1
Ninamvera mau amphamvu kuchoka mu tempile ya Mulungu kuuza angelo 7, "pitani muthire mbale 7 za mkwiyo wa Mulungu."
2
Mngelo oyamba anapita na kuthira mbale yake pa ziko; zilonda zoipa ni zobaba zinachoka pa anthu amene anali na chizindikiro cha chilombo, amene anapembeza fano lake.
3
Mngelo wachiwiri anathira mbale yake mnyanja. Inasanduka magazi, monga magazi ya munthu wakufa, ndipo chilichonse cha moyo mu manzi chinafa.
4
Mngelo wa chitatu anathira mbale yake m'misinje na nyenje za manzi ndipo zinasanduka magazi.
5
Ninamvera mgelo wa manzi kukamba ati, "ndinu oyera-amene aliko ndipo analiko, Oyera- chifukwa mwaweruza zinthu izi.
6
Chifukwa anathira magazi ya okhulupilira na aneneri, mwabapasa magazi kuti bamwe; ni zamene bayenera.
7
Ninamvera guwa kukamba ati, "Inde, ambuye Mulungu a mphamvu zonse, chiweruzo chanu ni ca zoona na cholungama."
8
Mngelo wa chinai anathira mbale yake ku zuba, ndipo inapasidwa chilolezo chotentha anthu na muliro.
9
Anatenthedwa na kupya kwakukulu, ndipo ananyoza zina la Mulungu, amene ali na mphamvu pa ziwawa zimenezi. Sibanalape kapena kumupasa ulemelero.
10
Mngelo wa cisanu anathira mbale yake pa mpando wa chilombo, ndipo mdima unaphimba umfumu wake. Anakukuta malilime ao chifukwa cha kuwawa.
11
Ananyoza zina la Mulungu chifukwa cha kuwawa na zilonda, koma anakana kulapa zoipa zomwe anali kuchita.
12
Mngelo wa nambala 6 anathira mbale yake mu msinje waukulu wa Euphrates. Manzi yake yanauma kupanga njira ya mamfumu yamene yanachokera ku m'mawa.
13
Ninaona mizimu yoipa yomwe yanaoneka monga achule kutuluka mkamwa mwa chinjoka, mwa chilombo na mwa mneneri wa boza.
14
Chifukwa ni mizimu ya ziwanda kuchita milakuli ni zizindikiro. Anali kupita kwa mamfumu a ziko lonse kuwasonkhanisa pamozi kukonzekera nkhondo pa siku lalikulu la ambuye amphamvu zonse.
15
("Onani! Ine nibwela monga kawala! Odalisika ni uja wamene apitiliza kuona, ankala ovala vovala vake kuti asaka ende chintako kuti bantu bamuone mwamene aonekela mochitisa nsoni.")
16
Banaba leta pamozi pamalo yoitaniwa kuti Amagedoni muchitundu cha Aheberi.
171819
Pamene apo mungelo wa namba seveni anatila mumwamba vinali mu mbale yake. M'mpando wachifumu wamene unali munyumba yoyela munachoka mau yokamba kuti, "Chasilizika!" Kunali kungwelebela kwa kaleza, kuundumuka,
20
Ma ziko yonse ya pa manzi yana soba, na malupili siyana pezeke.
21
Vimyala vikulu, volema kulingana na talent imozi, vinagwa kuchoka kumwamba kugwa pali bantu. Bantu bana nyoza Mulungu chifukwa cha kugwa kwa myala koma futi chifukwa chakuti kugwa kwa myala kunali ko vutisa kwambili.