Mutu 2

1 Pamene Yesu anabadwa mu Betelehemu mu malo ya Yudeya mu masiku ya Helodi mfumu, bamuna bopunzila bochokela ku mawa banafika mu Yelusalemu nakukamba kuti, 2 "Nanga alikuti wamene anabadwa Mfumu ya ba Yuda? Tinaona nyenyezi yake ku mawa nichifukwa chake tabwela kumupembeza." 3 Pamene Helodi mfumu anamvela ichi, anavutika mutima, na Yelusalemu yonse. 4 Helodi anaitanila pamozi bonse bakulu bansembe na bakalembela ba bantu, naku bafunsa kuti, "Nanga nikuti kwamene Kristu ayenela kubadwila?" 5 Bana muuza kuti, "Mu muzinda wa Betelehemu kudela ya Yudeya, chifukwa ichi ndiye chamene chinalembewa na muneneli, 6 'Koma iwe, Betelehemu, mumalo ya Yudeya, sindiwe ochepela pa basogoleri baku Yuda, chifukwa kuchoka kuli iwe kuzabwela olamulira wamene azasogolera bantu banga ba Israyeli. 7 Koma Helodi mwachisinsi anaitana bopunzila kuti abafunse ntawi yeni yeni pamene nyenyezi inaonekela. 8 Anabatuma ku Betelehemu, kukamba kuti, "Endani muka funisise mwana uyu moikako nzelu. Ngati mwamupeza, nileteleni mau mwakuti naine nibwele nimupembeze." 9 Pamene banasiliza kumvela mau ya mfumu, bana enda, ndipo nyenyezi yamene banaona kumawa inabasogolela kufikila pamene inabwela yaimilila pamalo pamene panali mwana wamungóno uja analili. 10 Pamene banaiona nyenyezi ija, banakondwela na chimwemwe chikulu maningi. 11 Banangena munyumba nakumuona mwana mungóno anali na Maria mai wake. Banagwa pansi nakumupembeza. Bana masula tuma tumba twabo naku mupasa mpaso za golide, frankincense, na mala. 12 Mulungu anaba chenjeza muchiloto kuti basabwelele kuli Helodi, chifukwa cha ichi banabwelela ku ziko yabo kusebenzesa njila inangu. 13 Pamene bana enda, mungelo wa Mulungu ana onekela kuli Yosefe muchiloto naku muuza kuti, "Uka, tenga mwana mungóno na mai wake, tabila ku Igupto. Nkalani kwamene kuja kufikila pamene nizakuuza, chifukwa Helodi azasakila mwana mungóno uyu kuti amu ononge." 14 Usiku wamene uja Yosefe anauka nakutenga mwana mungóno na mai wake naku enda ku Igupto. 15 Anankala kwamene kuja mpaka kufikila imfa ya Helodi. Ichi china fikiliza vamene Ambuye bana kamba kupitila mumuneneli, "Kuchokela ku Igupto naita mwana wanga." 16 Koma Helodi, pamene anaona kuti banamunama baja bantu bopunzila, ana kalipa maningi. Anatuma nakupaya bonse bana bamuna bamene banali mu Betelehemu na malo yonse yakuja bamene banali na zaka zibili nakubwela pansi, kukonkeleza ntawi yamene anaganizila pamene anakambisana nabopunzila. 17 Ichi chinafikilisa vamene vinakambiwa kupitila muli Yelemaya muneneli. 18 "Liu imveka ku Rama, kulila kwakukulu, Rakeyo ala bana bake, ndiposno akana kutontozewa, chifukwa bana bake basila." 19 Pamene Helodi anamwalila, onani, mungelo wa Ambuye unaonekela muchiloto kuli Yosefe mu Igupto naku kamba kuti, 20 "Uka tenga mwana na mai wake muyende ku ziko ya Israyeli, chifukwa baja bamene banali kusakila umoyo wamwana bamwalila. 21 Yosefe anaima, anatenga mwana na mai wake, naku bwela ku ziko ya Israyeli. 22 Koma pamene anamvela kuti Akelas anali kulamulila mu Yudeya mumalo ya tate wake Helodi, anagwiliwa na manta kuti ayendeko. Pamene Mulungu anamuchenjeza muchiloto, 23 ana enda kumalo ya Galili naku yenda kukankala mu muzinda oitaniwa Nazaleti. Ichi chinafikilisa chamene chinakambiwa kupitila muli muneneli, kuti azaitaniwa mu Nazaleni.