Mutu 2

1 Aneneri aboza anabwera kwa anthu, naonso aphunzisi aboza azabwera kwa inu. Azaleta zipunziso zaboza, elo bazakana mukulu amene anabagula. Baziletela mabvuto pali beve beka. 2 Banthu bambiri bazabakonkha, elo chifukwa cha beve chilungamo chizaonongeka. 3 Chifukwa cha kuzikonda bazapangirapo pindu pali imwe chifukwa cha mau yao yaboza. Chiweruzo chao chizabwera manje-manje; kuonongeka kwao sikugona. 4 Chifukwa Mulungu sanaleke angelo bamene banachimwa. Anabapereka kwa Tartarus kuti bankhale mu cheni ya kumidima mpaka pa nthawi ya chiweruzo. komanso, sanalekelele dziko la kudala. 5 mu malo mwake anasunga Noah wamene anali oyera mtima, pamozi na benangu asanu ndi awiri, pamene analeta mvula yosasila pa dziko la banthu ochimwa. 6 Mulungu anaonongaso Sodom na gomorrah na moto, ngati chisanzo cha chilango chamene chizabwera kusogolo. 7 Koma Lot oyera, amene enze anankhala pakati pa banthu ochimwa, Mulungu anamupulumusa. 8 Kwa uja munthu osachimwa, amene enze kunkhala pakati pao masiku onse, enzeli kubvutika mu mtima pa zimene anali kuona na kumvera. 9 Mulungu amaziba mopulumusila anthu ake kuchoka mu mayesero, na kuziba motengera banthu oipa kuti balandire chilango pa siku la chiweruzo. 10 Izi zinkhala zoona kwa baja bamene bapitirira kuchita zinthu zoipa kulingana na zamene thupi lao lifuna nakukana kumvera lamulo. Ndi olimba mtima komanso odzala ni chifuniro. Sayopa kunyoza banthu ozozedwa. 11 Angelo ali ndi mphamvu zambiri, koma sabweresa manyozo ya chiweruzo pa iwo kwa ambuye. 12 Koma izi nyama zopanda nzeru zinapangiwa kuti zigwidwe mu chionongeko. Saziba chamene atukwana. Muchionongeko 13 bazapeza mpaso ya machimo ao. Aona monga kusangalala kwa masana nikwabwino. ni odesedwa na zoipa. Amamva bwino akamachita zinthu zao zoipa pomwe alikudya nanu. 14 Ali na menso yozula na bakazi ba chiwelewele; sakhutira nao machimo. Amatuntha mitima yofoka kuti yachite zoipa, ndipo mitima yao yanaphunzisidwa kukhumbwa vinthu. Ni bana ba tembelero. 15 Ataya njira yabwino. Anasokera, nasata njira ya Balaam mwana wa Boer, omwe akonda kulandira malipiro ya machimo. 16 Koma analandira chizuzulo pa zoipa zake. Bulu osakamba koma kukamba mau ya munthu analetsa utsiru wa mneneri. 17 Anthuwa ali ngati nyenje yopanda madzi. Ali ngati mmakumbi yamene mphepo imayendesa. Mdima olema unasungiwa pali beve. 18 Bakamba na nthota zopanda pindu. Bamanyengelera banthu na zofuna za thupi lao. Bamanyengelera banthu bamene bafuna kuthaba bamene bankhala mu zoipa. 19 Bamalonjeza mutendere kwa beve, koma beve nibakapolo ba zoipa. Chifukwa munthu nikapolo wa vamene vimubvuta. 20 Aliyense wamene apewa chionongeko cha dziko lapansi kusebenzesa chizibiso cha Yesu Ambuye wathu, koma abweleranso ku zoipa, ndiye kuti chothera chinkhala choipa maningi kuchira choyamba. 21 Chinakankhala bwino kuti sibanazibe zabwino kuchira kuziba na kubwelera futi ku zoipa kusiya malamulo yamene yenze banapasiwa. 22 Mwambi uyu niwazoona pa beve: " galu abwelera futi ku vamene waluka. Nkhumba yosambika bwino imabwelera futi ku matika."