Chapta
1
Pamene Sauli anabwelela kuchoka kuputikisa ma Philisitina, anauziwa kuti ''Davide ali mu sanga yaku Enigedi''
2
Ndipo Sauli anatenga wanthu wali thiri sauzande amuna osankhindwa kuchokela kuli Israeli yonse,nakuyenda kusakila Davide na banthu wake ku myala ya Mbuzi zamusanga.
3
Anabwela kunakhola yankhosa munjila, pamene panali khevu. Sauli anangena mukati kuti avirunkhile mendo yake. Apa Davide na banthu wake anali nkhale kothela kwa khevu.
4
Banthu wa Davide anati kuli eve, ''Lyi ndiye siku yamene Mulungu anakambapo pamene anati kuli iwe, 'Nizapeleka badani bako mu manja yako, pakuti iwe uchite naye mwamene ufunila.''' Apo Davide ananyamuka nakukalaba mwakachetechete kuyenda pasogolo nakujuwa kona ya mukhanjo wa Sauli.
5
Pasogolo pake Davide anavela mitima kuwawa chifukwa anajuwa nsonga ya mukhanjo wa Sauli.
6
Anati kuli banthu bake,'' Mulungu asachilole kuti ningachite ichi chinthu kuli mbuye wanga,wozozedwa wa Yehova, kutambulula kwanja yanga momuchita chipongwe,nitaona kuti niwozozedwa wa Mulungu.
7
Apo Davide anawazuzula wanthu wake na aya mau,ndipo sanawalole kumuyamba Sauli. Sauli ananyamuka,nakuchoka mu khevu,nakuyenda kwao.
8
Pasogolo pake Davide naye ananyamuka,nakuchoka mu khevu,nakuyitana mokuwa mbuyo mwa Sauli; ''Ambuye wanga mfumu,''pamene Sauli anayang'ana kumbuyo kwake, Davide anawelama nankhope yake pansi nakuonesa ulemu.
9
Davide anati kuli Sauli, ''Nchifukwa chani mumamvelela wanthu wamene wakamba kuti, 'Onani, Davide afuna kukuchitani choyipa?'
10
Lelo menso yanu yawona mwamene Yehova enze akuyikani mumanja mwanga,pamene tinali mu khevu. Wenangu wenze waniuza kuti nikupayeni,koma wakulekelelani imwe,nakamba kuti,sini zatambasule kwanja yanga mochita chipongwe ambuye wanga, pakuti mwozozedwa wa Mulungu.
11
Onani,atate wanga,onani nsonga ya mukhanjo wanu mumanja mwanga. Pa chifukwa chazoona kuti najuwako nsonga ya mukhanjo wanu nakusakupayani,imwe mungaziwe nakuona kuti kulibe choyipa kapena mulandu wowukila usogoleli mumanja mwanga,ndipo sininakuchimumwileni,ngaukhale kuti imwe muzengela moyo wanga kuti munipaye.
12
Mulungu aweluze pakati pa imwe na ine,ndipo Mulungu azanibwezelamo kuli imwe m'malo mwanga,koma kwanja yanga sizakuchitani chipongwe imwe.
13
Monga mwambi wa wakudala ukamba kuti,'kunja kwa oyipa kumatuluka choyipa koma kwanja yanga siyizasusana na imwe.
14
Nindani wamene mfumu ya Israeli ya chokela kunja? Mupitikisa ndani? Mukonkha galu wakufa? Mupitikisa inda?
15
Mulungu ankhale woweluza ndipo apase chiweluzo pakati kaimwe na ine,nakuona kuti anikambilako zofuna zanga,na kunilola kuti nizwenge kuthawa kwanja yanu.''
16
Pamene Davide anasiliza kukamba aya mau kuli Sauli , Sauli anati , '' Nimau yako ayo , mwana wanga Davide ?'' Sauli anakweza mau yake nakulila.
17
Anati kuli Davide , ''Niwe olungama maningi kuchilapo ine , pakuti wanilipila chabwino ine , pamene ine ninakulipila choyipa.
18
Waulula lelo mwamene wachitila zabwino kwa ine , pakuti sinunanipaye pamene Yehova enze aniyika mu chifundo chako.
19
Pakuti ngati munthu apeza mudani wake angamusiye kuti ayende mumtendele ? Mulungu akulipile chabwino pa chamene wachita kwa ine lelo.
20
Apa , ine naziwa kuti iwe uzankhala zoona mfumu nakuti ufumu wa Israeli uzankhauzankhazikisiwa mumanja mwako.
21
Ulapile kwa ine kuti siuza juwa kusilizilatu mbadwo wanga wamene ukonkha ine nakuti siuza ononga zina yanga kuichosa pa banja ya batate wanga.''
22
Apo Davide analapa njazi kuli Sauli . Ndipo Sauli anayenda kwawo, koma Davide na wanthu wake anayenda kungaka yawo.