1
Inu mweka muziba, abale, kuti kubwera kwathu kwa inu sikunali kopanda nchito.
2
Muziba kuti tinabvutika poyamba komanso tinachitisidwa manyazi ku afilipi. tinali olimba mwa mulungu wathu kulankhula nanu za mau ya mulungu mobvutikila.
3
chifukwa kuyamikidwa kwathu sikunali kwangozi, kapena kwa kudesedwa, kapena kwa chinyengo.
4
Mumalo mwake, monga mwamene mulungu watiyeneleza kuti tikhale okulupilika mu mau ya mulungu, kuti tikambe. tikamba, osati kuti tikondwerese banthu, koma kuti tikondwerese mulungu. niwamene amaona mitima yathu.
5
Sitimagwiritsa nchito mau yoipa pa nthawi ina iliyonse, monga muziba, kapena kamba ka kukumbwila. chifukwa mulungu ndiye mboni yathu.
6
Kapena tinapempha ulemelero kuchoka ku banthu, kwa inu kapena benangu. tinakafuna ukondeledwa monga atumwi ba khristu.
7
Mumalo mwake, tinali odekha mtima pakati panu monga muzimai atonthoza ana ake.
8
Mu njira iyi tinali na chikondi na inu. tinali okondwa kugawana na inu osati thenga chabe wa mulungu komanso miyoyo yathu. chifukwa munankhala okondwedwa kwambiri kwa ife.
9
Pakuti mukumbukira, abale, nchito yathu na kubvutika kwathu. usana na usiku tinali kugwira nchito kuti tisamibwezeni kumbuyo. pa nthawi ija, tinalalikira kwa inu uthenga wa mulungu.
10
Ndimwe mboni, na mulungu, mwamene mulili oyera, opanda chilema, komanso oliungama tinankhala bwino kwa inu okulupilika.
11
Mu njira imozi-mozi muziba mwamene tinankhalira na wina aliyense monga atate achitira na bana bake, tinali kukupapatirani na
12
Kukulimbikisani na kukupemphani kuti muyende munjira yoyenera pamenso pa mulungu, wamene anamuitanani mu ufumu wake.
13
Mwa ichi tiyamika mulungu mosalekeza. chifukwa pamene munatilandira uthenga wa mulungu wamene munamvera kuchoka kwa ise, munayalandira osati monga mau ya munthu. mumalo mwake, munayandila mwamene yalili, mau ya mulungu. ni mau yamene aya yamene yagwira nchito pakati panu okulupilira.
14
Kwa inu, abale, munankhala okonkha ba mipingo ya mulungu yamene yali ku yudeya mwa khristu yesu. chifukwa naimwe munabvutika zinthu zimozi kuchoka ku anthu bamozi-mozi, mwamene banachitira bayuda.
15
Ni bayuda bamene banapaya ambuye yesu na baneneri. ni bayuda bamene banatipisha. sibakondweresa mulungu. mumalo mwake, bali na nkhanza ku banthu bonse.
16
Batilesa kukamba na bamitundu kuti bapulumuke. chosatira ni chakuti bapakisa machimo yao. chilango chiyenera kufika pa iwo pothera.
17
Ndise opatulidwa kwa inu, abale, kwa ka nthawi kang'ono, muthupi osati mu mutima. ndise okonzeka, na kufunisisa, kuona nkhope yanu.
18
Chifukwa tinafunisisa kubwera kwa inu, ine , paulo, nafuti, koma satana anatilesa.
19
Chiyembekezo chathu cha kusogolo ni cha bwanji, kapena chimwemwe, kapena kolona yotikondweresa pamenso pa ambuye yesu pa kubwera kwake? si inu na benangu?
20
Chifukwa ndimwe chimwemwe na ulemelero wathu.