1 Simon Petulo, kapolo ni mpositoli wa Yesu Khristu kwa onse bamene banalandira chikhulupiliro cholingana na chamene talandira, chikhulupiliro na kuyera kwa mulungu na mpulumusi wathu Yesu Khristu. 2 Lekani cisomo na mtendere zinkhale zambiri pa zinthu za Mulungu na Yesu Khristu ambuye athu. 3 Zinthu zonse za mphamvu ya moyo na umulungu zinapasidwa kwa ife pa kuziba Mulungu amene anatiitana mwa mphamvu zake. 4 Kupitira mwa izi anatipasa malonjezo yambiri yakulu kuti munkhale otengako mbali pa zinthu zabwino, kuti musapezeke mu mabvuto yomwe yali mu ziko chifukwa cha kuzikonda. 5 Pa ichi, muyeseko kubweresa mtendere chifukwa cha chikhulupiriro chanu, ubwino wanu kamba ka zamene muziba za Mulungu. 6 Pa kuziba kwanu, mufakepo kuzilesa elo pa kuzilesa kwanu mufakepo kukosa elo pa kukosa kwanu mufakepo kuziba Mulungu. 7 Pa kuziba Mulungu kwanu mufakepo kukonda ba bululu banu elo pa kukonda banzanu mufakepo chikondi. 8 Ngati izi zonse zili mwa inu elo zikula mkati kanu, simuzakangiwa kubala zipaso pa zamene muziba za ambuye Yesu Khristu. 9 Koma aliyense amene alibe izi zinthu amaona zamene zili pafupi chabe; alibe menso. Aibala kusukidwa ku machimo yake yakudala. 10 Manje, ba bululu, muyenera kuyesa kuchita zamushe kuti kuitanidwa na kusankidwa kwanu kusankhale kobvuta. Ngati mwachita izi zinthu, simuzagwa. 11 Ngati mwachita zimenezo ndiye kuti ufumu wa kumwamba wa ambuye Yesu Khristu uzapasidwa kwa inu. 12 Kotero ine nizankhala okonzeka kukukumbusani pa izi zinthu nangu kuti muviziba kudala, nangu kuti munakosa kudala mu chikhulupiliro manje. 13 Niona ni chinthu chabwino kukukumbusani na kukupasani mphamvu pa izi malinga ngati nili mu tenti. 14 chifukwa niziba ati manje-manje nizachosa tenti, monga mwamene Yesu Khristu anionesera. 15 Nizayesesa kuti mukazikumbuka izi zinthu pamene ine nizayenda. 16 Chifukwa sitinakonkhe maningi zinthu za boza zamene zinapangidwa pamene tinamuuzani za mphamvu na kuonekera kwa ambuye athu Yesu Khristu. koma tenzeli mboni ya ukulu wake. 17 Chifukwa analandira kwa Mulungu atate ulemu na ulemelero pamene mau yanaletewa kwa yeve na mphamvu za Mulungu kukamba ati, "uyu ni mwana wanga, okondewa wanga, wamene nikondwera nayeve." 18 Tinamvera mau aya yamene yanachoka kumwamba, pamene tinali nayeve pa lupiri loyera. 19 Tili na mau aya ya uneneri yosimikizirika. Muzachita mushe ngati mwamvera. Ili ngati nyale yowala younika mu m'dima kufika kuseni na nyenyezi ituluka mu mitima yanu. 20 Muzibe ichi poyamba, ati palibe uneneri wamene uli na kutantauzila kwa kaena. 21 palibe uneneri wamene umabwera pa chifuniro cha munthu. Koma banthu bamene banatengewa na mzimu oyera banamvera kwa Mulungu.