1 Manje ma apostozi na abale benzeli mu Yudeya banamvela kuti ba Kunja nabeve balandila mau ya Mulungu. 2 Pamene Petro anabwela ku Yelusalemu, baja bamene benzeli ku gulu ya amudulidwe banamususha; 3 banakamba ati, unayanjana na banthu osadulidwa nakudya nabo!" 4 Koma Petro anayamba kubafotokozela nkhani yonse mufikapo; anakamba ati, 5 Nenzeli kupemphera ku tauni ya Yopa, ndipo nenzeli namaso mphenya pali contena ibwela pansi, monga cinyula cikulu kucokela kumwamba kubwela nama kona yake yali 4. Cinabwela kwa ine. 6 Ninayanganamo ndipo ninaganizilapo. Ninabona nyama zamendo yali 4 zili muziko, nyama zamusanga, nyama zokalaba pansi, na nyoni zamumwamba. 7 Ninamvera mau kukamba naine, "Myamuka, Petro; paya nakudya!" 8 Ninakamba ati, osati so, Lord: kulibe cosayela kapena codesedwa camene cinalowapo mukwamwa mwanga." 9 Koma mau yanayankha futi kucoka kumwamba, Camene Mulungu wayelesa, usaciitane codesedwa." 10 Ici cinacitika katatu, ndipo zonse zinabwelelamonso kumwamba. 11 Ndipo apo onani, pamena apo panali bamuna batatu oyimilila pasogolo ya nyumba mwamene tenzelili; wanatumiwa kwa ine kucoka ku Sizeliya. 12 Mzimu unanituma kuti niyende nabeve, ndipo kuti nisapusanise paki beve. Aba ba bale bali 6 banayenda naine, ndipo tinaloba munyumba ya uyu munthu,. 13 Anatiuza mwamene anabonela mngelo kuyimilila mnyumba mwake nokamba ati, "Tuma amuna ku Yopa kuti babwelese Simoni ocedwa Petro. 14 Azakamba naiwe uthenga wamene uzapulumuka nabo -iwe na nyumba yako yonse." 15 Pamene ninayamba kukamba nabeve, Mzimu Oyela unabwela pali beve, monga cenzeli kwa ife poyamba paja. 16 Ninakumbukila mau ya Ambuye, mwamene anakambila, "Yohane zoonadi anabatiza na mazi; koma muzabatizika mu Mzimu Oyela." 17 So ngati Mulungu anabapasa beve mphaso monga anatipasila pamene tinakhulupilila pali Ambuye Yesu Kristu, ndine ndani ine, kuti nitalikane na Mulungu?" 18 Pamene anamvera izi zinthu, palibe camene anakamba moyankha, koma anayamika Mulungu nokamba ati, "Kansi Mulungu wapasa kutembenuka kwa moyo kuli akunja nabeve." 19 Manje baja bamene banamwazikana cifukwa cakusausidwa kwamene kunayamba nopaiwa kwa Stefano banafika paka ku Fonisia, Saipulasi, naku Antioku, koma anakamba za uthenga wa Yesu cabe kuli ba Yuda. 20 Koma benangu pali beve, bamuna ocokela ku Saipulasi na Sailini, anabwela ku Antioku nokambanso nama Giliki, kubauza za uthenga wabwino wa Ambuye Yesu. 21 Ndipo kwanja kwa Ambuye kwenzeli nabeve; namba ikulu maningi inakhulupilila notembenukila kwa Ambuye. 22 Uthenga pali beve unafika mumatu ya mpingo ku Yelusalemu: ndipo banatuma Banabasi kufika mpaka ku Antioku. 23 Pamene anabwela nobona mphaso ya Mulungu, anakondwela, ndipo anabalimbikisa bonse kuti ankhale mwa Ambuye namtima wabo bonse. 24 Cifukwa enzeli munthu wabwino nabozula na Mzimu Oyela, nacikhulupililo, ndipo banthu bambili banafakiliwako kwa Ambuye. 25 Banabasi apo anayenda ku Tasisi kuyendo sakila Sauli. 26 Pamene anamupeza, anamuleta ku Antioku. Cinabwela cacitika nicakuti, caka conse banasonkhana pamozi namupingo nophunzisa banthu bambili. Ophunzira banaitanidwa kuti Akristu koyamba ku Antioku. 27 Manje pamasiku aya aneneri benangu banabwela kucoka ku Yelusalemu kubwela ku Antioku. 28 Umozi mwa beve, Agabasi mwazina lake, anaimilila nobonesela mwa Mzimu kuti njala izacitika paziko lonse. Izi zinacitika mumasiku ya Kilaudiyasi. 29 So, ophunzira, kulingana mwamene anakwanisila aliyense, anaganizila kutuma thandizo kuli abale ku Yudeya. 30 Anacita ici; anatuma ndalama kuli akulu mumanja ya Banabasi na Sauli.