Mutu 14 8

1 Pamenepo Solomo anasonkanisa bakulu ba Israyeli, na bonse basogoleli ba mitundu, na basogoleli ba mabanja ya bana ba Israyeli, pamenso pake ku Yerusalemu, kuti akabwelese likasa ya chipangano cha Yehova kuchokela ku Mizinda ya Davide, ndiyo , Ziyoni. 2 Bamuna bonse ba Israeli banasonkana kwa Mfumu Solomoni ku madyelelo, mumwezi wa Etanimu, wamene ni mwezi wachisanu namba seveni. 3 Bakuluakulu bonse ba Israeli anabwela, na bansembe bananyamula likasa. 4 Bananyamula likasa la Yehova, mutenti yokumanilamo, na vopangiwa vonse vopatulika vamene vinali mutenti. Bansembe na Balevi banabwelesa izi. 5 Mfumu Solomoni na bosonkana bonse ba Israeli banasonkana pasogolo pa Likasa, kupeleka nkosa na ng'ombe zamene sibanakwanise kuzipenda. 6 Bansembe banangenesa likasa la chipangano cha Yehova kumalo yake, ku chipinda chamukati cha munyumba, Malo yoyela yopambana, pansi pa mapipiko ya Akerubi. 7 Chifukwa Akerubi banatambasula mapipiko yawo kumalo kwa Likasa, na kuvininkila Likasa na mitengo yake yonyamulila. 8 Mitengo inali itali kwambili chakuti kosilizila kwake yanali kuonekela kuchokela kumalo yoyela kusogolo kwa chipinda chamukati, koma siyanali kuonekela panja. yalipo mpaka lelo. 9 Munalibe kantu mulikasa koma chabe minyala ibibli yamene Mose anaikamo ku Horebe, pamene Yehova anapanga chipangano na bana ba Israyeli, pamene banachoka muziko ya Aigupto. 10 Panali kuti pamene bansembe banachoka mu malo yopatulika, kumbi inazula mu tempele ya Yehova. 11 Bansembe sibanakwanise kuimilila chifukwa cha kumbi, chifukwa ulemelelo wa Yehova unazula mu nyumba yake. 12 Pamenepo Solomoni anati, "Yehova akamba kuti azankala mumdima otikama, 13 koma nakumangila malo, malo yako yonkalamo muyayaya." 14 Ndipo mfumu inapindamuka na kudalisa bonse mupingo wa Isiraeli, pamene mupingo bonse wa Isiraeli unali woimilila. 15 Anakamba kuti, Alemekezeke Yehova Mulungu wa Israyeli, wamene anakamba na Davide tate wanga, na kukwanilisa na manja yake, kuti, 16 Kuyambila siku yamene ninachosa bantu banga Israyeli mu Aigupto, sininasanke muzinda kuchoka mumitundu yonse ya Israeli kuti amange nyumba, kuti zina yanga linkale pamenepo. Mwaichi, ninasankha Davide kuti alamulile banthu banga ba Israeli. ' 17 Manje chinali mumutima wa Davide tate wanga ndi mtima womangira nyumba dzina la Yehova Mulungu wa Israyeli. 18 Koma Yehova anati kwa atate wanga Davide, Popeza munali mumutima mwanu kuti mumange nyumba pa zina yanga, munachita bwino kuli ichi mumitima mwanu. 19 Koma iwe suizamanga nyumba; Mumalo mwake, mwana wako wamwamuna, wamene azakabadwa mumusana mwako, azakamanga nyumba pa zina yanga. ' 20 Yehova wakwanilisa mawu yamene anakamba, chifukwa nanyamuka mumalo mwa Davide batate banga, ndipo ninkala pamupando wachifumu wa Israyeli, monga Yehova anakamba. 21 Namanga nyumba mu zina ya Yehova, Mulungu wa Israyeli. Napanga malo ya likasa kwamene kuja, mwamene muli chipangano cha Yehova, chamene anapangana na makolo bathu pobachosa muziko ya Aigupto. 22 Solomoni anaimilila pasogolo pa guwa ya bansembe ya Yehova, pamenso pa banthu bonse ba Israyeli, natambasulira manja ake kumwamba. 23 Iye anati, "Yehova, Mulungu wa Israeli, palibe Mulungu wina monga imwe kumwamba kapena pansi pano wamene amasunga chipangano chake na bakapolo banu bamene bamayenda pamenso panu na mutima wabo bonse; 24 Imwe bamene mwasunga pamozi na mutumiki wanu Davide batate banga, vamene munamulonjeza. Zoona, munakamba na kamwa kanu ndipo mwakanilisa na kwanja kwanu, monga chili lelo. 25 Manje, Yehova Mulungu wa Israyeli, chitani zamene munalonjeza mutumiki wanu Davide tate wanga, pamene munakamba kuti, Siuzasoba kunkala na muntu pamenso panga wakunkala pa mupando wachifumu wa Israyeli, ngati chabe bana bako basamala mu kuyenda pasogolo panga, monga wayendela pasogolo panga.' 26 Manje, Mulungu wa Israyeli, lekani mau yanu yasimikizike, yamene mwayakamba kuli Davide mutumiki wanu tate wanga. 27 Ushe Mulungu nizoona azankala paziko lapansi? Onani, thambo yonse na kumwamba sikungankhale kukukwanisani imwe-nanga kuli bwanji kwa iyi tempele yamene namanga! 28 Ndipo lemekezani pempelo ya mutumiki wanu na kufuna kwake mozichepesa, Yehova Mulungu wanga; nvelani kulila na pempelo yamene mutumiki wanu apempela pamenso panu lelo. 29 Lekani Menso yanu yankhale yoseguka pali iyi tempele usiku na mu kukachisi uyu usiku na muzuba, kumalo yamene mwane kuti, Zina langa na kunkhalapo kwanga kuzankhala kwamene kuja, kuti mumvele mapemphelo yamene mutumiki wanu azapemphela pali yano malo. 30 Sopano mvelani pempelo y yozichepesa ya mutumiki wanu na banthu banu ba Israeli pamene tikupemphelela pamalo yano. Zoona, mvelani kuchokela kumalo kwamene munkala, kuchoka ku mwamba, ndipo mukanvela, kululukilani. 31 Munthu akachimwila munzake wapafupi na akufunika kulapila chipangano, ndipo ngati abwela na kulapila chipangano pasogolo pa guwa yanu yansembe munyumba ino, 32 mvelani kuchokela kumwamba na kuchita kantu. Weluzani bakapolo banu, kuweluza wosalungama na kuleta zamene achita pamutu wake. Muzikamba babwino kuti wosalakwa na kumupasa monga mu kuyela kwake. 33 Pamene banthu bako ba Israeli bagonjesedwa kuli badani chifukwa bakuchimwilani imwe, ngati batenukila kuli imwe, kukambilila pa zina yanu, nakupempela, nakufuna ubwino wanu mu tempele ino- 34 napapata nvelani kuchoka mumwamba na kukulukilila uchimo wa banthu banu ba Israeli; babweleseni futi kumalo yamene munapasa makolo yawo. 35 Pamene thambo yavalika ndipo kulibe mvula chifukwa banthu bakuchimwilani — ngati bapemphela bakalangana pamalo yano, kukamilila pa zina yanu, na kuchoka ku machimo yawo pamene mwabavutisa- 36 pamenepo mvelani kumwamba na kukululukila chimo ya mutumiki wanu na banthu banu ba Israeli, pamene mwabapunzisa njila yanu yabwino yamene bafunika kuyendamo. Tumani nvula pamalo yanu, yamene mwapasa kuli banthu banu monga cholowa chawo. 37 Tiyelekeze kuti muziko mwanu muli njala, kapena ngati muli matenda, chimphepo kapena kachilombo, zombe kapena malasankhuli; kapena kuti ngati mudani aukila zipata za muzi muziko yao, kapena kuti pali mulili uli wonse kapena matenda; 38 ndipo nichani ngati mapemphelo na zopempha zichokela kwa munthu, kapena na banthu banu bonse ba Israyeli, ali bonse aziba mulili wamene uyo mumutima mwake; atambasula manja yake kuyangana ku tempele iyi. 39 Ndipo mvelani kuchokela kumwamba, kumalo kwamene munkala, khululukilani na kuchitapo kanthu, ndipo bwezelani munthu aliyense pali vonse vamene achita; muzina mutima wake, chifukwa imwe ndipo imwe chabe muziba mitima ya bonse banthu. 40 Chitani izi kuti bakuyopeni masiku yonse yamene bazankhala mu malo yamene munapasa makolo yawo. 41 Komanso mulendo wonkhala pakati pa banthu banu ba Israeli: bakabwela kuchokela ku ziko yakutali chifukwa cha zina lanu, 42 chifukwa bazamvela za zina yanu yaikulu, na zanja yanu yamphamvu, na mukono wanu wokwezedwa, pamene babwela na kupemphela kuyangana ku tempele iy, 43 napapata mvelani kuchokela kumwamba, kumalo kwamene munkala, na kuchita chilichonse chamene mulendo akupempani imwe. Chitani ichi kuti banthu bonse paziko lapansi bazibe zina yanu na kukuopani, monga mwamene mumachitila banthu banu ba Israeli. Chitani ichi kuti bazibe kuti nyumba iyi yamene namanga iyitaniwa pa zina yanu. 44 Tiyelekeze kuti anthu anu apita kukamenyana na mudani, kudzera njira iliyonse yomwe mungatumize, ndipo akuganiza kuti akupemphera kwa inu, Yehova, kumzinda umene mwasankha, komanso kunyumba imene ndamangira dzina lanu. 45 Kenako mverani kumwambako pemphero lawo ndi pempho lawo, ndipo athandizeni pa zomwe akuchita. 46 Tiyelekeze kuti bakukuchimwilani, popeza palibe wamene samachimwa, ndipo muganiza kuti mwabakwiyila nakubapeleka mumanja mwa badani, kotelo kuti mudani wamene uyo azabatenga ukapolo kuziko yawo, ngakhale kutali kapena pafupi. 47 Ndiye ganizilani kuti bakumbukila kuti bali muziko yamene banatengewa ukapolo, nakuganiza kuti balapila nakupempha chifundo kwa imwe kuchokela kuziko ya bamene banabatenga. Tiyelekeze kuti banakamba, 'Tachita zolakwa ndipo tachimwa. Tachita vinthu voipa. ' 48 Tiyelekeze kuti abwelela kwa inu na mitima yabo bonse na moyo wabo bonse mu ziko ya badani bawo bamene banabapoka, ndipo ngati bapemphela kwa imwe kusata ziko yawo, yamene munapasa makolo yawo, na muzinda wamene munausankha , na kunyumba yamene ndamangamo zina yanu. 49 Pamenepo kuchokera kumwamba, kwamene imwe munkala, mvelani imwe pemphero yabo na chopempa chabo kupempa tandizo, ndipo muzabalungamisa. 50 Mukululukire banthu banu bamene banakuchimwirani, na volakwa vawo vonse vamene banakulakwirani, ndipo mubachitire chifundo pamenso pa bamene bawagwira, na kubachitira chifundo bamene banabagwira. 51 Iwo ni banthu banu bamene munabasankha, bamene munawapulumutsa ku Iguputo ngati kuti mukuwotcha chitsulo. 52 Maso anu yakhale otsegukila pempho la ine mtumiki wanu, na zopempha za banthu banu Israyeli, kuti muwamvere iwo, pamene iwo alira kwa inu. 53 Pakuti munawapatula pakati pa anthu a mitundu yonse ya paziko lapansi yankhale banu, na kulandila malonjezano anu, monga umo munalongosolela na Mose mtumiki wanu, m'mene munaturutsa makolo athu m'Aigupto, Ambuye Yehova. 54 Ndipo kunali pamene anasiliza Solomoni kupemphela pemphelo ili lonse ndi kupemphera kwa Yehova, anauka pasogolo pa guwa la nsembe la Yehova, atagwada pansi, ndi manja ake atatambasulira kumwamba. 55 Iye anayimirira ndi kudalitsa mpingo wonse wa Israeli mofuwula, 56 nati, "Alemekezeke Yehova, amene wapatsa anthu ake Aisraeli mpumulo mwa kusunga malonjezo ake bonse. Palibe mawu amodzi omwe sanakwaniritsidwe pa malonjezo onse yabwino ya Yehova na Mose mutumiki wake. 57 Lekani Yehova Mulungu wathu ankhale naife monga anachitila na makolo bathu. 58 Asatisiye kapena kutitaya, kuti atembenukile mitima yathu kwa iye, kuti tikonke njila zake zonse, na kusunga malamulo yake, na malemba yake, yamene analamulila makolo yathu. 59 Vomelezani mawu aya nakamba, yamene napempha pamenso pa Yehova, yankale pafupi na Yehova Mulungu wathu usana na usiku, kuti atandize pa nchito ya mutumiki wake na mulandu wa anthu ake Israyeli, monga zifunikila siku na siku; 60 kuti anthu onse ya ziko lapansi bazibe kuti Yehova ndiye Mulungu, ndipo palibenso Mulungu wina; 61 Potero mutima wanu ukhale wokhulupirika kwa Yehova Mulungu wathu, kuyenda mumalemba ace, ndi kusunga malamulo ake, monga lero. " 62 Mwaichi mfumu na bonse Israeli bonse pamozi naye anapeleka nsembe kwa Yehova. 63 Solomo anapereka nsembe yoyamika kwa Yehova: ng'ombe zikwi makumi awili mphambu zibilii, na nkhosa 120,000. Momwemo mfumu na bana bonse ba Israyeli banapatula nyumba ya Yehova. 64 Pa siku yamene iyo mfumu inapatula pakati pa bwalo pasogolo pa tempele ya Yehova; pakuti pamenepo anapeleka nsembe zopseleza, na nsembe za mbeu, na mafuta ya nsembe zoyamika; zing'onozing'ono kulandila nsembe yopseleza, nsembe yambewu, ndi mafuta a nsembe zoyamika. 65 Pamenepo Solomoni anachita madyelelo pantawi yamene iyo, naba Israyeli bonse nayeve, musonkano waukulu, kuyambila ku Lebano Hamati kufikila ku musinje wa Aigupto, pamenso pa Yehova Mulungu wathu masiku yali seveni na yenangu masiku yali seveni, pamozi nimasiku yali fotini. 66 Pa siku lachisanu na chitatu anabatuma bantu kuti bapite, ndipo beve banadalisa mfumuyo na kupita kwawo na chimwemwe na mitima yokondwa chifukwa cha zabwino zonse zimene Yehova anachitira Davide mutumiki wake, na Israeli, bantu bake.