6

1 Ndipo Solomoni anayamba kumanga nyumba ya Yehova. Vinachitika mu chaka cha 480 kuchokela pamene bana ba Israeli banachoka muziko ya Igipto, mu chaka chachinayi ya ulamulilo wa Solomoni mu Israeli, mu mwezi wa Zivi, yamene ni mwezi wachibili. 2 Tempele yamene Mfumu Solomoni anamangila Yehova inali mikono 60 utali, mikono 20 ufupi, na mikono 30 kutalimpa kwake. 3 Malo yo mangiwa yamu mbali yachipinda kusogolo kwa chipinda chikulu cha tempele inali mikono 20 utali, kulingana na ufupi ya nyumba iyo. 4 Pa nyumba anapanga mazenela yama fulemu yamene yanalengesa kuti yachepa kunja kuchila mukati. 6 5 Pamakoma ya chipinda yachikulu anamangamo chipinda chozunguluka ponse pa chipinda chakunja na chamukati. Anamanga chipinda chozungulila mumbali yonse. v6 Chipinda yapansi kwambili inali mikono 5 ufupi, yapakati inali mikono 6 ufupi, ndipo yachitatu inali mikono 7 ufupi. Pakuti kunja anamangamo vomangila pakhoma ya nyumba kuzungulila kuti mapulanga asazi ngena muvipupa va nyumba. 7 Nyumba inamangiwa na miyala yokonzewa pamwala. Kunalibe chongo cha sando, nkhwangwa, kapena chida chilichonse pamene inali ku mangiwa. 8 Kumbali ya kumwela ya tempele ija kunali po ngenela pa malo, wina anakwela na masitepu yapakati, kuyambila pakati kufikila pa wachitatu. 9 Solomoni anamanga tempele nakusiliza; Eve ana vinikila nyumba na mapulanga na mapulunga ya sida. 10 Eve anamanga chipinda vambali voyanganana na chipinda chamukati cha nyumba, mu mbali iliyonse kutalimpa kwake mikono isanu; anazigwilizana ku nyumba na mapulanga ya sida. 11 Mau ya Yehova yanabwela kuli Solomoni, kuti, 12 "Pokomba pali tempele yamene umanga, ukayenda mumalembaba yanga, na kuchita chilungamo, kusunga malamulo yanga yonse, nakuyakonka, pamene apo nizaika lonjezo yanga na iwe, yamene ninapangana na iwe na Davidi tate wako 13 Nizankala pakati pa bana ba Isiraeli ndipo sinizabasiya." 14 Mwaicho Solomoni anamanga nyumba nakuyisiliza. 15 Mukati anamanga makoma yamukati ya nyumba na mapulanga ya sida. Kuyambila pansi pa nyumba mpaka kumwamba, anavala mukati na mapulanga, ndipo pansi pake anavala na mapulanga ya cypress. 16 Anamanga mikono 20 kumbuyo kwa nyumba na mapulanga ya mukuguza pansi mpaka kumwamba. Eve anamanga chipinda chino kukhala chipinda chamukati, malo oyela maningi. 17 Chipinda chachikulu, ndiye kuti, malo yopatulika yomwe yanali kusogolo kwa malo yopatulikisa,yanali mikono 40 utali. 18 Mukati mwa nyumba munali mitengo ya mukunguza, yobezewa mooneka monga mphonje na maluwa otseguka. Zonsezi zinali mkungudza mkati. Palibe mwala womwe unkawoneka mkati.