1
Kunali mwamuna winangu waku Ramathayimu wa mutundu wama Zufayite , wa ziko yakumutunda wa Efuremu ; zina yake anali Elukana mwana wa Jerohamu mwana mwamuna wa Eliwu mwana wa Towu mwana wa Zufu , wakumutundu wa chimasulidwe chamauuli na Ramathayimu Zofayimu, koma chimaziwika kuti Zofayimu iyimilila maningi malo mwamene mbadwo unachokela kwamene Zufu anaukhala.
2
Anali na azikazi abili ;zina ya woyamba anali Hanna , ndipo zina ya wachiwili inali Peninna . Peninna anali na wana , koma Hanna analibe loko mumozi .
3
Uyu munthu anali kuchokela ku tawuni ya kwao chaka na chaka nakubwela ku shilo kupembeza nakupeleka nsembe kwa Ambuye Yehova . Wana wamuna abili wa Eli , Hofini na Finiyasi , ansembe wa Yehova , anali kwameme .
4
Siku ikafika yakuti Elukana apeleke nsembe chaka chili chonse , nthawi zonse zigawo za nyama kuli Peninna mkazi wake , na kuli wonse wana wake wamuna nawakazi.
5
Koma kuli Hanna nthawizonse anali kupasa vambili maningi , pakuti anamukonda Hanna , mimba yake.
6
Pofuna kumuyamba , mkakazi mzake anali kumukalipisa kabili kabili , chifukwa Yehova anamuvala mimba yake .
7
Apo chake na chaka , akayenda ku nyumba ya Yehova na banja yako , mdani wake mpaka amukalipise . Nchifukwa chake anali kulilalila nakasadya kanthu.
8
Elukana mwamuna wake nthawi zonse anali kuti kwa yeve , ''Hanna , ulila chani ? Ulekelanji kudya ? Mtima wako ukunyililanji? Kodi ine sini pambana wana wamuna bali teu?''
9
Chinachitikapo siku inangu mwa imozi mwa aya masiku , Hanna ananyamuka watasiliza kudya nakumwa ku Shilo . Apa Eli wansembe enze anaukhala pa mupando wake wapa fupi na polowela mu tempile ya Yehova.
10
Enze anavutika kuchokela pansi pa mutima wake ; anapemphela kwa Yehova na kulila mokuwa mwaukali maningi.
11
Anapanga chipangano kuwana kuti , '' Yehova wa makawu , ngati muzayanganila kuvutika kwa kapolo wanu nakumukambukila mumutima mwanu , nakusamuyiwala kapolo wan , koma mumupase kapolo wanu mwana mwamuna , pasogolo pake ine nizamupasa kwa Yehova masiku onse amoyo wake ndipa kulibe kaleza kazaka kumyako mutu wake''.
12
Pamene anapitiliza kupembhera kwa Yehova , Eli anali kumuyang'ana pakamwa .
13
Hanna anali kukambila mumutima mwake . Milomo yake inali kunyang'anya koma mau yake siyanali kunveka . Apo Eli anaganiza kuti Hanna anali wokolewa.
14
Eli anamuwuza kuti , '' Uzankhala wokolewa mpaka liti ? uwuleke mowa wako.
15
Hanna anayankha , '' Iyayi abusa wanga, ndine muzimayi wa muzimu wokwinyilila . Sininamweko wayini loko munkhoyo ukali , koma nankhala nithila moyo wanga kwa Yehova.
16
Musamuganizile kapolo wanu kunkhala muzimayi wamusewanya ; nankhala nikamba kuchokela wuku khuziwa maningi nakavunduliwa''.
17
Apo Eli anayankha nakukamba kuti , '' Yenda mwanitendele ; Mulungu wa Isirayeli a funika akupase chamene wamupempha.''
18
Anayankha kuti, '' Lekani kapolo wanu apeze chifundo mumanso mwanu . '' Apo muzimayi anayenda kwawo na kudya ; nkhope yake siyinawoneke futi yokwiya.
19
Anauka m'mawamawa maningi nakupembeza Yehova , ndipo wanabwelela futi kunyumba kwao ku Roma . Elukana anagonana na mukazi wake , ndipo Mulungu anamukumbukila yeve.
20
Pamene nthawi inakwanila , Hanna anankhala namimba nakubala mwana mwamuna . Anamuyitana zina yako Samweli , kutanthauza kuti ,'' Chifukwa ninamumphepha kwa Mulungu.''
21
Nafuti , Elukana na wamunyiemba yake wonse wanayenda kukapeleka kwa Yehova nsembe ya chaka na chaka nakukalipila chilayo chake .
22
Koma Hanna sanayende , anati kuli mwamuna wake , ''Sinizayenda mpaka mwana akaleke kunyonkha ; ndiye pamene nizamuleta , kuti akaonekele pamenso pa Yehova nakunkhala kwamene kuja kwamuyaya.''
23
Elukana mwamuna wake anakamba kuti kuli yeve , '' Uchite chamene chikuwonekela bwino kwa iwe. Yembekeza mpaka ukamulumule ; chabe , leka Mulungu asimikize mau yake .'' Apo muzimayi uja anasala nakulela mwana wake mpaka kumulesakunyonkha.
24
Atamulesa kunyonkha , anamutenga pamozi na ng'ombe imuna yazaka zitatu, mpiwo umozi wa ufa , na botolo imozi ya wayini , nakumuleta kunyumba ya Yehova ku Shilo . Apa mwana enze akali m'ng'ono.
25
Anapaya ija ng'ombe imuna , nakumuleta uja mwana kuli Eli.
26
Anati , '' Oh , Abusa wanga ! Mukali na moyo , Abusa wanga , ndiwe mkazi uja wamene anayimilila pamene pano kupemphela kwa Yehova .
27
Ninapempha uyu mwana ndipo Yehova ananipasa yankho ya dandaulo yanga yamene ninamupempha.
28
Namupasa kwa Yehova , makoinga ali mamoyo niwobwelekewa kwa Mulungu .'' Chokonkhapo anapembeza Yehova pamene apo .