Mutu 3

1 Manje muchaka cha eitini cha Jehoshphat mfumu ya Yuda, Joram mwana mwamuna wa Ahab anayamba kulamulila Israyeli mu Samaria; ana lamulila zaka twovu. 2 Anachita voipa pamenso ya Yahwe, koma osati monga batate bake naba mai bake; niichi anachosa chimwala choyofya chamapilala cha Baal chamene banapanga batate bake. 3 Anagwilila machimo ya Jeroboam mwana mwamuna wa Nebat, wamene analengesa Israyeli kuchimwa; sana chokeko kuliyeve. 4 Manje Mesha mfumu ya Moab mwana wambelele.Anapasa mfumu waba Israyeli 100,000 bana ba mbelele. 5 Koma kucoka pameme Ahab anafela, mfumu ya Moab analeka ku nvelela mfumu ya Israyeli. 6 Manje mfumu Joram anachoka ku Samaria nthawi kuti akalimbise Israyeli yonse kuti ichite nkondo. 7 Anatuma mau kuli Jehoshaphat mfumu ya Yuda, kukamba, "Mfumu ya Moab yaniukila ine. Uzayenda naine mu nkondo yomenyana na Moab?" Jehoshaphat anayanka, "Nizayenda. Nili mwamene mulili, banthu banu nibanthu banga, mohosi yanga ni mahosi yanu." 8 Ndipo anakamba, "Tizamumenya mu njila bwanji?" Jehoshaphat anayanka, "Munjila yanu nsanga mwa Edom." 9 Mwaicho mfumu waba Israyeli anayenda na mfumu waba Yuda na mfumu waba Edom. Bana zunguluka masiku seveni, ndiponso kunalibe manzi yaba nkondo olo vinyama vinayenda na beve. 10 Mwaicho mfumu waba Israyeli anakamba, "Nichani ichi? Kodi Yahwe aitana mfumu zitatu kubapasa mumanja mwa Moab?" 11 Koma Jehoshaphat anakamba, "Kulibeko mneneli wa Yahwe pano, kuti tifunse Yahwe kupitila muli eve?" Umozi wa nchito wa mfumu wa Israyeli anayanka naku kamba, Elisha mwana mwamuna wa Shaphat ali pano, wamene anatila manzi pamanja pa Elia." 12 Jehoshaphat anakamba, "Mau ya Yahwe yali naeve." Mwaicho mfumu wa Israyeli na mfumu wa Edom banayenda naye. 13 Elisha anakamba kuli mfumu wa Israyeli, "Nichani cheninga chite naiwe? Yenda kuli mneneli waba tate bako naba mai bako." Mwaicho mfumu wa Israyeli anakamba kuli eve, "Awe, chifukwa Yahwe anaitana ma mfumu yatatu pamozi kuba pasa muma manja mwa Moab." 14 Elisha anayanka, "Monga Yahwe wamoyo, naimilila pasogolo pake, ngati sinapase ulemu wa Jehoshaphat mfumu wa Yuda, sininga kuikeko nzelu olo naku kulanga. 15 Koma manje niletele oyimba, "Ndiye ichi chinapita pamene oyimba analiza, kwanja ya Yahweina bwela pali Elisha. 16 Anakamba, "Yahwe akamba ichi, 'Panga mumana uyu oyuma. 17 Nichifukwa Yahwe akamba ichi, 'Simuza ona kavuluvulu olo nvula, koma mumana uyu uza zula zula namanzi, ndipo muzamwa, imwe na zibeto zanu na nyama zanu zonse.' 18 Ichi sichintu chovuta pamnso ya Yahwe. Ndiponso azakupasani ulemelelo pali ma Moabite. 19 Muza menya aliyense olimbisa muzinda na yonse yabwino, mujube chimutengo chili chonse cha bwino, mulekese manzi kuyenda, na kuononga malonyalin yonse ya bwino namyala." 20 Mwaicho kuseni nthawi yo pasa chopeleka kuna bwela manzi kuchokela ku Edom; chalo cnenzeli fulu na manzi. 21 Manje pamene bonse ma Moabite kuti mfumu anabwela kuchita ndeo na beve, bana sonkana pamonzi, bonse banakwanisa kuvala vovala va nkondo, ndipo bana imilila pa malile. 22 Bana uka kuseni nazuba yenzeli kusanika pamanzi. Pamene ma Moabite banaona manzi ku mbali kwabo, yana oneka redi monga magazi. 23 Bana punda, "Aya nimagazi! Mafumu yaonongewa, naku payana! Manje, Moab, leka tiyende kuba menya!' 24 Pamene bwela ku msonkano wa Israyeli, ba Israyeli bana nyamuka nakumenya ma Moabite, bana mbuluka pasogolo pabo. Ba nkondo ba Israyeli ku bapisha ba Moabite pakati pa malo. 25 Bana ononga mzinda, napa malo pabwino ponse mwamuna aliyense anatema myala mpaka pana valiwa. Bana lekesa manzi kupita naku juba vimitengo va bwino vonse. Kir Hareseth chabe nde anasala na chi mwala. Koma ma soja ba nkondo navomenyela anabazungulila naku menya. 26 Pamene mfumu wa Moab kuti bana luza ndeo, anatenga bamuna bama naifi bali seveni handiredikuti bangene kuti bangene kuli mfumu wa Edom, koma bana kangiwa. 27 Ndiye anatenga mwana wake mwamuna wamene afunika ku langanile ku choka eve, naku mupasa nsembe yo shoka ku chipupa. Mwaicho kunali ukali pakati paba Israyeli, ndipo ba tuimiki ba Israyeli bana basiya mfumu Mesha naku bwelela ku malo yabo.