Mutu 4

1 nipereka chilamulo ichi pamaso pa mulungu ni yesu khrostu, wamene azaweruza amoyo na bakufa, ndipo chifukwa cha kuonekera kwake na umfumu wake: 2 Lalikani mau. nkhalani okonzeka pamene zili bwino na pamene sizili bwino. simikizirani, zuzulani, yamikani na kuleza mtima na chipunziso. 3 pakuti nthawi izafika pamene banthu sibazakonda chipunziso chabwino. mumalo mwake bazaitana apunzisi kulingana na zofuna zao. bamene bazamvesa bwino matu yawo. sibazafuna kumvera chilungamo, 4 ndipo bazaika matu yawo ku zinthu zaboza. 5 koma inu, nkhalani tcheru pa zinthu zonse. bvutikani; gwirani nchito ya uvangeli; chitani nchito yanu. 6 chifukwa nithiridwa kudala panja. nthawi yanga ya kuchoka yafika. 7 nalimbana nako kulimbana kwa bwino; nasiliza nchito yanga; nasunga chikulupiliro. 8 kolona wa chilungamo wasungidwa wanga, wamene ambuye, oweruza oyera mtima, azanipasa pa siku lija, osati ine chabe koma ku onse bamene bakonda kuonekera kwake. 9 chitani zonse zotheka kuti mubwere kwa ine mwa msanga. 10 Pakuti Demas wanisiya. akonda ziko lino ndipo wayenda ku thessalonika. crescens anayenda ku galatia, tito anayenda ku dalmatia. 11 Luka chabe ndiye ali na ine. Mumutenge Marko mubwere nayeve chifukwa ali na nchito maningi kuli ine pa nchito. 12 Tichikasi ninamutuma ku Aifeso. 13 Chovala chamene ninasiya ku troas na carpus, mubwere nacho pamene mubwera. 14 alexander waku chipala cha kopa anaonesa zichitidwe zoipa kwambiri pa ine. mulungu azamulipila kulingana na zinchito zake. 15 Iwe naiwe uyenera kunkhala ochenjera naye, chifukwa anashusha maningi mau yathu. 16 Pa kuzichinjiliza kwanga koyamba, palibe wamene anaimilira naine. mumalo mwake, bonse banathaba. zisawerengedwe pa iwo. 17 koma mulungu anaimilira na ine na kunilimbisa kuti mwa ine zokambidwa zikwaniritsidwe mokwanira, nakuti bonse ba mitundu bamvere. ninapulumusidwa mukamwa mwa mukango. 18 Ambuye bazanipulumusa ku zoipa zonse ndipo bazanipulumusa kamba ka ufumu wa umwamba. kwa iye kunkhale ulemelero nthawi zonse. amen 19 Mumuposhe priscilla, aquilla, na nyumba ya onesiphorus. 20 Erastus anasala ku corinth, koma trophimus ninamusiya odwala ku miletus. 21 Chitani zonse zotheka pamene nthawi yozizila isanafike. eubulus akupasani moni, komanso pudens, linus, claudia, na abale onse. 22 Ambuye ankhale na muzimu wako. Chisomo chinkhale na iwe.