1
zitapita izi zinthu ninamvera chamene chinamveka kwati ni mau yampamvu ya banthu bambiri kumwamba kukamba ati, "hallelujah. chipulumuso, ulemelero na mpamvu zikhale kwa mulungu wathu.
2
chiweluzo chake ni chachilungamo na choona, cifukwa aweluza hule ya mpamvu yamene inasokoneza ziko la pansi na nkhalidwe yake ya uhule. wabwezera magazi ya akapolo ake, yamene iye anakhesa."
3
banakamba kaciwiri: "hallelujah! chusi chamene chichoka kwa yeve muyayaya."
4
akulu 24 na zamoyo 4 zinagwa pansi na kupembeza mulungu amene anali nkhale pa mpando wa chimfumu. banali kukamba ati, "zinkhale tero. hallelujah!"
5
elo mau yanachoka pa mpando wa mulungu, kunena kuti, "tiyamike mulungu wathu, inu onse akapolo ake, inu amene muyopa iye, onse opanda nchito na ba mpamvu.
6
elo ninamva chamene chinali ngati mau ya anthu ambiri, kwati ni chongo cha manzi yambiri, elo kwati ni chongo cha kugunda kwa kaleza, kunena kuti, "hallelujah! pakuti mulungu alamulira, mulungu wamene alamulira zinthu zonse.
7
tiyeni tikondwere na kunkhala okondwa na kumupasa ulemu chifukwa chisangalalo cha ukwati wa mwana wa nkhosa chafika, elo mkazi wa chikwati wakonzeka.
8
Analoledwa kuti abvale zovala zowala na zopanda dothi" (chifukwa zovala zopanda dothi ni zincito za anthu oyera).
9
mungelo anakamba kwa ine, "lemba izi: ni odala amene aitaniwa ku pwando la ukwati wa mwana wa nkhosa." anakamba futi kwa ine ati, "aya ni mau ya zoona ya mulungu."
10
ninagwa pansi pa mapazi ake kuti nimupembeze, koma anakamba kwa ine ati, "osachita tero! naine ndine kapolo kwati iwe na abale ako amene ali na umboni wa yesu. pembeza mulungu, pakuti umboni wa yesu ni muzimu wa uneneri."
11
elo ninaona kumwamba kuseguka, ninayangana kunali hosi yoyera. wamene analipo ni ozibika na zina yakuti okulupilika na wazoona. ni pa chilungamo kuti aweruza na kumenya nkhondo.
12
menso yake yali ngati muliro, elo pa mpumi pake pali makolona yambiri. ali na zina yolembewa pa yeve yamene kulibe amene aziba koma yeve yeka.
13
avala mukanjo wamene unafakiwa mu magazi, na zina lake ni mau ya mulungu.
14
basilikali ba kumwamba banali kumulondola pa mahosi yoyera, ovala zovala zabwino, zoyera elo zopanda dothi.
15
mukamwa mwake muchoka mupeni wakutwa wamene amenyera maiko, azalamulira maiko na mphamvu. anaponda mothwela mpesa mu kukalipa kwa mulungu wa mphamvu.
16
ali na zina yolembewa pa chovala chake na pa chibelo chake: "mfumu ya mamfumu na mbuye wa ambuye."
17
ninaona mungelo oimilira pa zuba. anaitana na mau yamphamvu ku nyoni zonse zouluka mumwamba, "bwerani, munkhale pamozi ku pwando la mulungu.
18
bwerani mudye matupi ya mamfumu, matupi ya akulu a nkhondo, matupi ya banthu ba mphamvu, matupi ya mahosi na bamene bakwerapo, na matupi ya banthu bonse, akapolo na omasuka, banthu bopanda nchito na ba mphamvu."
19
ninaona chilombo na mamfumu ba pa ziko lapansi na banthu babo ba nkhondo. banakumana kuti bamenye nkhondo na baja bali pa mahosi na bankhondo bake.
20
chilombo chinagwiliwa pamozi na mneneri waboza wamene anachita zodabwisa pamenso pake. na zizindikiro zamene izi ananamiza bonse bamene banalandira cizindikiro cha chilombo na bamene banapembeza chifano chake. bonse babili banaponyedwa mu nyanja ya muliro wa sufule.
21
benangu bonse banapaiwa na mupeni wamene unacoka mukamwa mwa uja wamene anali pa hosi. nyoni zonse zinadya matupi yawo.