba, kwamene zizibika zonse zocitita zake kucoka kudala.) 19 Cifukwa ca ici, maganizo yanga ni aya, kuti tisavutise baja acikunja bamene babwela kwa Mulungu; 20 koma kuti tibalembele kuti bacoke kupemphelera mafano, kuciwelewele, nacakufa ceka, namwazi. 21 Kucoka ku mibado yakudala kulibanthu mu tauni iliyonse bamene alalikila nobelenga Mose mumasinagoge sabata ili yonse." 22 Ndipo cinaboneka bwino kuli ma apostozi na akulu, namupingo bonse, kusankha Yudasi oyitanidwa Basabasi, na Sailasi, amene anali azisogoleli mu mpingo, nobatuma ku Antioku pamozi na Paulo na Banabasi. 23 Analemba izi: "Ma apostozi, akulu na abale, kwaAkunja abale ku Antioku, Siriya na Cilisiya, moni. 24 Tinamvela kuti ba muna benangu bamene tinapasa malamulo maningi, banacoka kuli ise ndipo bakuvutisani naviphunziso vamene vivutisa moyo yanu. 25 So cinatibonekela bwino tonse kuti tigwilizane kuti tisankhe banthu nobatuma kwa imwe okondedwa Banabasi na Paulo, 26 banthu bamene baika moyo wabo pangozi cifukwa ca zina la Ambuye Yesu Kristu. 27 Tatuma cifukwa caici Yudasi na Sailasi, bamene azakuuzani zinthu zimozi nazimozi. 28 Cifukwa cinaoneka bwino kwa Mzimu Oyela na kwa ise, kuika paimwe katuntdu olema kupambana izi zinthu zofunikila: 29 kuti mucoke ku vinthu vopelekewa nsembe kumafno, mwazi, vakufa veka, nakuciwele wele. Ngati muzisunga kuli ivi vinthu, zizankhala bwino na imwe. Mukhale bwino." 30 Ndipo beve, pamene banamasulidwa, anabwela ku Antioku; anabwelesa banthu pamozi, anapeleka kalata. 31 Pamene anaibelenga, banakondwela cifukwa ca cilimbikiso. 32 Yudasi na Sailasi, na neneri, analimbikisa abale namau ambili nobalimbikisa. 33 Pamene banankhalako pakanthawi, banabamasula mwamutendele kucoka ku abale kuli beve bamene anabatuma. 34 (Koma cinamuonekela bwino Sailasi kusalila). 35 Koma Paulo na Banabsi anankhala mu Antioku pamozi na bene bambili, kwamene anaphunzisa nolalikila mau ya Ambuya. 36 Pamene panapita nthawi Paulo anakamba ati kwa Banabsi, "Tiye tibwelele manje tikayendela abale mutauni iliyonse kwamene tinalalikila mau ya Ambuye, nobona mwamene alili. 37 Banabasi anafunanso kuti atenge Yohane woitanidwa Mariko. 38 Koma Paulo anaganiza kuti sicinali cabwino kutenga Mariko, wamene anabasiya ku Pafaliya ndipo sanapitilize nchito pamozi nayeve. 39 Ndipo kunapezeka kusushana kwambili, kufika mpaka banapatukana, ndipo Banabasi anatenga Mariko noyenda ku Sipulasi. 40 Koma Paulo anasankha Silasi ndipo anacoka, pambuyo pobapasa kuti asamalile mwacisomo ca Ambuye. 41 Ndipo anapitila ku Siliya na Silisiya, kulimbikisa mipingo.