Mutu 1

1 Paulo, Silvano, na Timoteyo ku mpingo wa ku Tesalonika mwa Mulungu Atate na Ambuye Yesu Kristu. Chisomo na mtendere unkale na imwe. 2 Timayamikila Mulungu nthawi zonse chifukwa cha imwe, pamene tikamba za imwe muma pemphero yatu. 3 Tikumbukila mosalekezela pamaso pa Mulungu nchito zanu za chikulupiliro, nchito za chikondi, na kuleza mutima koma futi chisimikizo cha msogolo mwa ambuye wathu yesu khristu. 4 Abale okondedwa ni ambuye, tiziba bakusankhani inu, 5 Chifukwa cha uthenga wa mulungu unaza kwa inu osati mu mau chabe komanso mu mphamvu, ya Muzimu Oyera, na chisimikizo cha mphamvu. chimozi-mozi, muziba tinali banthu ba bwanji pakati panu chifukwa cha inu. 6 munankhala olondola bathu komanso ba ambuye, pamene munalandira mau mumabvuto yambiri mokondwa kuchoka kwa muzimu oyera. 7 Mwa ichi, munankhala chisanzo kwa onse ku macedonia ni achaia bamene banakulupilira. 8 Chifukwa kwa inu mau ya ambuye yamveka, osati ku macedonia ni achaia. mumalo mwake, kumalo yaliyonse chikulupiliro chanu mwa mulungu chasila. mwa ichi, sitifunika kukamba kalikonse. 9 chifukwa beve beka bakamba kuti tinali banthu ba bwanji pamene tinali kubwera pakati panu. bakamba mwamene munabwerea kwa mulungu kuchoka ku mafano kutumikila mulungu wa moyo na wa zoona. bakamba kuti 10 muyembekeza mwana wake kuchoka ku mwamba, wamene anamuukisa kwa akufa. uyu ni hyesu, wamene atitabisa ku zowawa zamene zizabwera.