Mutu 3

1 Manje, nilemba kwa inu, okondewa, nkhalata iyi ya chiwiri ngati chikumbuso cha ku maganizo yanu, 2 kuti mukumbukire zamene zinakambika kudala naba neneri oyera na lamulo la ambuye Yesu Khristu kupasiwa naba positoli banu. 3 Ziwani izi poyamba, kuti banthu bovuta bazabwera mu masiku yosiliza. Bazakamba voipa na kupitirira kuchita zofuna zao. 4 Bazakamba, " ili kuti lonjezo ya kubweraso kwake? kuchoka pamene batate bathu banagona zinthu zonse zili chimozi-mozi, kuchoka pamene chalo chinapangiwa." 5 Baibalira dala kuti kumwamba na dziko la pansi zinapangiwa kuchoka ku manzi na manzi, kudala kulingana na malamulo ya Mulungu. 6 Nakuti chifukwa cha izi zinthu, dziko la kudala linaonongewa, kuzula na manzi. 7 Koma manje dziko liyembekeza chiweruzo cha muliro kulingana na lamulo limozi-mozi. Bachisungira siku la chiweruzo na kuonongeka kwa banthu ochimwa. 8 Simuyenera kuibala, okondewa, kuti siku limozi kwa Mulungu ili ngati zaka 1000, elo zaka 1000 zili ngati siku imozi kwa Mulungu. 9 Mulungu samachedwa pa malonjezo yake, monga mwamene benangu bangaonere kuchedwa. M'malo mwake niodekha mtima pa inu. Safuna ati umozi wa inu akaonongeke, koma aliyense apange malo ya kuleka zoipa. 10 Koma, siku la ambuye lizabwera monga kawalala: Dziko lizatha na chongo chachikulu. Zinthu zizapsya na muliro, ndipo dziko na nchito zonse za mkati zizaziwika. 11 Pakuti zinthu zonse zizasila motere, inu muzankhala banthu ba bwanji? Mufunika kunkhala umoyo wabwino wa umulungu. 12 Mufunika kuyembekeza kubwera kwa siku la Mulungu. Pa siku limenelo, miyamba izaonongewa na muliro, na zonse zizasungunuka kamba ka kupya. 13 Koma kulingana na malonjezo yake, tikali kuyembekeza kumwamba kwasopano na dziko lasopano, mwamene banthu babwino bazankhala. 14 Kotero, okondewa, pakuti muyembekeza izi zinthu, muchite zonse zamene mungakwanise kuti mukapezeke mulibe bvuto pa menso pa Mulungu, muli yeve. 15 Komanso muone kuchedwa kwa ambuye kunkhala ngati kudekha mtima kwake kukhala cipulumus o, monga momwe m'bale wathu Paulo analembera inu, kulingana na nzeru zamene zinapasidwa kwa yeve. 16 Paulo akamba pa izi zinthu mu makalata yake yonse, mwamene muli zinthu zobvuta kumvesesa. Mbuli na banthu osankhazikika bamasokoneza zinthu zimenezi, mwamene bamachitira malemba yenangu, kuti bakaonongedwe. 17 Kotero, okondewa, pakuti muziba izi zinthu, muzichinjirize kuti musasokonezewe na chinyengo cha anthu oipa ndi kutaya chilungamo chanu. 18 Koma kulani mu cisomo ndi nzeru za ambuye ndi mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Ulemelero unkhale kwa yebve lero na nthawi zonse. Amen!