Mutu 1

1 Buku ya mubadwe wa Yesu Kristu, mwana wa Davidi, mwana wa Abrahamu. 2 Abrahamu anali tate wa Isaki, ndipo Isaki anali tate wa Yakobo, ndipo Yakobo anali tate wa Yuda na babale bake. 3 Yuda anali tate wa Pelezi na Zela kupitila muli Tamar, Pelezi tate wa Hezeloni, ndipo Hezeloni anali tate wake wa Ramu. 4 Ramu anali tate wake wa Aminadabu, Aminadabu anali tate wake wa Nashoni, and Nashoni tate wake wa Salimoni. 5 Salimoni anali tate wake wa Bowazi kupitila muli Rahabu, Bowazi tate wake wa Obedi kupitila muli Lute, Obedi tate wake wa Yesse. 6 Yesse anali tate wake wa Davidi mfumu, Davidi tate wake wa Solomoni kupitila mu mukazi wake wa Yuliya. 7 Solomoni anali tate wake wa Rehobowamu, Rehobowamu tate wake wa Abija, Abija tate wake wa Asa. 8 Asa anali tate wake wa Yehosafat, Yehosafat anali tate wake wa Yolamu, ndipo Yolamu kolo wa Uziya. 9 Uziya anali tate wake wa Jotamu, Jotamu tate wake wa Ahazi, Ahazi tate wake wa Hezekaya. 10 Hezekaya anali tate wake wa Manase, Manase tate wake wa Amoni, Amoni tate wake wa Josiya. 11 Josiya anali kolo wa Jokoniya na abale bake pa ntawi yo pelekewa ku Babiloni. 12 Kuchoka ntawi yopelekewa ku Babiloni, Yekoniya anali tate wake wa Shiyatiyewo, Shiyatiyewo anali kolo ya Zelubabewo. 13 Zelubabewo anali tate wa Abiyudi, Abiyudi tate wa Eliyakimu, ndipo Eliyakimu tate wa Azo. 14 Azo anali tate wa Zadoki, Zadoki tate wa Akimu, ndipo Akimu tate wa Eliyudi. 15 Eliyudi anali tate wake wa Eliyaza, Eliyaza tate wa Matani, ndipo Matani tate wa Yakobo. 16 Yakobo anali tate wake wa Yosefe mwamuna wa Maria, kupitila mwa eve Yesu anabadwa, wamene aitaniwa Kristu. 17 Mibadwe yonse kuchokela pali Abrahamu mpaka pali Davidi inali fourteen, kuchokela pali Davidi kufikila ntawi yopelekewa ku Babiloni inali mibadwe 14, ndipo kuchokela ntawi yotengewa ukapolo ku Babiloni kufikila ntawi ya Kristu inali mibadwe 14. 18 Kubadwa kwa Yesu Kristu kunachitika munjila iyi. Bamai bake, Maria, banakolobekewa kuti bakwatiliwe kuli Yosefe, koma basanabwele pamozi, banamupeza napakati kupitila muli Muzimu Oyera. 19 Koma Yosefe, mwamuna wake, anali muntu olungama sanafune kuti amuchitile manyazi poonekela, mwa ichi anali kufuna kuti amusiye mwa chisinsi. 20 Pamene eve anali kuganizila ivi vintu, mungelo wa Ambuye unamuonekela eve mu chiloto, nakukamba kuti, "Yosefe mwana wa Davidi, osayopa kutenga Maria kunkala mukazi wako, chifukwa eve wamene apelekewa mwa eve apelekewa na mu Muzimu Oyela. 21 Azabeleka mwana mwamuna, ndipo uzamupasa zina Yesu, chifukwa azapulumusa bantu bake kuchoka kuma chimo yao." 22 Ivi vonse vinachitika kuti vifikilise mau yanakambiwa na Ambuye kupitila mwa muneneli, kukamba kuti, 23 "Taonani, namwali azankala na pakati na kubeleka mwana mwamuna, ndipo bazamuitana zina yake kuti Imanuweli" -yamene tantauzo yake ni, "Mulungu ali naise." 24 Yosefe anauka kuchiloto chake na kucita vamene mungelo wa Ambuye unamuuza, nakumutenga kunkala mukazi wake. 25 Koma sanamuzibe kufikila pamene anabeleka mwana wa mwamuna. Ndipo anamuitana zina yake kuti Yesu.