1
Kotero, pamene sitinakwanise kuchisunga, tinaona chinali bwino kutisiya ku athens teka.
2
Tinatuma timoteyo, m'bale wathu na ogwira naye nchito mwa mulungu mu uthenga wa khristu, kuti akulimbiseni nakuku tonthozani mu chikhulupiliro.
3
Tinachita izi kuti winangu asagwedezeke na mabvuto awa. chifukwa inu muziba kuti pa ichi tinasankhidwa.
4
Zoonadi, pamene tinali na inu, tinakuuzani poyamba kuti tinali kufunika kubvutika, ndipo izi zinachitika, monga muziba.
5
Mwa ichi, pamene sininakwanise kuimilira, ninatuma kuti nizibe za chikulupiliro chanu. mwina oyesa uja anakuyesani mu njira ina yake, na nchito yathu inali yopanda phindu.
6
Koma timoteyo anabwera kuchoka kwa inu na kuleta kwa ise uthenga wabwino wa chikulupiliro na chikondi. anatiuza kuti mumatikumbukira, na kuti mufuna kutionanso monga mwamene ise tifunila kukuonani.
7
chifukwa cha ichi, abale, tinatonthozedwa chifukwa cha chikulupiliro chanu, mumabvuto yathu yonse na kunzunzidwa.
8
tsopano tili na moyo, ngati muimilira mwa ambuye.
9
nimatokozo ya bwanji yamene tingapase mulungu pa inu, pa chimwemwe chonse chamene tili nacho pamenso pa mulungu cha inu?
10
usiku na muzuba timakupemphelerani na mphamvu kuti tione nkhope yanu na kukupasani chamene chipelebera pa chikulupiliro chanu.
11
lekani mulungu atate athu yeve, na ambuye yesu, atipase njira yofika kwa inu.
12
mulungu akupangiseni kuti mukule mu chikondi cha wina na mnzake na banthu bonse, mwamene naise tichitira kwa inu.
13
alimbise mitima yanu, kuti yankhale yopanda zodesa mu chiyelo pa menso pa mulungu atate, pa kubwera kwa ambuye yesu na bonse boyera.